Nduna yayikulu ya dziko la Iraq yakhazikitsa komiti yomwe izigwira ntchito yoteteza akhristu komanso madera ena omwe amayang’aniridwa ndi boma m’dzikolo.
Ndunayi yakhazikitsa komitiyi potsatira pempho la mtsogoleri wa maepiskopi mdzikolo Patriarch Louis Raphael Sako yemwe wapempha boma kuti liteteze akhristuwa omwe akukumana ndi nkhanza zosiyanasiyana kuchokera ku magulu a ziwembu.