Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

NZIKA ZILI NDI UDINDO PA ZISANKHO ZA 2014-MEC

$
0
0

Bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC), lati nzika za m’dziko lino zikuyenera kuonetsa udindo wawo potenga mbali pazisankho zachaka cha mawa polembetsa m’nkaundula wa mavoti.

Wapampando wa bugweli mdziko muno a Justice Maxon Mbendera  ndiye wanena izi mu mzinda wa Lilongwe pamene amalankhula  ndi Radio Maria Malawi.

Justice Mbendera wati ntchito yolembetsa mkaundula wa zisankho ikuyembekezeka kuyamba pa 22 mwezi wa  July chaka chino mpaka pa 4January chaka  cha  mawa.

“Aliyense    akuyenera   kulembetsanso kuti alandire chitupa chatsopano kamba koti zimphanso zakale zisidzagwiranso ntchito”  watero Justice Mbendera.

Ntchitoyi igwiridwa m’magawo khumi kwa masiku 14 m’gawo
lililonse.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>