↧
Bungwe la United Nations (UN) lawopseza kuti lichitapo kanthu ngati mtsogoleri wa dziko la South Sudan a Salva Kiir sasayina pangano la mtendere ndi magulu omwe akuwukira dzikolo.
Pa msonkhano wa atolankhani omwe nthambi ya zachitetezo ku bungwelilinachititsa, m`modzi mwa akuluakulu a bungweli a Stephen O`Brien ati padakali pano, zinthu sizili bwino ku South Sudanndipo mwazina anthu akumaotchedwa m`nyumba zawo.
Pulezidenti Kiir amayenera kuti asayine pangano la mtendere ndi cholinga choti athetse kusamvana pakati pa boma lake ndi gulu lowukira lomwe likutsogoleredwa ndi a Riek Machar omwe anasayinira kale panganoli.
Padakali pano anthu zikwizikwi aphedwa kale pankhondoyi ndipo ena opososa 2.2 million anathawa m`nyumba zawo.