Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisko wakhazikitsa Stanislaus wa Yosefe ndi Maria komanso Maria Elizabeti Hesselblad kukhala oyera.
Papa wakhazikitsa awiriwa kukhala oyera lamulungu pa mwambo wa nsembe ya misa ku likulu la mpingowu ku Vatican.
Papa anayamikira awiriwa kamba ka chikhulupiliro chomwe anali nacho komanso kupilira kwao pa nthawi yomwe anali kukumana ndi mayesero.
Iye wati kudzera mu mazunzo a yesu awiriwa anali okhudzidwa ndipo zinachititsa kuti chinsinsi cha mphamvu ya kuuka kwake chiwululike mwa iwo.
Pa mwambowu panafika nthumwi za mmaiko a Sweden ndi Poland komwe oyerawa ankachokera.