Gulu lomwe lili paulendo wopita ku Yerusalemu lochokela mu Arch-Diocese ya Lilongwe lapempha Akhristu m`dziko muno kuti akuyenera kumatenga nawo gawo pamaulendo osiyanasiyana makamaka okapemphera kumalo oyera ndi cholinga chofuna kuzamitsa chikhristu chawo.
Mlembi wagululi mayi Claire Chikaya aku Likuni Parish ananena izi poyankhulana ndi Radio Maria.
Mayi Chiyaka anati maulendo ngati awa amathandiza kuzamitsa chikhulupirilo pamoyo wauzimu. Pakadali pano mapemphelo anovena okonzekera ulendowu akuchitika ndipo atsirizidwa pa 16 June ku St Patricks parish.
Iwo anatinso akhristu a mu Arch-Dioecese-yi anakatsazikana ndi Episcope Ambuye Ziyaye, ndipo awapempha kuti akapempherere dziko lawo, ma banja awo, mimphakati komanso Diocese yawo.
Yemwe wakhala akupita ku malo oyera osiyanasiyana a Andrew Makupete anayamikira Bambo Josephy Kimu kaamba kokonza maulendowa pakati pawo mdziko muno. Akhristu womwe akupita ku yerusalemu chaka chino alipo 47 ndipo akuyembekezeka kunyamuka pa 17 mwezi uno.