M’bindikiro wa masiku asanu ndi atatu wa asisiteri a chipani cha Presentation for the Blessed Mary mu dayosizi ya Dedza watha lamulungu mudayosiziyo.
↧
M’bindikiro wa masiku asanu ndi atatu wa asisiteri a chipani cha Presentation for the Blessed Mary mu dayosizi ya Dedza watha lamulungu mudayosiziyo.
M’bindikirowu omwe unachitika ndi mutu oti Mayi Maria Chitsanzo Cha Atumiki A Mulungu unachitika potsatira pempho la mtsogoleri wampingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco loti chaka chino chikhale chaka cha utumiki.
Polankhula ndi Radio Maria Malawi potsekera m’bindikorowu omwe anatsogolera ndi Bambo Joseph Kimu omwenso ndi mkulu owona za mapulogalamu ku Radio Radio Maria Malawi m’modzi mwa asisiteri omwe anali nawo pa m’bindikirowu Sister Martha Mwaluka ati m’bindikirowu apindula nawo kwambiri pamene alimbikitsika muutumiki wawo.
Iwo ati aphunzira kufunika kokhala odzichepetsa pautumiki wawo,monga mayi Maria ngati mtumiki oyambilira adawonetsa pofuna kutumikira Mulungu.