Bomba la timke nawo lapha anthu 14 pa msika wina m’dziko la Chad.
Munthu yemwe akumuganizira kuti wachita izi ati anavala ngati munthu wa mayi kenaka ndi kulowa mu msika wina komwe anakaphulitsa bombalo iye ndi kuferanso pamalo omwewo.
Mwa anthu 14 omwe afa ndi bombalo asanu ndi anayi ndi amayi.
Gulu la zigawenga za Boko Haram ndi zomwe akuziganizira kuti zinakonza chiwembucho.
Malingana ndi atolankhani a Nyuzi 24 , dziko la Chad ndi limodzi mwa mayiko omwe anachita mgwirizano ndi dziko la Nigeria pofuna kulimbana ndi gulu la zigawengazi.