Makadinala a Mpingo wa Katolika akupitiliza mwambo osankha Papa watsopano atalephera kupeza yemwe wapambana pachisankho chawo pa 12 March 2013.
Makadinala 115 ndiomwe akusankha Papa yemwe alowe m’malo mwa Papa opuma Benedikito wachi 16.
Makadinalawo ali pa m’bindikiro mpaka apeze kadinala m'modzi, yemwe akhale mtsogoleri wa Mpingowu kudzera mu voti yawo ya chinsinsi.
Kunali mfuwu kuchokera kwa anthu mazanamazana omwe anasonkhana kubwalo la St.Peters Square ku likulu la mpingowu pomwe utsi wakuda unatuluka kusonyeza kuti panalibe kadinala yemwe anasankhidwa pa voti yoyambayo.
Malipoti ati pakadali pano palibe Kadinala yemwe akusonyeza kuti ndi yemwe asankhidwe pa udindowu.
Makadinalawo akuti adzivota kanayi tsiku lililonse mpaka Papa watsopanoyo adzasankhidwe.