Mtsogoleri wa mpingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco wapempha atsogoleri a mayiko a Israel ndi Palestine kuti athetse kusamvana komwe kwakhala kukuchitika pakati pa mayiko awiriwa.
Kusamvana komwe kwayambiranso masiku apitawa pamene anthu awiri anakachita za chiwembu pa tchalitchi lina mdziko la Israel ndipo anapha anthu asanu ndi kuvulaza ena khumi ndi atatu akuti kwasokoneza bata ndi mtendere zomwe zinalipo mu mzinda wa Yerusalemu ndinso mizinda ina yomwe ili kufupi ndi mzindawu.
Papa Francisco wati mayiko awiriwa akuyenera kuwonetsetsa kuti mzinda wa Yerusalemu ukutetezedwa mokwanira kamba koti ndi mzinda opatulika mu mbiri ya chikhristu.