Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Dayosizi ya Zomba Ikufufuza Njira Zofuna Kupeza Thandizo Lokwanira Lothandizira Anthu Okhudzidwa ndi

$
0
0

Pofuna kupeza thandizo lokwanira lopita kwa anthu omwe akhudzidwa ndi madzi osefukira potsatira pempho la maepiskopi a mpingo wakatolika mdziko muno,dayosizi ya Zomba ya mpingowu, yati ikufufuza njira zabwino zomwe zingathandize kuti thandizoli lidzapezeke lokwanira kuchokera kwa akhristu ake.

Kalata yomwe maepiskopi mdziko muno alemba,yapempha kuti zopereka zomwe akhristu mumpingowu adzapereke lamulungu pa 8 mwezi uno,zidzapite kunyumba kwa a Episkopi mmadayosizi onse, komwe zidzapezeredwe tsiku lokazipereka kwa anthu okhudzidwa ndi vutoli.

Polankhula ndi Radio Maria Malawi,mkulu ofalitsa nkhani za dayosiziyi Bambo Steven Likhutcha,ati pakadali pano zokambirana zofuna kupeza njira zabwino zomwe dayosiziyi ingatsate pofuna kupeza thandizo lokwanira potsatira pempholi,zikupitilira.

‘Pali ganizo loti mwambo otolera thandizoli udzachitike lamulungu pa 15 February, pofuna kuti akhristu mu dayosiziyi, akonzekere bwino,’anatero Bambo Likhucha.

Pamenepa iwo apempha akhristu a dayosiziyi kuti asayang’anire nkhani ya ndalama yokha komanso aganizirepo pa zokolora zosiyanasiyana zimene zingathandize anthu okhudzidwawa.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>