Mpingo wakatolika mdziko la Nigeria wati siwukugwirizana ndi ganizo loti amayi omwe adapatsidwa pathupi ndi mamembala a gulu la zigawenga za Boko Haram atagwidwa ukapolo,achotsedwe pathupipo.
Mkulu owona za umoyo mumpingowu m’dzikolo Bishop Anselm Umoren, ndi yemwe wanena izi polankhula ndi kampani yosindikiza nkhani ya Fides.
Iye wati sikoyenera kuthandiza amayiwo kuchotsa pathupipo ndipo alonjeza kuti mpingowu mogwirizana ndi anthu akufuna kwabwino mdzikolo ndi wokonzeka kuthandiza amaiwo mwanjira zina.
Malipoti akusonyeza kuti amayi ndi asungwana omwe adagwidwa ukapolo ndi zigawengazo akhala akusungidwa ndi mamembala azigawengazo,ndipo ambiri mwa iwo tsopano ndi woyembekezera.
Mpingowu wati ana amene akuyembekezeka kubadwa mwa amayiwo pawokha ndi wosalakwa ndipo chomwe chikufunika ndi kuthandiza amayiwo pa zosowa zawo.