Unduna owona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa akazi ndi amuna, ana ndi chisamaliro cha anthu olumala wapempha anthu omwe ali ndi abale omwe ali ndi zilema zosiyanasiyana kuti apite kumaofesi a mundunawu kuti akathandizidwe pandondomeko yopereka maphunziro a luso losiyanasiyana kwa anthuwa.
Nduna yowona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa akazi ndi amuna, ana ndi chisamaliro cha anthu olumala Mayi Patricia Kaliati ndi omwe apereka pempholi polankhula ndi Radio Maria Malawi mumzinda wa Lilongwe.
Mayi Kaliati ati boma layika ndondomeko zosiyanasiyana zomwe likhale likugwiritsa ntchito mpaka mtsogolomu pofuna kuthandiza anthuwa kuti azikhala moyo odzidalira.
Pakadali pano undunawu wati ukupereka mpata oti anthu omwe ali ndi zilema zosiyanasiyana alembere chomwe angathe kuphunzira kuundunawu pasanafike pa 20 mwezi uno, kuti apatsidwe mwayi wamaphunziro pantchito yomwe akufuna.