Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

A MANG'ANJA AKUMANA- CHILUKUNZAKO

$
0
0

Bungwe la anthu a mtundu wa a MANG’ANJA lati liri mkati mokonza dongosolo lofuna kukhaka ndi msonkhano waukulu wa anthu a mtundu-wu m'dziko muno. M’modzi mwa akuluakulu a bungweli m’dziko muno a PULENI CHILIKUNZAKO ndi omwe alankhula izi pa msonkhano wa bungweli mu mzinda wa Blantyre. A CHILIKUMZAKO ati mwa zina ku msonkhanowu, anthu a mtunduwu adzakambilana mfundo zina zomwe zikhale zikutsatidwa ndi cholinga chofuna kupititsa pa tsogolo chikhalidwe cha mtundu wa amang'anja chimene mbuyomu chakhala chikungoponderezedwa kamba ka zifukwa za ndale mu mthawi ya ulamuliro wa chipani chimodzi. Malingana ndi kafukufuku wina yemwe sukulu ya ukachenjede ya chancellor inachita , mtundu wa AMANG’ANJA ndi umodzi mwa mitundu yoyambilira kufika m'dziko muno mzaka za mma 100 , Ambuye Yesu asanabadwe, ndipo kufikira pano uli ndi chiwerengero cha anthu oposera 3 million.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>