Mtsogoleri wampingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco wabwerezanso kupempha maiko padziko lonse kuti achitepo kanthu polimbana ndi nkhanza zomwe akhiristu ndi magulu ena azipembedzo zing’onozing’ono akukumana nazo m’maiko ena.
Kudzera mkalata yomwe Papa Francisco walembera Episikopi othandizira mu Dayosizi ya Yerusalemu, mtsogoleri wampingo wakatolikayu wati akupitiliza kupemphelera anthu a mdziko la Iraq omwe akukhala M’dziko la Jordan pothawa ziwembu zomwe magulu a zauchifwamba akumawachitira M’dzikolo.
Iye wati anthuwa akhonza kutchulidwa kuti ndi amalitiri a lero chifukwa cholimba pachikhulupiliro chawo.
Mtsogoleri wampingo wakatolikayu wanena izi pamene mlembi wamkulu wa bungwe la ma Episikopi M’dziko la Italy Arkibishopu Nunzio Galatino ali mdziko la Jordan komwe mwa zina akuyembekezeka kuyendera anthu a dziko la Iraq-lo omwe akukhala m’misasa M’dziko la Jordan-lo.