Bwalo lalikulu lamilandu mdziko la Kenya lakana kuwonjezera malipiro a aphunzitsi a mdzikolo ndi ma peresenti 60 monga momwe bwalo la milandu lowona za kagwiridwe komanso kalembedwe ka ntchito linagamulira.
Bwaloli lati bwalo la milandu lowona za kagwiridwe komanso kalembedwe ka ntchito linalibe mphamvu zopereka chigamulo pa mlanduwu.
Malipoti a wailesi ya BBC ati koyambilira kwa chaka chino aphunzitsi mdzikolo ananyanyala ntchito kwa sabata zisanu kaamba koti boma limakana kuwakwezera malipiro.
Malinga ndi malipoti boma la dzikolo ati likhala lokondwa ndi chigamulochi kaamba koti silikanakwanitsa kuwonjezera aphunzitsiwa malipolo awo kaamba ka vuto la zachuma mdzikolo.
Padakali pano aphunzitsiwa ati akamang’ala ku bwalo lalikulu la supreme kuti litembenuze chigamulochi.