Khonsolo ya boma la Machinga,yayamikira bungwe lowona za chitukuko mu mpingo wakatolika la Cadecom mu Dayosizi ya Zomba, kamba ka thandizo lomwe bungweli likupereka kwa anthu omwe akhudzidwa ndi mvula yamphamvu.
Bwanamkubwa wa bomalo Mayi Reighard Chavula,ndi yemwe wayamikira bungweli pomwenso akulikulu la bungweli anakawona momwe bungweli likugwilira ntchito zake mudayosiziyo.
Mayi Chavula ati poyang’anira kuchuluka kwa maboma omwe akhudzidwa ndi ngozi ya madzi mdziko muno, mpovuta kuti boma palokha likwanitse kupereka thandizo kwa anthu onse omwe akhudzidwa ndi ngoziyi ,ndipo ati thandizo lomwe bungwe la Cadecom likupereka ,lafika mu nthawi yake pamene anthu asowa thandizo mwachangu.