Bungwe la Aphunzitsi a Mpingo wa Katolika ozungulira Parish ya Mayaka mu Dayosizi ya Zomba aliyamikira kamba kozipereka pa ntchito zachifundo.
Wothandizira Bambo Mfumu a pa Parishiyi Bambo James Chaweza ndi womwe anena izi pamene bungweli limakachezera odwala pa Chipatala chaching'ono cha Mayaka m'boma la Zomba.
Bambo Chaweza ,womwenso anatsogolera Nsembe ya Ukaristia pa mwambowu, anati odwala amasowa zinthu zambiri ndipo zomwe achita aphunzitsiwa, zichepetsa ena mwa mavuto omwe odwala pa chipatalachi amakumana nawo.
Iwo anayamikiranso chitsanzo chomwe aphunzitsiwa awonetsa ndipo apempha anthu ndi mabungwe ena akufuna kwabwino kuti atengere chitsanzo chabwinochi.
Mkulu woyang'anira Chipatala cha Mayaka Sister Emma Nazombe anati katundu yemwe bungwe la aphunzitsiwa lapereka athandiza pa ntchito zosiyanasiyana za pa Chipatalachi. Wina mwa katundu yemwe aphunzitsiwa apereka ndi shuga, sopo ndi zidebe za plastic.