Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Francisco Wapempha Akhristu kuti Akhale Okonda Kuchita Ntchito za Chifundo

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapempha akhristu, kuti aziwonetsa chikhulupiliro chawo, pothandiza anthu ovutika komanso odwala matenda osiyanasiyana.

Papa Francisco, wanena izi mchikalata cha nambala 23 chomwe watulutsa, pokonzekera tsiku  loganizira anthu odwala padziko lonse, lomwe limachitika pa 11 February chaka chilichonse.

Muuthenga wake, Papa wapempha anthu okhulupirira Mulungu kuti akhale maso a anthu omwe ali ndi vuto losawona ndinso phazi kwa anthu osayenda.

Pamenepa,Iye wati akhristu akuyenera kukhala pafupi ndi anthu odwala, powawonetsa chikondi kudzera muthandizo losiyanasiyana lomwe akusowa pamene iwo akulephera kudzichitira okha zofuna zawo.

Kwa anthu odwala, mtsogoleri wampingo wakatolikayu wati ngakhale kuli kovuta kumvetsetsa kufunika kokhala moyo pamene munthu ukumva kuwawa,mpofunika kukhala ndichiyembekezo pazazikulu za Mulungu pamoyo wa munthu.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>