Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mabungwe a Mpingo Wakatolika Ogwila Ntchito za Chifundo Ayamba Msonkhano Wawo Lachiwiri

$
0
0

Mabungwe 164 a mpingo wakatolika omwe amagwira ntchito zachifundo padziko lonse omwe adabwera pamodzi ndikupanga bungwe la Caritas International, lachiwiri ayamba msonkhano wawo wa pachaka pofuna kupeza njira zomwe zingathandize kuchepetsa umphawi pakati pa anthu kwazaka zinayi zikudzazi.

Kumsonkhanowu,omwe uchitikire mumzinda wa Rome mdziko la Italy, kukuyembekezeka kufika nthumwi mazana atatu zoyimilira mabungwewa kuchokera mmayiko osiyanasiyana.

Msonkhanowu uchitika kuyambira pa 12 mpaka pa 17 mwezi uno motsogoleredwa ndi mutu oti “Banja Limodzi, Kusamalira Zachilengedwe.”

Polankhula ndi wayilesi ya mpingo wakatolika kulikulu la mpingowu kuti Vatican, mtsogoleri wa bungwe la Caritas International Cardinal Oscar Rodrick Maradiaga yemwenso akuyembekezeka kupuma paudindowu atakhalapo kwazaka zisanu ndi zitatu, wati mtsogoleri wampingowu padziko lonse Papa Francisco walimbikitsa nthumwi zomwe zikhale nawo pamsonkhanowu, kuti ziwunikire mozama mavuto omwe akudzetsa umphawi pakati pa anthu komanso kupeza njira zabwino zothana ndi mavutowa.

Malinga ndi mlembi wamkulu wabungwe la Caritas International, kusiyana pachuma, nkhondo, kusintha kwa nyengo, njala ndi zina ndi mavuto aakulu omwe bungweli likukumana nawo pantchito yake padziko lonse.

Kumsonkhanowo kukuyembekezeka kufika nthumwi makumi asanu zoyimilira achinyamata, anthu  ogwira ntchito modzipereka komanso nthumwi za mmabungwe omwe amagwira ntchito zolimbana ndi vuto la njala mmayiko osiyanasiyana.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>