Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all 1875 articles
Browse latest View live

Ophuzira pa Sukulu ya Ukachenjede ya Lilongwe Technical Ayamba Kunyanyala Maphunzirowo

$
0
0

Ophunzira a pasukulu yosulira anthu maluso osiyanasiyana ya Lilongwe Technical ayamba kunyanyala maphunziro awo pokwiya ndi mavuto osiyanasiyana omwe akukumana nawo pa sukuluyo. Pulezidenti wa anthu omwe amaphunzira pasukuluyo Promise Daniel Chidothi wawuza Radio Maria Malawi mumzinda wa Lilongwe kuti ophunzira pa sukuluyi, akukumana ndi mavuto osiyanasiyana kuphatikizapo a zaumoyo. Chidothi wati ophunzira akudandaula kuti madzi mzimbudzi za pasukuluyi anasiya kutuluka zomwe zikuchitsa kuti azitenga madzi akafuna kukadzithandiza komanso kuti madzi akasamba mzipinda zosambira samachokamo. Iye anawonjezela ponena kuti akudandaulanso kuti patha chaka tsopano chipelekereni pempho kwa akuluakulu a pasukuluyo kuti ayambe kupereka maphunziro a makina a komputa kwa ophunzira a ntchito za manja, pofuna kuti nawo adziyendera limodzi ndi dziko pogwiritsa ntchito zipangizo zamakono koma mpaka pano palibe chomwe chikuchitika Radio Maria Malawi inalephera kumva zambiri kuchokera kwa akuluakulu a pasukuluyi kamba koti anali ndi zokambirana.


Kusamvana Kwakula Pakati pa Dziko la Israel ndi Palestine

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco wapempha atsogoleri a mayiko a Israel ndi Palestine kuti athetse kusamvana komwe kwakhala kukuchitika pakati pa mayiko awiriwa.

Kusamvana komwe kwayambiranso masiku apitawa pamene anthu awiri anakachita za chiwembu pa tchalitchi lina mdziko la Israel ndipo anapha anthu asanu ndi kuvulaza ena khumi ndi atatu akuti kwasokoneza bata ndi mtendere zomwe zinalipo mu mzinda wa Yerusalemu ndinso mizinda ina yomwe ili kufupi ndi mzindawu.

Papa Francisco wati mayiko awiriwa akuyenera kuwonetsetsa kuti mzinda wa Yerusalemu ukutetezedwa mokwanira kamba koti ndi mzinda opatulika mu mbiri ya chikhristu.

                         

 

Beam Trust Yakonzeka Kulimbikitsa Amayi pa Chuma

$
0
0

Bungwe la Beautify Malawi (BEAM) TRUST lati posachedwapa liyamba kulimbikitsa amayi komanso asungwana kukhala odzidalira pachuma pamwamba pa ntchito zake zowonetsetsa kuti mdziko muno muli ukhondo.

Mkulu wa bungweli Mayi Getrude Hendrina Mutharika,yemwenso ndi mayi wa fuko la dziko la Malawi, ndi yemwe wanena izi kulikulu la bungwe la United Nations mumzinda wa New York mdziko la America, pamwambo okhazikitsa tsiku lodzidalira pachuma padziko lonse.

Iye anati bungweli lizigwiritsa ntchito zinyalala zomwe lizitolera mdziko muno pozisandutsa zinthu zomwe zingathandize amayi komanso asungwana kupeza chuma, chomwenso chingathandize kupititsa patsogolo chitukuko cha dziko Malawi.

Mayi Mutharika anauza nthumwi ku msonkhanowo kuti kusowa kwa chikole, Matenda a Malungo, komanso HIV ndi Edzi ndi ena mwamavuto omwe amayi ndi asungwana akukumana nawo mu Africa, ngakhalenso mdziko la Malawi.

Pamenepa iwo apempha mabungwe ndi makampani kuti agwirane manja ndi mabungwe ngati Beam pa ntchito yolimbikitsa amayi kukhala wodzidalira pa chuma.

Mayi wa fukoyu watsimikiza kuti bungwe lake lichita chotheka kuti cholinga chake chowonetsetsa kuti mdziko la Malawi  muli ukhondo chikwanilitsidwe, pofuna kuthandizanso amayi kuchita malonda awo mmalo osamalilika.

Mwambowu womwe unachitika ndi mutu wakuti "Amayi Odzidalira ndi Makina Atsopano Opititsira Patsogolo Chitukuko cha Makampani Mmaiko Amene Akukwera Kumene," panafika amayi omwe anachita bwino pa ntchito zamalonda, mabungwe omwe si aboma ndi magulu osiyanasiyana.

 

UKALISTIYA

$
0
0

UKALISTIYA BY ST ANDREWS CATH. CHOIR MUA PARISH DIOCESE OF DEDZA

Dotolo Amwalira Atadwala Matenda a Ebola

$
0
0

Dotolo wina wa mpingo wakatolika amene wakhala akudzipeleka kwambiri pothandiza anthu odwala matenda a Ebola mdziko la Siera Lione akuti wamwalira atapezeka ndi matendawa.

Dotoloyo Martin Saliya yemwe anali ndi zaka 44 zakubadwa,akuti anali m’modzi mwa madotolo amene amagwira ntchito yawo modzipereka pothandiza anthu odwala matendawa mdzikolo, ndipo akuti wakhala akunenetsa kuti iye sangasiye kuthandiza anthu odwala  matenda a Ebola pofuna kuteteza moyo wake.

Kafukufuku wa bungwe la zaumoyo pa dziko lonse la World Health Organization wasonyeza kuti chibukileni matenda a Ebola chaka chino, anthu ogwira ntchito za umoyo omwe akhudzidwa ndi matendawa alipo 570 ndipo mwa anthuwa 354 amwalira.

Abwenzi a Radio Maria aku Archdayosizi ya Lilongwe ndi Okondwa ndi Kagwiridwe Ntchito ka Wailesiyi

$
0
0

Abwenzi a Radio Maria ochokera ku ma parishi a Mponera, Nambuma ndi Mpherere parish mu Arch-dayosizi ya Lilongwe ati ndi okhutira ndi momwe Radio Maria Malawi ikugwilira ntchito zake.

Abwenziwa anena izi lachisanu atafika kulikulu la wailesiyi ku Mangochi komwe mwa zina athandiza wailesiyi ndikulowanso nawo m’maprogramu osiyanasiyana.

Mmawu ake  wapampando wa abwenziwa aJoseph Kapiza ayamikira abwenzi a mu arkdayosiziyi kamba kokonza ulendo wodzayendera likulu la wailesiyi ndi cholinga choti adziwonere okha zina mwa zimene wailesiyi imasowa poyendetsa  ntchito zake.

Paulendowu abwenziwa analinso ndi m’bindikilo omwe unachitikira ku tchalichi la St John the Babtist lomwe lili kufupi ndi ku likulu la wailesiyi .

Mkulu owona za mapulogalamu ku wailesiyi Bambo Joseph Kimu ndi amene anatsogolera m`bindikilowo.

Mmawu awo Bambo Kimu  alimbikitsa abwenziwa kuti pomwe akufalitsa za ubwino wothandiza Radio Maria Malawi, akuyeneranso kumaonetsa zitsanzo zabwino pachikhristu chawo.

Mutharika Akhululukira Akayidi 268

$
0
0

Pamene dziko lino lolemba pa 6 July likuyembekezeka kukondwelera ufulu wodzilamulira, m’tsogoleri wa dziko lino Professor Peter Mutharika wakhululukira akayidi 268 omwe amasungidwamundende zosiyanasiyana m’dziko muno.

 

Malinga ndi chikalata chomwe  unduna wa za m’dziko watulutsa akayidi omwe ayikidwa pa m’ndandanda woti akhululukidwe ndi okhawo omwe anatsala  ndi masiku ochepa kuti amalize kugwira ukayidi wawo, ndipo akhala akuonetsa makhalidwe abwino, komanso omwe anali m`gulu la akayidi omwe sanapalamule milandu ikuluikulu.

 

Pulezidenti Mutharika wakhulukilira akayidiwa pomwe tsopano dziko lino likutha zaka makumi asanu ndi chimodzi lili paufulu odzilamulira.

Zigawenga za Boko Haram Zapha Anthu Pafupifupi 150 Sabata Ino

$
0
0

Zigawenga za Boko Haram zapha anthu pafupifupi zana limodzi ndi makumi asanu sabata ino mchigawo cha Borno mdziko la Nigeria.

Anthu omwe awona izi zikuchitika awuza wailesi ya BBC kuti anthu a mfuti analowa mmudzi wina omwe uli pafupi ndi nyanja ya Chad lachitatu ndikupha anthu 97 kuphatikizapo amayi ndi ana.

Anthu ena 48 aphedwa lachiwiri atangomaliza mwambo wamapemphero omwe anali nawo mmidzi ina iwiri mdera lomwelo koma pa chiwembuchi amayi anasiyidwa.

Anthu ena afa paziwembu zosiyanasiyana zomwe zakhala zikuchitika mdzikolo musabata ino kufikitsa chiwerengero cha anthu omwe aphedwa musabata yokhayi pa 150.

Padakali pano malipoti a bungwe lomenyera ufulu wa anthu padziko lonse la Amnesty International akusonyeza kuti anthu 17 sauzande ndi omwe aphedwa ndi zigawengazi kuyambira mchaka cha 2009 pomwe zidayamba mtopola mdzikolo pofuna kukhazikitsa boma laulamuliro wa chisilamu


Anthu Akupitilira Kukhala Mopanda Ukhondo pa Dziko Lonse

$
0
0

Anthu oposa 2.4 miliyoni ati akupitiliza kukhala mmoyo osowa zipangazo zoyenera kuti azikhala mwaukhondo pa dziko lonse.

Malinga ndi wailesi ya mpingo wa katolika kulikulu la mpingowu ku Vatican, lipoti lomwe bungwe la mgwirizano wa mayiko la United Nations latulutsa mogwirizana ndi nthambi yake yowona za ana ya UNICEF lati ambiri mwa anthuwa ndi omwe amakhala kumidzi zomwe zikupereka chiwopsezo choti ngati ntchito yopititsa patsogolo ukhondo maka pankhani zokhudza madzi sizisintha, anthu ambiri maka ana azimwalira.

Lipotilo lomwe mutu wake ndi Zomwe zakhala zikuchitika pankhani za Ukhondo ndi Madzi Akumwa Abwino, limawona zomwe zakhala zikuchitika kwa zaka zingapo pankhani zaukhondo maka pano pamene mfundo zosiyanasiyana zachitukuko za Millenium Development Goals MDGs zikutha chaka chino.

Ilo lati pafupifupi 90 mwa anthu zana aliwonse akukwanitsa kupeza madzi abwino padziko lonse, koma lati anthu 2.4 miliyoni maka akumidzi akupitiliza kuvutikira madzi abwino.

Mkulu oyendetsa ntchito za umoyo kubungwe lowona za umoyo padziko lonse  la World Health Organisation Maria Neira, wachenjeza kuti ngati  anthu ambiri sapatsidwa mwayi opeza madzi abwino ntchito yolimbana ndi matenda omwe amadza chifukwa chosowa madzi abwino apitilira kupha anthu.

Atsogoleri a mmayiko akuyembekezeka kukumana mmwezi wa September chaka chino, pomwe akufuna apange mfundo zina zachitukuko zotchedwa Sustainable Development Goals SDGs zomwe ndi kuphatikizapo kuchepetsa  umphawi, imfa za ana,kusintha kwa nyengo ndi zina pomafika mchaka cha 2030.

Dayosizi ya Mongu Dziko la Zambia Yatolera Thandizo la Anthu a Mdziko la Sudan

$
0
0

Dayosizi ya Mongu ya mpingo wakatolika mdziko la Zambia yatolera thandizo la ndalama zofuna kuthandizira anthu okhala kummwera kwa dziko la Sudan.

 

Malinga ndi malipoti a wailesi ya ku likulu kwa mpingo wa katolika ya Vatican, dayosiziyi yachita izi pofuna kuyankha pempho lochokera ku bungwe la Amecea.

 

Thandizoli latumizidwa kale kudzera ku bungwe lomwe limagwira ntchito za chifundo padziko lonse la Caritas International la mdzikolo.

 

Episkopi wa Dayosiziyo Ambuye Evans Chinyama Chinyemba wati ngakhale dzikolo lili kutali ndi dziko la Sudan awonetsetsa kuti achite ubale wabwino.

 

Thandizolo latoleredwa kuchokera kwa akhristu akufuna kwabwino ammaparishi osiyanasiyana, mabungwe a mpingo komanso malo a mpingo wakatolika a mu dayosiziyo.

Apolisi ku Dowa Amanga Mnyamata wazaka 17 kamba Kogwilira

$
0
0

Apolisi m’boma la Dowa amanga mnyamata wazaka 17 zakubadwa pomuganizira kuti wagwilira mai wazaka 73.

 

Ofalitsa nkhani za apolisi m’bomali Sergeant Richard Kaponda wawuza Radio Maria Malawi kuti mnyamatayo yemwe satchulidwa dzina kamba koti ndi wachichepere panthawiyi amaweta ng’ombe za nyakwawa ina yomwe imakhala pafupi ndi msewu wawukulu okhotera ku Dowa.

 

Iye adakumana ndi mayiyo kutchire komwe amadyetsa ng’ombezo pomwe mayiyo amakafuna ndiwo.

 

Zotsatira zakuchipatala zasonyeza kuti mnyamatayo anagwiliradi mayiyo ndipo akuyembekezera  kukawonekera kubwalo la milandu posachedwapa komwe akayankhe mlandu ogwilirira

CCJP MEDIA STATEMENT

$
0
0

                      

On the murder of Mr Issa Njauju, Director of Corporate Affairs, Anti-Corruption Bureau

1.0. Preamble

We, the Catholic Commission for Justice and Peace of the Episcopal Conference of Malawi are deeply saddened by the killing of the Anti Corruption Bureau Director of Corporate Affairs Mr. Issa Njauju. Whatever the reason for his murder, we strongly condemn his killing. This murder further highlights the levels of insecurity in our country.  Our thoughts and prayers are with his family.  

We also commiserate with his work colleagues.  ACB staff, who are legally mandated by the state, to deal with corruption cases on behalf of all Malawians, deserve our full support at this difficult time. Such brutal acts cannot be allowed to affect the anti-corruption initiatives currently underway in response to cash gate. 

2.0. Our Concerns

Whilst there is no official report yet providing details as to the reasons of the killing of the Director of Corporate Affairs for ACB; we in CCJP are worried that this incident will:

         I.            Send fear amongst and hinder the vital work of the anti-corruption agencies and justice delivery services like the courts, police and in particular the ACB.

    II.        Will jeopardize the anti-corruption efforts of government as it seeks to address the corroding malaise of financial looting that has impacted on the country’s limited resources, and which is currently affecting the delivery of timely and quality public services to all citizens.

 

 3.0. Our Appeal

Considering the possible impact of Mr. Njauju’s murder upon the anti-corruption drive in Malawi, our strong appeal is to the following institutions:

         I.            Malawi Police: To expedite the murder investigations of the ACB Corporate Affairs Director so that TRUTH is established and takes away any wild speculation.

       II.            Malawi Government: To provide the necessary support to the Malawi Anti-Corruption Bureau so that the security of its officials and offices is ensured, enabling them to carry out their national duty without fear and interference. 

      III.            Malawi Government: To prioritize internal security measures to ensure national security at all levels of the society which of late has been a great cause of worry.

   IV.            Malawian citizens and communities: To provide to the Malawian police services and the government any information or details related to this murder and other security incidents. Without citizens’ participation in addressing this country's security challenges, insecurity will continue to haunt us.

     V.            Justice Delivery Services, Police, ACB and Courts: To expedite current corruption-related cases, so as to limit the time and space for criminal interference and disturbance.  With delayed prosecutions hard core criminals will continue to seek ways of obstructing the justice system and structures.

   VI.            The Donor Community: Whilst appreciating your efforts in assisting government to conduct financial audits that are exposing various financial leakages that occurred in the past; we appeal to you to continue and strengthen your assistance to the Malawi government in capacitating the Police to combat crime; to the ACB in investigating and concluding timely corruption cases; and to the judiciary to effectively and timely deliver justice.

  VII.            The Media: Whilst CCJP acknowledges your efforts at exposing crime incidences, we in CCJP appeal to you to increase investigative journalism that provides information to complement justice delivery efforts in Malawi.

4.0. Conclusion

The Catholic Commission for Justice and Peace (CCJP) makes this media statement in solidarity with the other key players in the anti-corruption drive in Malawi and to express our sadness on the sudden death of the ACB Director of Corporate Affairs Mr. Issa Njauju (May His Soul Rest in Peace). Let us not get discouraged from our commitment to fight corruption and graft in Malawi as our continued efforts are needed now more than ever to ensure good governance and the future security of our country.

 

Signed:  Chris Chisoni CCJP National Secretary. 07/07/15

Achinyamata Apemphedwa Kukhala Odzisunga

$
0
0

Dayosizi ya Mangochi ya mpingo wakatolika yapempha achinyamata mudayosiziyo kuti adzisunge pofuna kuti adzathe kukwaniritsa utumiki wawo mtsogolo.

Mlembi wamkulu wowona za chiyitanidwe mu dayosiziyi Bambo Raphael Mkuzi,ndi omwe apereka pempholi lamulungu pamsonkhano wa pa chaka wa achinyamata ochokera mmaparishionse 19 a mudayosiziyo pomwenso mpingo wakatolika pa dziko lonse umatsekera chaka cha chipembedzo.

Bambo Mkuzi ati achinyamata omwe masiku ano akudziwika kuti ndi atsogoleri a lero akuyenera kukula ndimakhalidwe abwino komanso awuzimu pofuna kuteteza tsogolo la mpingo womwe ukudalira iwo.

“Masiku am’mbuyomo timati achinyamata ndi atsogoleri a mawa, koma masiku ano tikuti ndi a lero ndi mawa chifukwa zomwe akuchita lero ndi zomwe zidzakhale zikuwonekera mtsogolo,” anatero Bambo Mkuzi.

Iwo ati anasonkhanitsa achinyamatawo kuti awaphunzitse mtima wokhala limodzi ngati mpingo komanso zachipembedzo chawo.

“Takhala ndi zolankhulalankhula zokhudza chiyitanidwe monga unsembe, ubulaazala wanzipani, usistere komanso mabanja ndi cholinga chofuna kuwakonzekeretsa mu njira zimene angasankhe” anatero Bambo Mkuzi.

Polankhulapo mkulu woyendetsa mapulogalamu a zaumoyo ku bungwe la zaumoyo mu mpingowu la Catholic Health Commission a Richard Mankhwazi, ati achinyamata akuyenera kusamala kwambiri maka pamene matupi awo akusintha, yomwe ati ndi nthawi imene tsogolo lawo limakhala pachiwopsezo.

A Makhwazi ati,“ngati achinyamata sadzisamala ngakhalenso kudziletsa matupi awo sangakhale athanzi ndipo moyo wa mayitanidwe ndi wosatheka.”

Chaka chilichonse tsiku lamulungu lotsiriza mu chaka cha mpingo lomwe limakhala tsiku la chaka cha Yesu Khristu Mfumu ,dayosizi ya Mangochi imachita msonkhano wa achinyamata kuti awonetse umodzi wawo ndikupempherera limodzi.

 

 

 

 

Dziko la Italy Litsatire Mfundo Zokhudza Banja

$
0
0

Mlembi wamkulu wa bungwe la maepiskopi mdziko la Italy Bishop Nunzio Galatino wati dziko la Italy likuyenera kuwonetsetsa kuti mfundo zake zoyendetsera dzikolo pa nkhani yokhudza banja, zikhale zokhazo zowonetsetsa kuti banja lizikhala la pakati pa mwamuna ndi mkazi.

Bishop Galatino wanena izi potsatira mphekesera yoti nduna yayikulu yadzikolo Matteo Renzi ikuyembekezeka kupereka maganizo oti maukwati a anthu ofanana ziwalo akhale ovomerezeka mdzikolo.

Malipoti a wailesi ya mpingo wakatolika ku likulu la mpingowu ya Vatican Radio yati bishop Galatino watsutsanso zoti iye ali mgulu la anthu omwe akufuna kuti maukwati a mtunduwu azivomerezedwa.

Mlembi wamkulu wa bungwe la maepiskopi mdziko la Italy Bishop Nunzio Galatino wati dziko la Italy likuyenera kuwonetsetsa kuti mfundo zake zoyendetsera dzikolo pa nkhani yokhudza banja, zikhale zokhazo zowonetsetsa kuti banja lizikhala la pakati pa mwamuna ndi mkazi.

Bishop Galatino wanena izi potsatira mphekesera yoti nduna yayikulu yadzikolo Matteo Renzi ikuyembekezeka kupereka maganizo oti maukwati a anthu ofanana ziwalo akhale ovomerezeka mdzikolo.

Malipoti a wailesi ya mpingo wakatolika ku likulu la mpingowu ya Vatican Radio yati bishop Galatino watsutsanso zoti iye ali mgulu la anthu omwe akufuna kuti maukwati a mtunduwu azivomerezedwa.

Anthu Awiri omwe Akupikisana pa Chisankho Mdziko la Uganda Amangidwa

$
0
0

Anthu awiri omwe akufuna kudzapikisana nawo pa mpando wa pulezidenti pachisankho chomwe chichitike mdziko la Uganda anamangidwa kamba kochititsa misonkhano popanda chilolezo cha apolisi.

Mmodzi mwa anthuwa ndi a Kizza Besigye omwenso akhala akuyima pa zisankho za pulezidenti pa zisankho zomwe zakhala zikuchitika mdzikolo mzaka za m’mbuyomu.

Padakali pano akuluakulu awiriwa amasulidwa.

Chisankho cha pulezidenti mdziko la Uganda,chichitika chaka cha mawa pomwe mtsogoleri wadzikolo Yoweri Museveni, akuyembekezeka kuyimanso.

Pulezidenti Museveni wakhala akulamulira dzikolo kwa zaka 29 zomwenso sizikusangalatsa anthu mdzikolo.


Nthambi ya Zaumoyo Yayamikira Abambo pa Nkhani ya Mdulidwe

$
0
0

Nthambi ya zaumoyo yowona za mdulidwe wa abambo mdziko muno yayamikira abambo omwe akuwonetsa chidwi potenga nawo mbali pa nkhani za mdulidwe omwe azaumoyo akulimbikitsa.

Mkulu oyendetsa ntchito zolimbikitsa anthu pa nkhani za mdulidwe wakuchipatala a Pius Mtike, ndi omwe ayamikira abambowa pomwe Radio Maria Malawi imafuna kudziwa momwe ndondomeko ya mdulidwe wa abambo yakhala ikuyendera mumzinda wa Zomba potsatira pempho la nthambiyi.

A Mtike ati kudzera mu pulojekiti ya Sankhani Moyenera yomwe idayamba mchaka cha 2013, amuna oposa 19 sauzande m’boma la Zomba achita mdulidwe.

Iwo ati nthambiyi ikukonza ndondomeko ina yolimbikitsa amuna kuchita mdulidwe kuyambira pa 27 July mpaka pa 5 September chaka chino pofuna kuchepetsa mpata wa kufala kwa kachirombo ka HIV komwe kamayambitsa matenda a Edzi.

Pamene kafukufuku wa bungwe lowona za umoyo padziko lonse la World Health Organisation W.H.O akusonyeza kuti mdulidwe wa abambo umathandiza kuchepetsa kufala kwa kachiromboka.

A Mtike ati panthawiyi nthambi yawo ikhala ikuzindikiritsa anthu zaubwino wa njirayi pochepetsa kufala kwa matenda a HIV/AIDS pogwiritsa ntchito akuluakulu a zaumoyo, a zisudzo komanso masewero a mpira.

Ambuye Msusa Alimbikitsa Akhristu Kubzala Mitengo

$
0
0

Episkopi wa Archdayosizi ya Blantyre olemekezeka ambuye Thomas Luke Msusa alimbiikitsa akhristu a mpingowu mu dayosizi ya Zomba kuti adzipereke pa ntchito yobzala mitengo.

Ambuye Msusa alankhula izi pa mwambo wodzoza madikoni anayi kukhala ansembe, komanso kuchita chikondwelero cha zaka 25 mu unsembe wa Bambo Patrick Phalawala.

Iwo ati akhristu akuyenera kudzipereka pa ntchito yobzala mitengo yomwe imateteza kukokoloka kwa nthaka ndi zinthu zina zofunika pa miyoyo ya anthu.

Iwo ati anthu m’dziko muno akuyenera kuonetsetsa kuti akutengapo mbali yayikulu pogwira ntchito zoteteza ndi kubwezeretsa zachilengedwe pofuna kupewa ngozi zosiyanasiyana zomwe dziko lino lakhala likukumana nazo kamba ka kuwonongeka kwa  chilengedwe.

Makwaya Akuyenera Kukhala Paubale Wabwino

$
0
0

Ubale wabwino pakati pa makwaya ati ndi njira imodzi yopititsira patsogolo moyo wauzimu pakati pa akhristu mu mpingo.

Mayi Bibiana Jimu omwe ndi wapampando wa Kwaya ya amayi ya St Agness ku parishi ya Bvumbwe mu Arkidayosizi ya Blantyre ndi omwe alankhula izi pomwe kwaya yawo inayitanitsa kwaya ya St Michaels Nansangwa kuti adzachezerane ndi kugawana luso la mayimbidwe.

Mayi Jimu ati ubale pakati pa makwaya a amayi ungathandize amayi kuzama pa uzimu komanso kukulitsa chikhulupiliro chawo mwa Mulungu.

Iwo ati kwayayi ndi chifukwa chake inaitana anzawowa kuti agawane nawo luso komanso kuthandizana pa  momwe angapititsire patsolo moyo wawo wa uzimu pomwe akutumikira Mulungu kudzera m'mayimbidwe.

Total Land Care Ilimbikitsa Ukhondo komanso Kuteteza Chilengedwe Msukulu za Pulayimale

$
0
0

Bungwe la Total Land Care lati ndi cholinga cha bungweli kuwonetsetsa kuti likulimbikitsa ukhondo komanso kuteteza chilengedwe msukulu za pulayimale m’dziko muno.

Mkulu wa bungweli a Jeliam Chiputu ndi yemwe walankhula izi m’boma la Mchinji pomwe limapereka mphatso kwa sukulu zomwe zachita bwino ku mbali ya ukhondo m’bomalo.

Iwo ati bungwe lawo lapeleka mphotozo pofuna kulimbikitsa sukulu zina ukhondo ndi ntchito yosamalira ndi kuteteza zachilengedwe.

Polankhulanso pa mwambowo mlangizi wa zamaphunziro m’bomalo  Agnes Zondolo yemwe anali mlendo wolemekezeka pa mwambowo walangiza sukulu zomwe zalandira mphotozo kuti zipitilize kudzipereka pogwira ntchitozi.

Sukulu zomwe zachita bwino ndikulandira nawo mphotozo ndi monga za Ndaula, Chazuka ndi Mpachila za kwa mfumu yayikulu Mavwele m’boma lomwelo la Mchinji ndipo zalandira mphatso monga mipira , zolembera ndi  motayira zinyalala.

Anthu 14 Afa ndi Bomba Mdziko la Chad

$
0
0

Bomba la timke nawo lapha anthu 14  pa msika wina m’dziko la Chad.

Munthu yemwe akumuganizira kuti wachita izi ati anavala ngati munthu wa mayi kenaka ndi kulowa mu msika wina komwe anakaphulitsa bombalo iye ndi kuferanso pamalo omwewo.

Mwa anthu 14 omwe afa ndi bombalo asanu ndi anayi  ndi amayi.

Gulu la zigawenga za Boko Haram ndi zomwe akuziganizira kuti zinakonza chiwembucho.

Malingana ndi atolankhani a Nyuzi 24 , dziko la Chad ndi limodzi mwa mayiko omwe anachita mgwirizano ndi dziko la Nigeria pofuna kulimbana ndi gulu la zigawengazi.

Viewing all 1875 articles
Browse latest View live


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>