Bungwe la Total Land Care lati ndi cholinga cha bungweli kuwonetsetsa kuti likulimbikitsa ukhondo komanso kuteteza chilengedwe msukulu za pulayimale m’dziko muno.
Mkulu wa bungweli a Jeliam Chiputu ndi yemwe walankhula izi m’boma la Mchinji pomwe limapereka mphatso kwa sukulu zomwe zachita bwino ku mbali ya ukhondo m’bomalo.
Iwo ati bungwe lawo lapeleka mphotozo pofuna kulimbikitsa sukulu zina ukhondo ndi ntchito yosamalira ndi kuteteza zachilengedwe.
Polankhulanso pa mwambowo mlangizi wa zamaphunziro m’bomalo Agnes Zondolo yemwe anali mlendo wolemekezeka pa mwambowo walangiza sukulu zomwe zalandira mphotozo kuti zipitilize kudzipereka pogwira ntchitozi.
Sukulu zomwe zachita bwino ndikulandira nawo mphotozo ndi monga za Ndaula, Chazuka ndi Mpachila za kwa mfumu yayikulu Mavwele m’boma lomwelo la Mchinji ndipo zalandira mphatso monga mipira , zolembera ndi motayira zinyalala.