Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all 1875 articles
Browse latest View live

Kapani ya candlex yankhazikitsa makina atsopano wopangila katundu.

$
0
0

Kapani ya candlex mdziko muno yankhazikitsa makina atsopano wopangira katundu ngati njira imodzi yofuna kuti mitengo ya katundu wawo inkhale yotsika mtengo.

Mkulu woona zopanga ndikugula katundu kukapaniyi Fredric Shangaya wati ,kampaniyi yachita  izi  potengera kukula kwachiwelengelo  cha makasitomala  womwe amagwilitsa tchito   katundu wawo.

Iwo anati katundu wawo yemwe amagwilitsidwa  tchito kwambiri pa ntchito yapankhomo akuyenera kuti ankhale ndi  mtengo woti aliyense anthe kugula posatengera kupeza kwake.

“Ife ngati a Candlex timankhulupilira kuti popanda ma kasitomala sitingankhalepo ndiye tikamapanga zinthu kaya ndi Sopo kaya Mafuta chinachilichonse, kasitomala amakhala patsogolo”,anatero a Fredrick.

 Iwo anathokoza Ambuye chifukwa cha phindu limene kapani yawo ikupeza, ananthokozanso Amalawi ndipo alonjedza kuti apitiliza kuwapatsa katundu wabwino. 

 


Papa Franscico Wavomeledza Nthumwi Zamabungwe ku Msonkhano Wonkhudza Mabanja.

$
0
0

Mtsogoleri wampingo wa Katolika padziko lonse Papa Francisco wavomereza nthumwi za mmabungwe pafupifupi makumi anai a maepiskopi zomwe zikuyembekezeka kudzakhala nawo pamsonkhano wachiwiri wa maepiskopi pankhani zokhudza banja omwe uchitike mmwezi wa October chaka chino.

Papa Francisco wavomereza nthumwizi pambuyo povomezereza zina zochokera mmabungwe 75 a maepiskopi a mmaiko osiyanasiyana omwe akuyembekezekanso kutenganawo mbali pamsonkhanowu.

Ndipo Maepisikopi a mdziko la Poland ati sazagwirizana ndi kusintha kulikonse pa chiphunzitso cha mpingo pankhani yokhudza banja pamsonkhano wa maepisikopiwa.

Ofesi yofalitsa nkhani zampingowu mdzikolo yanena izi posachedwapa pambuyo pa msonkhano omwe maepikopiwa adali nawo mdzikolo pofuna kugwirizana chimodzi ngati njira imodzi yokonzekera msonkhanowu.

Maepisikopiwa ati iwo amakhutira ndi chiphunzitso chomwe mpingowu amakhulupilira pakadali pano pankhani zokhudza banja chomwenso atsogoleri akale a mpingowu monga Papa Paulo wachinayi ndi Papa Paulo wachiwiri amkalimbikitsa.

Mwambo Wansembe Ya Ukalistia Opemphelera Akhristu Opita ku Yerusalemu Wachitika Dzulo.

$
0
0

Mwambo wa Nsembe ya Ukaristia opemphelera ulendo okayendera malo oyera mdziko la Israel wachitika lachitatu ku Parish ya St Patricks mu Arkdayosizi ya Lilongwe.

 Akhristu oposa makumi anayi ndiwomwe akupita kuulendowu ndipo ena mwaiwo  ndi Ansembe anayi ndi Sisiteri mmodzi.

Akhristuwa akuyembekezeka kukayendera ndi kupemphera mmalo osiyanasiyana oyera kuphatikizapo pamanda pomwe Yesu Khristu adayikidwa ndi kuuka kwa akufa.

Akhristuwa akuyembekezeka kufika mdziko muno lachiwiri pa 23 June.

Chaka ndi chaka akhristu amapita ku Malo oyera ku Yeruselemu motsogozedwa ndi Bambo Joseph Kimu womwenso ndi mkulu woyanganila  Radio Maria Malawi mdziko muno.

Boma likuyembekezeka kukhazikitsa Bugwe loona za Bata ndi Mtenderee dziko Muno

$
0
0

Boma likuyembekezeka kukhazikitsa nthambi yapadera yowonetsetsa kuti anthu mdziko muno akupitiliza kukhala mwa bata ndi mtendere.

Mmodzi mwa akuluakulu a mabungwe omenyelera ufulu wa anthu mdziko muno Mayi Seodi White ananena izi lachinayi pamsonkhano wa masiku awiri ozindikiritsa magulu osiyanasiyana omwe amakhudzidwa pa nkhani zolimbikitsa bata ndi mtendere omwe ukuchitikira m’boma la Mangochi.

Mayi White ati boma linaganiza zokhazikitsa nthambiyi mchaka cha 2012 litawona kuwopsa kwa ziwawa zomwe zidachitika mdziko muno mchaka cha 2011 pomwe anthu makumi awiri adataya miyoyo yawo.

“Boma ndi ma bungwe womwe Sali a boma monthandizana ndi UNDP akunkhazikitsa bungwe(National Peace Archtecture) loyanganira kuti kodi patachitika mavuto ngati mpungwe mpungwe kapena kusamvana kapena patankhala kuti pali chiopsezo chokuti magulu anthu pali kusavana bungwe la dziko linkhalepo loyanganila kutipankhalebata”.

Iwo ati pakadali pano boma likupitiliza kumva maganizo a anthu mdziko muno pankhaniyi ndipo pali chiyembekezo choti mamembala oyendetsa ntchito za munthambiyi azasankhidwa ndi aphungu akunyumba ya malamulo, pofuna kuti nthambiyi izakhale yoyima payokha.

“Bungweli likhazikitsidwa ndi Constitution ya Malawi (Buku lamalamulo adziko lino) komanso likhali lonkhala bungwe la boma komanso fundo yake yeniyeni ikhala yoyanganira kuti pankhale bata, liwu lomwe limange tchito za bungweri ndi bata”

Ntchito yoyeselera kagwiridwe ka ntchito ka nthambiyi, ikuyembekezeka kukhazikitsidwa mmaboma atatu mdziko muno kuphatikizapo la Mangochi, poyang’anira mbiri ya mabomawa pankhani ya ziwawa.

Bungwe la Episcopal Conference of Malawi Liri ndi Mlembi Watsopano.

$
0
0

Mlembi watsopano wabungwe la maepiskopi mdziko muno la Episcopal conference of Malawi Bambo Henry Saindi ati apitiliza kudzipereka potumikira Mulungu pogwiritsa ntchito mphatso zomwe ali nazo pofunanso kuthandiza anthu ena kupyolera muudindo womwe asankhidwa.

Bambo Saindi anena izi lero polankhula ndi Radio Maria Malawi yomwe imafuna kumva momwe iwo awulandilira udindowu.

Iwo ati nthawi zina anthu amaganiza kuti kukhala paudindo waukulu ndi chiphinjo pa moyo wa munthu ,koma iwo ati nkhani ya udindo amaiwonera mbali ziwiri mbali yoyamba ndichinthu cholemela pamene mbali ina tintha kuwona udindo ngati mwayi umene munthu walandila ndicholinga choti atenge nawo mbali  awonese mphatso imene ali nayo ponthandidza anthu ena ponthandidza mpingo komanso mbali zina.  

“Ine poyamba ndikufuna kuthokoza Mulungu amene kupyolela Mbungwe la Episcopal Conference of Malawi wandiona kuti ndine woyenela kunkhala pa udindo umenewu”.

Iwo anapitilidza kunena kuti ngati tichita bwino ndi Mulungu amene amatinthandidza kuti tikwanilise, ndipo ndimulungu yemweyo wandiyetsa kuti ndine woyenela.

 Kalata yotsimikiza Bambo Henry Saindi kunkhala Mlembe wa bungweri yatuluka lachinayi.

MA EPISKOPI AKU AMERICA AYAMIKIRA AMECEA

$
0
0

Mpingo wa katolika mdziko la United States ndi bungwe la Catholic Relief Services[CRS] ayamikira bungwe la Association of Member Episcopal Conferences in Eastern Africa [AMECEA] kamba kodzipeleka pa ntchito zotukula miyoyo ya anthu okhala m’maiko a pansi pa bungweli.

Msonkhano wa atsogoleri a mpingo wa katolika a mmaiko a mchigawo cha AMECEA omwe ukuchitikira ku Bingu International Conference Center mumzinda wa Lilongwe unayamba pa 16 july ndipo uzatha pa 26 july 2014.

Poyankhula pomwe nthumwi za ku msonkhano wa AMECEA zimakonzekera zoyamba kuchita zokambilana zawo mumzinda wa Lilongwe, Pulezidenti wa bungwe la ma episkopi a m’dziko la United States Archbishop Joseph Tobin pamodzi ndi a Carlolyn Wool omwe ndi mkulu wa bungwe la CRS ati bungweli ladzipereka kwambiri pokweza ntchito za umoyo kuzanso maphunziro.

Bungwe la AMECEA linakhazikitsidwa mchaka cha1961 ndipo mamembala ake ndi maiko a Eritrea, Ethiopia, Kenya, Malawi, South Sudan, Sudan, Tanzania, Uganda and Zambia.

                                                                                       

 

 

 

 

 

AMECEA IYAMIKIRA MUTHARIKA POKHALA PULEZIDENTI

$
0
0

Bungwe la Association of Member Episcopal Conferences in Eastern Africa (AMECEA) layamikira Pulezidenti wa dziko la Malawi Prof Peter Mutharika chifukwa chakupambana kwake pa chisankho chomwe chinachitika mwezi wa May.

Bungwe la AMECEA lomwe likuchita msonkhano wake mumzinda wa Lilongwe lanena izi kudzera kwa wapampando wake kiepiskopi Tarcisius Ziyaye omwe ndi Akiepiskopi wa Akidayosizi ya Lilongwe pa mwambo wa misa yotsekulira msonkhano wa nambala 18 wa bungweli omwe unayamba pa 16 July ndipo uzatha pa 26 July.

"Mmalo mwa bungwe la AMECEA ndi ndiyamikire Pulezidenti wathu chifukwa chopatsidwa udindo umenewu ndi a Malawi, ife a bungwe la AMECEA tikulonjeza kukupemphererani pamene mukulamulira dziko lino," anatero Ambuye Ziyaye.

Ambuye Ziyaye anathokozanso Prof Mutharika chifukwa chokhala nawo pa mwambowo zomwe anati zinasonyeza kuti a Malawi alandira bwino alendo a mmaiko osiyanasiyana omwe afika ku msonkhanowu.

Poyankhulaponso mogwirizana ndi zomwe Ambuye Ziyaye anayankhula,wapampando wa bungwe la Episcopal Conference of Malawi Ambuye Joseph Mukasa Zuza, anati mpingo onse wa katolika ku Malawi ukuyamikira Prof Mutharika chifukwa chopambana pa chisankho cha pulezidenti chomwe chinali chokhacho choyamba chapatatu.

"Mmalo mwa mpingo wa katolika ku Malawi ndikulonjeza kuti tigwira ntchito limodzi ndi boma lanu potukula dziko lino," anayankhula motero Ambuye Zuza.

M’mawu ake Pulezidenti Mutharika anathokoza mpingo wa katolika wa ku Malawi ndinso bungwe la AMECEA chifukwa chothandiza pa chitukuko cha mmaiko omwe ali pansi pa bungweli maka m’magawo a umoyo ndi maphunziro.

"Boma langa limayamikira ntchito zomwe mpingo wa katolika ukuzigwira mmaiko akumadzulo kwa Africa ndipo ndikofunika kuti tonse tizigwirira ntchito limodzi," a Mutharika anatero.

Pulezidenti Mutharika anafuniranso mafuno abwino nthumwi za ku msonkhanowo kuti ukhale wopambana.

Ena mwa akulu akulu omwe anafika pa mwambo wotsekulira msonkhanowu anali Cardinal John Cardinal Njue amdziko la Kenya, wachiwiri kwa pulezidenti a Saulos Chilima, mtsogoleri wachipani cha Malawi Congress Dr Lazarus Chakwera komanso mtsogoleri wachipani cha People's Progressive Movement Mark Katsonga Phiri.

Bungwe la AMECEA linakhazikitsidwa mchaka cha1961 ndipo mamembala ake ndi maiko a Eritrea, Ethiopia, Kenya, Malawi, South Sudan, Sudan, Tanzania, Uganda ndi Zambia.

Bungweli lmachita misonkhano yamtunduwu zaka zitatu zilizonse ndipo uwu ndi msonkhano wachitatu kuchitikira ku Malawi.

 

 

Anthu Achiwembu Avulaza a Polisi Mdziko la Burundi.

$
0
0

Apolisi khumi ndi mmodzi avulazidwa mu mzinda wa Bujumbura mdziko la Burundi pachiwembu chomwe anthu ena anachita.

Anthuwo akuti anachita zachiwembu za mtunduwu mmalo osiyanasiyana ogwilira ntchito a polisi maka mmaboma momwe mwakhala mukuchitika ziwonetsero zosakodwa ndi ganizo lamtsogoleri wadzikolo Pierre Nkuruzinza ofuna kuyima kachitatu paudindo wawu pulezidenti.

Apolisi adzudzula magulu a zipani zotsutsa boma kuti ndi omwe akukolezera ziwembu mdzikolo.

Malinga ndi Mkonzi wankhani ku wailesi ya BBC mmaiko a mu Africa Mary Harper wati pali chiyembekezo chachikulu choti ziwembu zamtunduwu zitha kuchulukirachulukira pamene anthu mdzikolo akuyembekezeka kusankha aphungu akunyumba yamalamulo komanso pulezidenti pa chisankho chomwe chichitike mwezi wa mawa.

Magulu omenyelera ufulu wa anthu mdzikolo ati pakadali pano anthu pafupifupi makumi asanu ndi awiri aphedwa ndinso ena oposa zikwi dzana limodzi     athawa nyumba zawo.

Ndipo Zipani zotsutsa mdzikolo zati kulola pulezidenti Nkuruzinza kuti ayimenso paudindowu ndikulakwira malamulo kaamba koti walamulira kale materemu awiri.


Ma Sisiteli Apereka Zipangizo pa Chipatala Chaching’ono cha Mayaka .

$
0
0

  Asisteri achipani cha daughters of wisdom lolemba anapereka zipangizo zosiyanasiyana zothandizira pachipatala chaching’ono cha Mayaka m’boma la Zomba.

Polankhula ndi Radio Maria Malawi Sister Ireen Vito omwe anaimilira nkulu wachipanichi mdzikomuno ati cholinga chawo popereka thandizolo chinali chofuna kuthandiza anthu omwe amadalira chipatalachi chomwe chimasowa zipangizo zosiyanasiyana pantchito zaumoyo.

Nkulu oyang’anira chipatalachi Sister Emma Nazombe anati mphatso zomwe analandira ndizamtengo wapatali ndipo ziwanthandidza kupereka chinthandizo choyenelera kwa anthu amene amalandira chinthandizo pa chipatalachi.

“mwachitsazo panopa talandila otokeleti,otokeleti imeneyi itinthandiza ifeyo kugwilitsa ntchito zinthu zimene zili zomphikidwa bwino moti tilewa kupeleka matenda kuchoka kwa patient(wodwala) wina kupita kwa patient wina komanso anthu wogwira ntchito mchipatala chifukwa zinthu zimenezi zitinthandiza kuti zinthu zimenezi zizinkhala zomphikidwa bwino.”

Ndipo anawonjezera ponena kuti Makina wothandizira kupuma omwe alandira athandiza kuti anthu amene akufunika mpweya adzinthandizidwa makamaka ana womwe amabadwa ndi phuma ngankhalanso azimayi womwe amabanika kochira. Katundu yemwe asisiteriwa apereka ndi wandalama zoposa 12 miliyoni kwacha.

Vuto lakusowa kwa Chipatala Chachikulu Cha Boma Likupitilira Mboma la Phalombe.

$
0
0

Khonsolo ya boma la Phalombe yalonjeza kuti ipereka kuboma madandaulo aanthu am’bomalo omwe atopa ndi vuto lakusowa kwa chipatala chachikulu.

Akuluakulu akukhonsoloyi anena izi lolemba atalandira kalata yamadandaulo yomwe anthuwa anakapereka pambuyo paziwonetsero zabata zomwe anakonza  mogwirizana ndi nthambi ya Chilungamo ndi Mtendere mumpingo wa Katolika mu Arkidayosizi ya Blantyre.  

Ndipo Cholinga cha ziwonetserozo chinali chofuna kukumbutsa boma za mavuto a zaumoyo omwe anthu m’bomalo akukumana nawo kaamba kosowa chipatala chachikulu.

Wapampando woimilira anthu wodandaula a Kingsley Pulala anati  ali ndi chinkhulupiliro chonse kuti pulezideti Muntharika anthandiza pavutoli.

“Ndili ndi chikhulupiliro  kuti boma ili timanena kuti its alistening government( boma lova madandaulo) ndiye ndiri ndichinkhulupiliro kuti apapa atiyankha, nkhani yaikulu tikufuna kuti apulezideti alowelelepo chifukwa nkhani imeneyi yankhala akukambirana ku parliament (nyumba yamalamulo) kuyambira mma 2005.”Anatelo a Dandaula.

Poyankhulapo atalandira Kalatayo mmalo mwa Bwanakumbwa wa Bomali,   wapampando  wa zaumoyo  komanso chilengedwe a Francis Nunkhazingwe anatsimikira anthuwo kuti kalatayo ayesesa  kuti ikafika kwa   Bwanankubwa ,ndipo  kuti bwanakuyo  achite chontheka kuti kalatayo ikafike kwa purezidenti.

 

“ine ndikuwatsimikizira abale anga wokhala kuno ku Phalombe kuti petition (kalata) imene atipasa iyenela kukafika kwa puresizidenti chifukwa ndiganizaso kuti sikoyamba kupelekedwa kwazimenezi,  komabe ngati anthu okhuzidwa kuno tiwonesesa kuti a Dc (bwanakumbwa)  atumize  kalata  imeneyi kuti ikafika kwa pulezidenti,”Anatelo a Nunkhazigwe.

Iimodzi mwa bungwe lomwe linatenga nawo ngawo padziwonetselopo linala la CCJP, ndipo  kudzera mwa  nkulu woona zamaphudziro komanso ulamuliro wabwino Apatrick  Chiphwanya anati chinthu china chofunikira kwambiri chikupelewela mbomalo.

 “Ku Phalombe kuno takhala tikupanga pulojekiti yonkhudza Demokalesi, ufulu wa anthu, ufulu wachibadwidwe, ndiye kudzera mupulojekiti imeneyi anthu akuno vuto lomwe ali nalo lachipata akhala akupempha boma, mwina mwankhala mukunva ku parliament, mma news zankhala zikulembedwa komano palibe chomwe chikuchitika ndiye anachiona kuti njira yabwino ndikuwadziwitsa  aPulezideti  kuti mwina alowelelepo.”a Patrick anatero.

Iwo anapitiliza ponena kuti   kubwela kwawo kunali kugopelekeza. 

 Magulu osiyanasiyana kuphatikizapo a mipingo mabungwe omwe siaboma,mafumu ndinso anthu okhala m’bomalo ndi omwe anatenga nawo mbali padziwoneselozo.

Zokonzekera Chikodwerero Choti Dayosisi ya Chikwawa Yatha Zaka 50 Zikuyenda Bwino.

$
0
0


Zokonzekera chikondwerero choti Dayosisi ya Chikwawa yatha zaka 50 chiyikhazikitsileni mdziko muno akuti ikuyendabwino.  

Ambuye Musikuwa amu Dayosisiyi anena izi poyankhula ndi Radio Maria ndipo anati  ngati Dayosizi, yakhazikitsa magulu osiyanasiyana omwe akuyendetsa dongosolo la chaka cha chikondwererochi chomwe chidzachitike pa 29 August chaka chino.

“Dayosisi ili pakalikiliki  yokangagalika kukodzekera mwambo wa Golden Jubilee ndipo pali zithu zingapo zomwe takonza kuti tichite. Choyamba  kukonza Golden Jubilee Celebration Committee, chachiwiri kuwona mmene mpingo wagwilira ntchito yake kuno ku Dayosisi ya Chikwawa  pa dzaka 50.”anatero a Bishop Musikuwa.

Iwo anapitiliza ponena kuti akuyenela kuchita izi ndicholinga choti akonzekere mmene angathe kuyendetsera ntchito ya mpingo pazaka 50 zikubwelazi.

“ mwambo udzafika pachimake penipeni pamene tidzankhala tikuchita mwambo wa nsembe yamisa pa 29 August chaka chomwe chino ndipo nkati mwachikodwelerochi muli zambiri zochitika.”antero Ambuye Musikuwa.

Dayosiziyi  alindi  mapulani wokhala ndi wailesi yawoyawo, kumanga malo a achinyamata komanso kumanga tchalichi chachikulu chatsopano komanso kuwonjezera magulu a chipembezo,zomwe zikhazikitsidwe posachedwa.

Bungwe la Episcopal Conference of Malawi Layamba Zokambirana Zapachaka Mudzinda wa Lilongwe.

$
0
0

Msonkhano wachiwiri wapachaka wa bungwe la maepiscope a mpingo wa katolika la Episcopal Conference of Malawi (ECM)   wayamba  mudzinda wa Lilongwe.

 Malinga ndi chikalata chomwe bungweli latulutsa ,msokhanowu wayamba lolemba   ndipo utha lachisanu.

Nthumwi ku kumsokhanowu zikukambirana nkhani yokhudza zokonzekera za chikondwerero choti Seminary ya Kachebere  yakwanitsa zaka 75,malamulo owona za chipembedzo mumpingo ndiponso  nkhani zokhudza msonkhano wa Sinodi.  

  Ma Bishopuwanso  akambirana malipoti ochokera mmakomishoni, mmadipatimenti ndi mapulojekiti osiyanasiyana amu`mpingo wakatolika.

Mavuto a Mmbanja Amavutitsa Ana.

$
0
0

Popitiliza kusinkhasinkha nkhani zokhudza banja, mtsogoleri wampingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco wati ndi okhudzidwa ndi mavuto omwe amachitika mmaanja maka amene amaika ana pamavuto.

Iye amalankhula izi pazolankhulalankhula zomwe amakhala nazo lachitatu lilonse pabwalo la St Peters Square kulikulu la mpingowu ku Vatican.

Papa Francisco wati amadziwa kuti palibe banja limene limangoyenda popanda mavuto maka chifukwa chosiyana maganizo pakati pa makolo zomwe zimachititsa kuti asiyane ndikukafuna mayankho a mavuto awo kwina.

Iye wati vutoli likakula limaika ana pamavuto.Iye anathokoza Mulungu chifukwa cha mabanja omwe amatha kupilira pa mavuto chifukwa chokhulupilira Mulungu.

Radio Maria Malawi Iyamikira Akhristu Pothandiza pa Mariatona

$
0
0

President wa Radio Maria Malawi a Nicholus Chonde wayamikira akhristu omwe akhala akuchitapo kanthu pothandiza Radio Maria Malawi m’masiku a Mariatona kuyambira pa 15 May mpaka pa 27 June 2015 yomwe imachitika ndi cholinga chofuna kupeza thandizo la  ndalama zoposera 15 Million Kwacha zothandizira ntchito yomangira Transmitter m’boma la Thyolo. .

A Chonde amalankhula izi loweruka pa mwambo wotsekera International Mariatona-yu ku phiri la Michiru  ku Chilomoni mu Arch diocese ya Blantyre.

Iwo ati ali ndi chikhulupiliro kuti thandizo lomwe akhristu achita lithandiza  wailesiyi  kukwaniritsa zolinga zake.

Polankhula wapampando wa abwenzi a Radio Maria Malawi mu Archdiocese-yi a Joseph Rappozo ati abwenzi a wailesiyi mu Archdiocese-yo apitiriza kudzipereka pothandiza wailesiyi kuti ikwaniritse zolinga zake

M’mawu ake mkulu woona ntchito za ma pologalamu ku wailesiyi Bambo Joseph Kimu alimbikitsa abwenzi a wailesiyi mdziko muno kuti azionetsanso chidwi potenga nawo mbali yokonza komanso kuwulutsa  ma pologalamu osiyanasiyana pogwiritsa ntchito luso ndi mphatso zomwe ali nazo.

Munthu Yemwe Wapha Anthu Ena Mdziko la Tunisia Anachita Kuthandizidwa

$
0
0

Malipoti ochokera mdziko la Tunisia ati munthu yemwe wapha anthu 38 pa malo ena okopera alendo lachisanu lapitali mdzikolo anathandizidwa ndi anthu ena omwe sakudziwika kuti achite chiwembucho.

Malipoti ati anthu makumi atatu mwa anthu omwe adafa pa chiwembucho ndi mzika za mdziko la Britain.

Padakali pano dziko la Britain latumiza apolisi oposa khumi ndi asanu mdziko la Tunisia kuti akathandizire pa ntchito za chitetezo pomwenso dzikolo likuwunika momwe chiwembucho chidachitikira.

Dziko la Tunisia lalengeza kuti litseka mizikiti pafupifupi makumi asanu ndi atatu 80 yomwe likuyiganizira kuti anthu omwe amapemphera mmizikitiyo amalimbikitsa mchitidwe wa ziwawa mdzikolo.

Zigawenga za Islamic State IS zalengeza kuti izo ndi zomwe zachita chiwembucho.


Ntchito Yoponya Voti Mdziko la Burundi Siyidayambe Bwino

$
0
0

Ntchito yoponya voti pa chisankho cha aphungu ndi makhansala mdziko la Burundi siyidayambe bwino, anthu omwe sakudziwika ataponya mabomba mmalo oponyera voti mumzinda wa Bujumbura ndinso mmadera ena mdzikolo.

Izi zikuchitika pamene anthu akupitiriza kuchita ziwonetsero pokwiya ndi ganizo la mtsogoleri wa dzikolo Pierre Nkurunzinza lofuna kuyima kachitatu paudindo wa pulezidenti pachisankho chomwe chichitike mdzikolo pa 15 mwezi wa mawa.

Zipani zotsutsa komanso mabungwe omwe siaboma akana kutenga nawo mbali pachisankhochi, boma litalephera kumvera malangizo a mabungwe osiyanasiyana omwe amapempha kuti chisankhochi chiyambe chayimitsidwa pofuna kukonza mavuto omwe anthu mdzikolo akudandaula.

 

 

Ulendo wa Papa Francisco Mdziko la USA Udzakhala Wopindula

$
0
0

Maepiskopi a mpingo wa katolika mdziko la United States ati akuyembekezera kuti ulendo wa Papa Francisco mdzikolo womwe uchitike mmwezi wa September  udzakhala wopindula.

 

Malipoti a Catholic News Agency ati pa ulendo wa masiku asanu ndi anayiwa pambuyo poyendera dziko la  Cuba komwe akakumane ndi atsogoleri a zipani zosiyanasiyana, Papa Francisco adzakayenderanso madera ena atatu mdziko la United States. 

Maepiskopi am’maderawa atamva izi anali okondwa kaamba koti anachiwona chinthu cha mtengo wapatali kuyenderedwa ndi mtsogoleriyu.

Papa Fransisco akatsirizira ulendo wakewu  pokumana ndi President wa dzikolo  Barrack Obama.

Papa Francisco Ayendera Papa Benedicto Wopuma

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco lachiwiri anakachezera mtsogoleri wakale wa mpingowu wopuma Papa Benedicto wa XVI yemwe wapita ku nyumba ya Papa ku dera la Castel Gandolfo mdziko lomwelo la Italy.

 

Malipoti a wailesi ya Vatican ati Papa Francisco amakafunira mafuno abwino Papa Benedicto pa ulendowo womwe akuyembekezeka kukakhalako sabata ziwiri.

 

Mtsogoleriyo anachita kupempha Papa wopumayo kuti mwezi wa July akacheze ku nyumbayo kamba koti yakhala nthawi yayitali osagwira ntchito ndipo Papa wopumayu anavomera.

Atsikana 170 Awotchedwa Mdziko la Sudan

$
0
0

Asilikali a kummwera kwa dziko la Sudan awotcha asungwana pafupifupi 170 kamba ka nkhondo ya pa chiweniweni yomwe ikuchitika mdzikolo.

 

Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC asungwanawa atagwidwa ndi asilikaliwa ena mwa iwo anagwiliridwa ndipo pa mapeto ake anawaotcha.

 

Boma la dzikolo lati silikugwilizana ndi lipoti lomwe bungwe la United Nations latulutsa lokhudza nkhaniyi ndipo ilo lati lifufuza gwero la mchitidwewu.

 

Nkhondo ya pachiweniweni yomwe yakhala ikuchitika mdzikolo inayamba mu chaka cha 2013 pulezidenti wa dzikolo Salva Kiir atachotsa wachiwiri wake Riek Marshal kaamba kotsogolera gulu lofuna kuwukira pulezidentiyo.

Makampani Opanga Zakumwa Mdziko Muno Apereka Katundu Osiyanasiyana ku Chipatala Chachikulu cha Zomba

$
0
0

Makampani opanga zakumwa a Carsberg Malawi komanso Southern Bottlers apereka katundu osiyanasiyana othandizira pachipatala chachikulu cha Zomba.

 

Popereka katunduyu mneneri wa kampani ya Southern Bottlers Mayi Towera Munthali ati kampani yawo yapereka thandizoli powona  mavuto omwe chipatalachi chikukumana nawo pantchito yake yothandiza anthu.

 

Mayi Munthali ati malinga ndi kafukufuku wawo anapeza kuti ntchito zina pa chipatalacho  sizikuyenda bwino kamba  kakuchepa kwa zipangizo.

 

Polankhulapo mkulu wa chipatalacho Dr Mathias Joshua ati katunduyu wabwera  pa nthawi yake   kamba koti chipatalachi chikukumana ndi mavuto ambiri  monga kusowa kwa mankhwala komanso zipangizo zoyezera matenda osiyanasiyana.

 

Katundu yemwe waperekedwa pa chipatalachi ndi wokwana 77 miliyoni kwacha ndipo ma kampaniwa akugwira ntchitoyi mothandizidwa ndi mabungwe a City Hope International komanso Medi Care a mdziko la  Amerika mu zipatala za mdziko muno za  Ekwendeni m’boma la Mzimba, Queen Elizabeth mu mzinda wa Blantyre komanso Zomba Central.

Viewing all 1875 articles
Browse latest View live


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>