Mtsogoleri wa mpingo wa katolika padziko lonse Papa Francisco wasankha Olemekezeka Ambuye Thomas Luke Msusa,omwe ndi arkepiskopi wa arkdayosizi ya Blantyre kukhala woyendetsa dayosizi ya Zomba ngati Apostolic Administrator, mpaka pomwe episkopi watsopano wa dayosiziyi adzasakhidwe.
Malinga ndi chikalata chomwe likulu la mpingowu latulutsa kudzera mwa kazembe wa mpingowu kuno ku Malawi ndi Zambia wolemekezeka Archbishop Julio Murat ,Papa Francisco wasankha Ambuye Msusa kuti aziyang’aniranso dayosiziyi potsatira imfa ya Monsignor Henry Kaleso omwe akhala akuyendetsa dayosiziyi.
Kudzera mchikalatachi, Olemekezeka Ambuye Murat apemphanso anthu kuti alumikizane nawo popemphelera dayosiziyi komanso Arc Episkopi Thomas Luke Msusa amene avomera udindo woyendetsa dayosizi ya Zomba poyembekezera episkopi watsopano.