Ubale wabwino pakati pa makwaya ati ndi njira imodzi yopititsira patsogolo moyo wauzimu pakati pa akhristu mu mpingo.
Mayi Bibiana Jimu omwe ndi wapampando wa Kwaya ya amayi ya St Agness ku parishi ya Bvumbwe mu Arkidayosizi ya Blantyre ndi omwe alankhula izi pomwe kwaya yawo inayitanitsa kwaya ya St Michaels Nansangwa kuti adzachezerane ndi kugawana luso la mayimbidwe.
Mayi Jimu ati ubale pakati pa makwaya a amayi ungathandize amayi kuzama pa uzimu komanso kukulitsa chikhulupiliro chawo mwa Mulungu.
Iwo ati kwayayi ndi chifukwa chake inaitana anzawowa kuti agawane nawo luso komanso kuthandizana pa momwe angapititsire patsolo moyo wawo wa uzimu pomwe akutumikira Mulungu kudzera m'mayimbidwe.