Mlembi wamkulu mu ofesi yoona za madyedwe ndi matenda a Edzi Mai Edith Mkawa ati ndiwokhudzidwa ndi kufala kwa kachilombo ka matenda oyambitsa Edzi ka HIV ngakhale Boma likuyesetsa kupeza njira zopewera kufala kwa matendawa.
M’dziko muno anthu 1 sauzande akumatenga matendawa pa sabata.
Mai Mkawa anena izi pa mwambo wokumbukira matenda a Edzi omwe unakozedwa ndi nthambi yoona za madyedwe komanso matenda a Edzi mu mzinda wa Lilongwe.
Iwo ati chiwerengero cha anthu otenga matendawa chikukwera sabata iliyonse zomwe zikubwezera mbuyo ntchito yolimbana ndi kufala kwa matendawa.
“Ngakhale mauthenga onena zakuopsa kwa matendawa akufalitsidwa, anthu sakusintha makhalidwe awo komanso ambiri akusankha kukhala m’chimbulimbuli posakayezetsa magazi awo kuti adziwe mmene mthupi mwawo muliri zomwe zikuchititsa kuti nthendayi idzifala chomwechi,”watero Mkawa.
Iwo ati kuti boma lingakwanitse kuthetsa kufala kwa kachilomboka komanso imfa zomwe zimadza kamba ka matendawa komanso kusalana ngati anthufe titachitapo kanthu.
“Kuyambira chaka cha 2011 mpaka 2015 mitu ya masiku okumbukira matenda a Edzi ikuunika
njira zothetsera matendawa ndipo tiyeni a Malawi tiyesetse kuthandiza kuchepetsa kufala kwa matendawa”, watero mlembiyu.
Iwo alangiza onse amene ali ndi matendawa kuti azidziteteza komanso kumwa mankhwala otalikitsa moyo.
“ Ndikulangiza onse amene anapezeka ndi kachilomboka kuti ayambe kulandira thandizo nsanga komanso kutsatira malangizo akuchipatala,” watero Mkawo.
Mkulu woona za ndondomeko ku bungwe la National AIDS Commission (NAC) Mai Mirriam Mangochi ati anthu ambiri akumalephera kukayezetsa kuti adziwe mmene thupi mwawo muliri kamba koopa kusalidwa komanso kukaima pamzere kuchipatala.
“Anthu akusankha kusadziwa mmene mthupi mwawo muliri kamba koopa kuti anthu awaona akaima pa mzere kuchipatala kuti alandire chithandizo.
Bungwe loona zaumoyo padziko lonse lapansi linaika pa 1 December kuti maiko,mabungwe komanso madera adzikumbukira komanso kuganizira mmene angathetsere matenda a Edzi,