Mtsogoleri wa dziko lino Proffessor Arthur Peter Mutharika walonjeza amalawi kuti palibe amene akumane ndi vuto la kusowa kwa chakudya chaka chino.
Mtsogoleriyu walankhula izi lachiwiri pa msonkhano wa atolankhani mu mzinda wa Lilongwe.
Iye wati pali mgwirizano wabwino pakati pa dziko lino ndi nthambi ya bungwe la United Nations yowona za chakudya ya World Food Programme WFP lothandiza dzikoli.
Malinga ndi unduna wa zamalimidwe, dziko lino silikhala pa chiwopsezo chachikulu ku mbali ya chakudya kamba koti pakhazikitsidwa njira zosiyasiyana zothana ndi vutoli kuphatikizapo ulimi wa mthilira.