Bwalo loyamba lamilandu m’boma la Ntchisi lalamula mamuna wina wa zaka 27 zakubadwa kuti akakhale kundende kwa miyezi makumi atatu, atapezeka olakwa pa mlandu opanga kalata za chinyengo ndi cholinga chofuna kubera anthu.
Bwalolo lachiwiri sabata ino, linamva zoti mwamunayo, pa 27 mwezi wa October chaka chatha, ananamiza a Lameck Gaweni a m’bomalo pofuna kuwabera katundu komanso a Alick Soko pofuna kuwabera ndalama mu dzina la wapolisi pogwiritsa ntchito kalatazo, zomwe ati ndi kulakwira gawo 364 la malamulo oweluzira milandu m’dziko muno.
Malinga ndi m’neneri wa apolisi m’bomalo Sergeant Gladson M’bumpha ngakhale kuti mamunayo anavomera mulanduwu, komabe bwalolo lapereka chilango chokhwima ati pofuna kuti anthu ena omwe ali ndi maganizo otere atengerepo phunziro.
Iye ndi wa m’mudzi mwa Chimanda m’dera la mfumu yayikulu Nthondo m’boma lomwelo la Ntchisi.