Anthu khumi ndi atatu afa ndipo ena makumi anayi avulala anthu ena ataphulitsa bomba pahotela ina mumzinda wa Mogadishu mdziko la Somalia.
Mtolankhani wa wailesi ya BBC mumzindawo wati chiwembucho ndi chimodzi mwa ziwembu zikuluzikulu zomwe wakhala akuwona mdzikolo.
Gulu lazauchifwamba la Ishabaab lalengeza kuti ilo ndi lomwe lachita chiwembucho.
Ilo lachita zaupanduzo mtsogoleri wadziko la America Barrack Obama,atangomaliza zokambirana ndi mtsogoleri wa dziko la Kenya za mmene angathanire ndi ziwembu zomwe gululo likuchita mmaiko osiyanasiyana.
Pakadali pano dziko la America ladzudzula zamtopola zomwe gululo lachita.