Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Francisco Wayamikira Mgwirizano wa Pakati pa Zipembedzo

$
0
0

Mtsogoleri wampingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco wayamikira mgwirizano omwe ulipo pakati pa zipembedzo padziko lonse.

Papa Francisco,amalankhula izi lachinayi pa msonkhano wa akuluakulu a mpingowu komanso a mipingo ndi zipembedzo zina a mmayiko akuulaya,omwe unachitikira ku likulu la mpingowu ku Vatican.

Polankhulapo mtsogoleri wa mpingo wakatolikayu wapempha  mabungwe osiyanasiyanasiya a mipingo ndi zipembedzo omwe adapanga umodzi, kuti adzigwira ntchito zawo motsogozedwa ndi chikhulupiliro chawo mwa Mulungu mmodzi pogwiritsa ntchito malembo oyera.

Popitiliza kulankhula kwa nthumwi zomwe zinafika kumsonkhanowo, Papa Francisco wadzudzula khalidwe la atsogoleri a mipingo ndi zipembedzo, omwe amadziwonetsa kwa anthu kuti akugwira ntchito zolimbikitsa umodzi koma akupanga zina, zomwenso zikuchititsa kuti anthu ena adzilephera kupemphera mwaufulu pa zikhulupiliro zawo.

Pomaliza, mtsogoleri wampingo wakatolikayu wapempha magulu osiyanasiyana kuti adzipereke pa ntchito yolimbana ndi mavuto omwe akuchititsa kuti anthu azithawa mayiko awo chifukwa cha kusowa kwa ufulu wachipembedzo,umphawi,nkhondo ndinso mavuto ena.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>