Bungwe la mgwirizano wa mayiko la United Nations UN lati liwulula mayiko omwe akulephera kupereka zilango kwa asilikali awo omwe akukhudzidwa ndi mchitidwe ozunza anthu osalakwa mmayiko omwe bungweli lidatumiza asilikaliwa kuti akhazikitse bata.
Mlembi wamkulu wa bungweli a Ban Ki-moon ndi yemwe wanena izi lachinayi pamsonkhano omwe anali nawo ndi akuluakulu a munthambi yowona zachitetezo kubungweli ya Security Council.
A Moon anena izi pambuyo pochotsa paudindo mkulu wa asilikakali a bungweli mdziko la Central African Republic, chifukwa cha kuchuluka kwa malipoti okhudza mchitidwewu pakati pa asilikali a bungweli omwe akugwilira ntchito yawo mdzikolo.
Mayiko osiyanasiyana omwe ndi mamembala a bungwe la United Nations amatumiza asilikali awo kubungweli kuti akhazikitse bata mmayiko momwe muli nkhondo koma malipoti akusonyeza kuti ena mwa asilikaliwa amachitira anthu nkhanza zosiyanasiyana kuphatikizapo kugwililira.
Iwo ati mu lipoti lawo lapachaka lomwe akuyembekezeka kutulutsa awulula komanso kuchititsa manyazi mayiko omwe akulephera udindo wawo pankhaniyi.
Malinga ndi malamulo a bungwe la United Nations dziko limene litumiza asilikali ake kubungweli kuti akathandize kukhazikitsa bata ndipo amayenera kukhala ndi udindo ofufuza ndi kupereka zilango kwa asilikali awo omwe akukhudzidwa ndi milandu ya mtunduwu.