Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Akristu a ku Middle East Ali Pamavuto Aakulu.

$
0
0

Mpingo wa Katolika mdziko la Greece wati akhristu a mmayiko a ku  Middle East, atha zaka zisanu tsopano ali pamavuto aakulu kaamba ka nkhondo yomwe ili mmayikowo.

Bishop Gregory Laham,ndi yemwe wanena izi muuthenga wake wanyengo yamasautso a Yesu Khristu,ndipo wati moyo omwe anthu a mmayikowo maka akhristu akukhala,ndichimodzimodzi njira ya mtanda.

Iye wati anthuwo, akukhala moyo ovutikitsitsa mumbiri ya padziko lonse,pena, kuposanso mavuto omwe anthu adakumana nawo panthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse.

Iye anatchulapo mayiko a Lebanon,Syria ndi Iraq kuti ndi momwe vutoli lafika poipa kwambiri padziko lonse.

Bishop Laham wati pakadali pano mdziko la Lebanon, lomwenso ndi laling’ono kwambiri,muli anthu 1.5 miliyoni omwe athawa nyumba zawo kamba ka nkhondo, zomwenso zikudzetsa mavuto aakulu pachitukuko cha dzikolo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>