Mtsogoleri wa mpingo wa Katolika pa dziko lonse Papa Francisco usiku wa pa 11 mwezi uno, adzachititsa mwambo wokhazikitsa chaka cha Chifundo cha Mulungu chomwe chidzayambe mwezi wa December chaka chino.
Malinga ndi malipoti a Vatican pa mwambowu Papa adzafotokozera zolinga za chakachi komanso zomwe iye wakonza kuti adzachite pa nthawiyi.
Papa anafotokoza za chakachi pa 13 mwezi watha ku tchalitchi la St Peters Basilica, kuti chakachi chidzayamba pa 8 mmwezi wa December lomwenso ndi tsiku lokumbukira Maria Wosayipa Konse, ndipo chidzatsekeledwa mwezi wa November chaka cha mawa tsiku la chaka cha Yesu Khrsistu Mfumu.