Malo 178 a mpingo wa Katolika mdziko la France kuphatikizapo matchalitchi, akuyembekezeka kutetezedwa ndi apolisi zitadziwika kuti gulu lazauchifwamba la mdziko la Syria limakonza zochita zamtopola pamatchalitchi awiri a mpingowu mumzinda wa Paris.
Nduna yayikulu ya dzikolo a Manuel Valls, yatsimikizira mpingowu kuti boma,liwonetsetsa kuti malowo ali ndi chitetezo chokwanira.
Malipoti a CNN ati chiwembucho chadziwika mnyamata wazaka 24 wa mdziko la Algeria, yemwe amachita maphunziro aukachenjede , atapha mayi wina.
Atachita chiwembucho, mnyamatayo akuti anauza apolisi zankhaniyi pomwe amadziwonetsa ngati iye analinso munthu yemwe amafuna kuchitiridwa chiwembu.
Apolisi atafufuza nkhaniyi, apeza kuti mnyamatayo, ndi yemwe wachita chiwembucho molumikizana ndi zigawenga za mdziko la Syria, pamene zimakonzekera kuwononga mmatchalitchiwo.