Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Ambuye Stima at Akhristu Akuyenera Kulemekeza Tsiku la Utumiki wa Ana

$
0
0

Episkopi wa Diocese ya Mangochi Ambuye Montfort Stima,ati akhristu a mpingo wakatolika mdziko muno akuyenera kulemekeza tsiku la chaka cha Epifania , lomwe mpingo wakatolika unaliyika mwapadera kuti likhale la utumiki wa ana.

Ambuye Stima anena izi loweruka polankhula ndi mtolankhani wathu.

Iwo anena izi pamene dayosizi ya Mangochi  ndi madayosizi ena, akuchita miyambo ya misa yotsogoleredwa ndi ana pofuna kutumikira ana anzawo ngati njira imodzi yokometsera chakachi.

“Ana akamalangizana okhaokha amatha kumva kusiyana ndi munthu wamkulu chifukwa amagawana malangizo othandiza umoyo wawo wa tsiku ndi tsiku komanso tsogolo labwino,”anatero Ambuye Stima.

Ambuye Stima ayamikira mpingo komanso Radio Maria Malawi kamba kotengapo gawo polimbikitsa ana pa utumiki umenewu.

Iwo afunira ana mafuno abwino pa tsikuli ndipo kuti athe kupereka mauthenga osiyanasiyana kwa ana anzawo komanso polalika uthenga wabwino ndi chimwemwe.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>