Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wati abambo ali ndi udindo wawukulu pa miyoyo ya ana awo m’banja.
Papa, amalankhula izi dzulo pa mwambo wa mapemphero womwe amakhala nawo lachitatu lililonse ndi akhristu ozungulira ku likulu la mpingowu komanso alendo omwe afika kulikululo.
Papa wati abambo akakhala kuti akutanganidwa ndi ntchito zawo nthawi zambiri sakhala ndi mpata wokhala ndi ana awo,zomwe zimapangitsa kuti ana adzikula ngati opanda makolo awo pa banja.
Iye wati abambo ali ndi udindo waukulu owonetsetsa kuti akupereka chitsanzo chabwino kwa ana awo pofuna kuti adzikula ndi makhalidwe abwino komanso aluntha.