Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all 1875 articles
Browse latest View live

Ntchito Zoweruza Milandu Ziyamba Kuyenda Mwachangu

$
0
0

Ntchito zoweruza milandu mmabwalo osiyanasiyana mdziko muno ati ziyamba kuyenda mwachungu potsatira kusintha kwa zipangizo  zogwilira ntchitoyi zomwe mabwalo aakulu alandira mdziko muno.

Mmodzi mwa akuluakulu oweruza milandu ku bwalo lalikulu la Appeal mu mzinda wa Blantyre Justice Dastain Mwaungulu ndi yemwe wanena izi polankhula ndi  Radio Maria Malawi pomwe wailesiyi imafuna kudziwa zina mwa zifukwa zomwe zimachedwetsa kaweruzidwe ka milandu mmabwalo  a milandu mdziko muno.

Justice Mwaungulu wati pali mavuto ambiri omwe amachititsa kuti anthu azichedwa kulandira chilungamo pankhani zawo monga kusowa kwa zipangizo za makono.

Iwo ati zinthu ziyamba kuyenda bwino pomafika chaka cha mawa, potsatira zipangizo zomwe mabwalowa alandira kuchokera ku boma.

Justice Mwaungulu wati ngakhale mabwalo a milandu mdziko muno akhala akukumana ndi mavuto pa kagwiridwe ka ntchito zake, dziko lino likupitiliza kukhala mgulu la mayiko omwe makhothi awo amaweruza milandu mwachilungamo.


Papa Francisco Apepesa Mabanja omwe Ataya Abale Mdziko la China

$
0
0

Mtsogoleri wampingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco wapereka uthenga opepesa ku mabanja omwe ataya abale awo pangozi yomwe yachitika mdziko la China makina a fakitore ina ataphulika mchigawo chakumpoto kwa dzikolo.

Iye wati ndi wokhudzidwa kwambiri ndi imfa ya anthu omwe amwalira pangoziyo ndipo wati akhala akupemphelera  anthu omwe akhudzidwa ndi ngoziyi.

Kadinala Njue Wapempha Anthu a Mdziko la Kenya kuti Akhale a Makhalidwe Abwino

$
0
0

Kadinala John Njue wa m’dziko la Kenya wapempha m’zika za dziko la kwawo  zomwe zikukhala m’dziko la America kuti zisamatengere  makhalidwe oyipa omwe mzika zina zimachita m’dzikomo.

 

Kadinala Njue wanena izi pamsonkhano wapadera omwe anakonzekera m’zika za dziko la Kenya zomwe zikukhala mdziko la America.

 

Iye wati kafukufuku yemwe anachita wasonyeza kuti mzika zambiri za m’dziko la Kenya zikapita kunja kwa dzikolo  monga ku America zikumatengera makhalidwe osayenera  zomwenso zikudzetsa mavuto akululu pakati pawo.

 

Iye wati akanakonda  mzika za dzikolo zitagwilitsitsa makhalidwe okhawo omwe amalimbikitsa ubale wabwino ndi Mulungu.

 

Anthu oposera chikwi chimodzi  a mdziko la Kenya omwe akukhala mdziko la America ndi omwe anafika pa msonkhanowo.

 

 

Mayi wa Zaka 50 Wadzipha

$
0
0

Mayi wina wa zaka 50 m’boma la Ntchisiwadzipha podzimangilira ku mtengo kamba koti anapezeka ndi matenda a khansa.

 

Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomali Sergent Gladson M’bumpha watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati izi zachitika usiku wa lachiwiri sabata ino m`mudzi mwa Khadani kwa mfumu yayikulu Chikho m’bomalo. 

Iwo ati malemuyo wakhala akudwala komanso kugonekedwa mchipatala chachikulu cha Ntchisi kamba ka vuto la matendawa kwa nthawi yaitali.

Malinga ndi Sergent M’bumpha malemuyu wakhala akudwala matendawa kwa nthawi yaitali ndipo wakhala akugonekedwa kangapo konse ku chipatala chachikulu cha Ntchisi.

Mamuna wake wa malemuyo Zamtima Kanjedza atawona kuti sizikusintha ati pa 11 mwezi uno anaganiza zotengera mkazi wawoyo kwa sing’anga wa mmudzi wina wa m’bomalo. 

 

Atafika kwa sing’angayo ati sanathe kulandira thandizo kaamba koti mayiyo anali atafooka kwambiri. 

 

A M’bumpha ati usiku wa lachiwiri sabata ino ndi pamene amazindikira kuti malemuyo sakuoneka, atayang’ana anapeza kuti wamwalira atadzimangilira pa mtengo.

 

Malipoti achipatala asonyeza kuti malemuyo wamwalira kamba koti amalephera kupuma ndipo kuti palibe yemwe akumuganizira kuti wachita chiwembucho.

 

Malemuyo Selina Zamtima ankachokera mmudzi mwa Kankowe kwa mfumu yayikulu Nthondo m’boma lomwelo la Ntchisi.

 

 

 

Pulezidenti Kiir Asayinira Pangano la Mgwirizano

$
0
0

Mtsogoleri wadziko la South Sudan A Salva Kiir wati asayinira mgwirizano odzetsa mtendere pakati pa iye ndi magulu owukira boma mdzikolo.

Pulezidenti Kiir lolemba analonjeza kuti asainira panganoli pakatha sabata ziwiri.

Malipoti a NEWS 24 ati mlembi wa boma la dziko la United States  A John Kerry awuza Pulezidenti Kiir kuti zomwe akuchita ndi kulephera utsogoleri posafuna kusayinira panganolo kamba koti nkhondo yomwe yakhala ikuchitika mdzikolo kuyambira mchaka cha 2013, yapha anthu zikwizikwi.

Pulezidenti Kiir wati akuyenera kuti afunse maganizo koma walonjeza a Kerry kuti asayinira panganolo masiku akudzawa.

Padakali pano mtsogoleri wa kumbali yowukira boma a Rik Marshal mdzikolo wasayinira kale panganolo.

Bungwe la MEC Lichititsa Chisankho Chapadera

$
0
0

Bungwe loyendetsa zisankho mdziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC) lachiwiri lichititsa chisankho chapadera cha makhansala mmadera asanu  momwe mulibe makhansala pazifukwa zosiyanasiyana mdziko muno.

 

Muuthenga omwe bungweli latulutsa, wapampando wabungweli  Justice Maxon Mbendera SC, wati anthu okhawo omwe analembetsa mu kaundula wa voti m’madera omwe kuli chisankho ndi omwe akuyenela kukaponya voti.

 

Justice Mbendera wati pachisankhochi bungwe la MEC layikanso ndondomeko zomwe zithandize anthu olumala, amayi oyembekezela, okalamba ndi odwala kuti akavote mosavutikira.

 

Mundondomekoyi,bungweli lapempha anthu ogwira ntchito mmalo oponyera voti kuti athandize anthuwa powapatsa mwayi osayima panzere ndi cholinga choti aponye voti yawo mwachangu.

 

Bungweli lati anthu omwe ali ndi vuto losawona alinso ndi mwayi operekezedwa ndi munthu yemwe adalembetsa mu kaundula wa voti pachisankhochi kuti akawathandizire posankha munthu yemwe akumufuna pogwiritsa ntchito chikombole cha mabowo anayi chothandizira anthuwa povota.

 

Anthu omwe akuyembekezeka kuvota pachisankhochi mmadera onse asanu ndi 27,272. Malinga ndi Justice Mbendera zotsatira zachisankhochi zikuyembekezeka kudzalengezedwa lachitatu pa 26 sabata ino.

Apolisi m’boma la Dowa Agwira Mzika za Mdziko la Ethiopia

$
0
0

Apolisi m’boma la Dowa amanga mzika zisanu ndi zinayi za mdziko la Ethiopia zomwe zalowa mdziko muno popanda zitupa zoyenera.

 

Apolisi m’bomalo agwira anthuwa usiku wa lamulungu lapitali atawapeza akuchokera patchire lina pomwe anabisala podikilira nthawi kuti akalowe kumalo a anthu othawa kwawo m’bomalo a Dzaleka.

 

Malinga ndi ofalitsa nkhani za apolisi m’bomali Sergeant Richard Kaponda anthuwa omwe ndi a zaka zapakati pa 16 ndi 26 awuza apolisi kuti pa nthawiyi anali paulendo opita mdziko la South Africa pothawa umphawi mmayiko awo.

 

Anthuwa akuyembekezeka kukawonekera kubwalo loyamba lamilandu m’bomalo komwe  akayankhe mulandu olowa mdziko muno popanda zitupa zowayenereza.

Zigawenga Zisanu za Boko Haram Zaphedwa

$
0
0

Anthu asanu a mgulu la zigawenga za Boko Haram aphedwa ndi asilikali a boma mdziko la Nigeria.

 

Asilikaliwo apha zigawengazo zitachitira chiwembu mdipiti wa galimoto za asilikali zomwe zimaperekeza mkulu wa asilikali paulendo wake okawonana ndi asilikali a boma mchigawo cha Borno mdzikolo pomwe msilikali wa boma mmodzi waphedwa.

 

Mkulu wa asilikaliyo anatenga udindowu m’mwezi wa July chaka chino mtsogoleri wadzikolo Mahammudu Buhari atachotsa mmaudindo akuluaukulu asilikali chifukwa cholephera kuthana ndi gulu la zigawengalo.

 

Gululo linayamba kuchitira anthu ziwembu mchaka cha 2009 pofuna kukhazikitsa boma loyendetsedwa ndi malamulo a chisilamu mdzikolo.


Dziko la France Lipereka Ulemu kwa Omwe Ateteza Sitima ku Zauchifwamba

$
0
0

Dziko la France lolemba lapereka ulemu wapadera kwa mzika zitatu za mdziko la America ndi ina yaku Britain chifukwa cholepheretsa munthu wina wamgulu la zaufwamba yemwe amafuna kupha anthu mu sitima  yomwe imachokera mdziko la Germany paulendo opita ku France.

Mtsogoleri wa dzikolo Francois Hollande ndi yemwe wapereka ulemuwu kwa anthuwa.

Pulezidenti Hollande wati zomwe anthuwa achita zapereka chitsanzo chabwino pa zakufunika kolimba mtima pantchito yolimbana ndi mchitidwe wazauchifwamba omwe ukukulirakulira mmayiko osiyanasiyana.

Iye wati ndi zachidziwikire kuti pachiwembuchi anthu ambiri akanaphedwa koma kulimba mtima kwa anthuwa kwateteza zambiri.

Malipoti akusonyeza kuti panthawiyi musitimayo munali anthu mazana asanu.Pakadali pano akuluakulu a zachitetezo mdzikolo akufunsa mafunso munthu yemwe amafuna kuchita chiwembuchi yemwe ndi  wa mdziko la Morocco.

Boma Likhazikitsa Malo a Achinyamata Ophunziliramo Ntchito ZamanjaBoma Likhazikitsa Malo a Achinyama

$
0
0

Mlangizi wa pulezidenti pankhani za mabungwe a Mavuto Bamusi atsimikizira mabungwe omwe siaboma m’boma la Zomba kuti boma likhazikitsa malo oti achinyamata aziphunziliramo ntchito za manja m’boma lililonse mdziko muno.

 

A Bamusi anena izi lachitatu m’boma la Zomba pomwe amakumana ndi akuluakulu a mabungwewa mumzindawu.

 

Iwo atsimikizira mabungwewa kuti boma lidzachita chotheka kuti ntchito yosankha achinyamata okaphunzira msukuluzi isadzalowetsedwe ndale ndi cholinga choti achinyamata ambiri oyenera kuthandizidwa adzathandizidwe.

 

Iwo ati pofuna kukwaniritsa dongosololi boma lidzakhazikitsa komiti yapadera yomwe idzakhale ikusankha anthu oyenera kulandira maphunzirowa ndipo pamapeto ake boma lidzapereka ngongole kwa achinyamatawa zoyambira bizinezi zing’onozing’ono.

 

A Bamusi apemphanso mabungwewa kuti asamathamangire kunyumba zolemba nkhani pofuna kupereka nkhawa zawo kuboma.

Mlangizi wa pulezidenti pankhani za mabungwe a Mavuto Bamusi atsimikizira mabungwe omwe siaboma m’boma la Zomba kuti boma likhazikitsa malo oti achinyamata aziphunziliramo ntchito za manja m’boma lililonse mdziko muno.

 

A Bamusi anena izi lachitatu m’boma la Zomba pomwe amakumana ndi akuluakulu a mabungwewa mumzindawu.

 

Iwo atsimikizira mabungwewa kuti boma lidzachita chotheka kuti ntchito yosankha achinyamata okaphunzira msukuluzi isadzalowetsedwe ndale ndi cholinga choti achinyamata ambiri oyenera kuthandizidwa adzathandizidwe.

 

Iwo ati pofuna kukwaniritsa dongosololi boma lidzakhazikitsa komiti yapadera yomwe idzakhale ikusankha anthu oyenera kulandira maphunzirowa ndipo pamapeto ake boma lidzapereka ngongole kwa achinyamatawa zoyambira bizinezi zing’onozing’ono.

 

A Bamusi apemphanso mabungwewa kuti asamathamangire kunyumba zolemba nkhani pofuna kupereka nkhawa zawo kuboma.

Bungwe la UN Lawopseza Dziko la South Sudan

$
0
0

Bungwe la United Nations (UN) lawopseza kuti lichitapo kanthu ngati mtsogoleri wa dziko  la South Sudan a Salva Kiir  sasayina pangano la mtendere ndi magulu omwe akuwukira dzikolo.

Pa msonkhano wa atolankhani omwe nthambi ya zachitetezo  ku bungwelilinachititsa,   m`modzi mwa akuluakulu a bungweli a Stephen O`Brien ati padakali pano, zinthu sizili bwino ku South Sudanndipo mwazina anthu akumaotchedwa m`nyumba zawo.

Pulezidenti Kiir amayenera kuti asayine pangano la mtendere ndi cholinga choti  athetse kusamvana pakati pa boma lake ndi gulu  lowukira lomwe likutsogoleredwa ndi a Riek Machar omwe anasayinira kale panganoli.

Padakali pano anthu zikwizikwi aphedwa kale pankhondoyi ndipo ena opososa 2.2 million anathawa m`nyumba zawo.

Dziko la USA Lachenjeza Dziko la South Sudan kuti Lisaphwanye Pangano

$
0
0

Dziko la United States lachenjeza  atsogoleri  a dziko la South Sudan kuti asaphwanye pangano lomwe asayinira lomwe cholinga chake ndi kuthetsa nkhondo ya pachiweniweni yomwe yakhala ikuchitika m`dzikolo.

Panganoli labwenzeretsanso a Riek Machar  pampando wawo wa wachiwiri wa Pulezidenti m`dzikolo.

Nkhondo yapachiweniweni m`dziko la South Sudan yomwe yachititsa anthu oposa 2 million kuthawa m`nyumba zawo inayambika m`chaka cha 2013 pomwe Pulezidenti wadzikolo a Salva Kiir anachotsa paudindo a Machar kamba koti amawaganizira kuti amakoza chiwembu chowapha.

Izi zinachititsa a Macharkukhazikitsa gulu la khondo lomwe limawukira boma la South Sudan.

 

Dziko la Iraq Lakhazikitsa Komiti Yodzetsa Chitetezo

$
0
0

Nduna yayikulu ya dziko la Iraq yakhazikitsa komiti yomwe izigwira ntchito yoteteza akhristu komanso madera ena omwe amayang’aniridwa ndi boma m’dzikolo.

Ndunayi    yakhazikitsa komitiyi potsatira  pempho la mtsogoleri wa maepiskopi mdzikolo Patriarch Louis Raphael Sako yemwe wapempha boma kuti liteteze akhristuwa omwe akukumana ndi nkhanza zosiyanasiyana kuchokera ku magulu a ziwembu.

Maepiskopi Mdziko la France Adzudzula Anthu omwe Atentha Mzikiti Mdzikolo

$
0
0

Bungwe la maepiskopi mdziko la France ladzudzula anthu ena omwe atentha mzikiti mtauni ina kum’mwera chakumvuma mdzikolo masiku apitawa.

Muuthenga omwe bungweli latulutsa maepiskopiwo ati zomwe achita anthuwo ndi zongofuna kudzetsa udani komanso mantha pakati pa anthu mdzikolo ndipo ati ndi wokhudzidwa kwambiri ndi chiwembucho.

Pofuna kusonyeza umodzi omwe ulipo pakati pa mipingo ndi zipembedzo mdzikolo Arkepiskopi Maurice Gardes wa dayosizi ya Auch anakayendera mzikiti omwe anthuwo atentha.

Anthu Oposera 100 Afa mu Nyanja ya Mediterranean

$
0
0

Anthu oposera 100 akuwaganizira kuti afa mdziko la Libya mabwato awiri omwe anakwera  atamila munyanja ya Mediterranean pomwe amapita mmayiko aku ulaya.

Malinga ndi akuluakulu a boma mdziko la Libya anthu mazana awiri ndi omwe apulumutsidwa koma ati akudikira kuti atsimikize zowona za nkhaniyi.

Malipoti a bungwe la United Nations ati anthu 2400 ndi omwe afa pangozi za mtunduwu chaka chino chokha pomwe amafuna kulowa mmayiko aku ulaya kudzera panyanjayi pothawa mavuto osiyanasiyana mmayiko awo.

Padakali pano anthu oposa  100 000 ati adafika kale mdziko la Italy ndipo ena oposa 160 000 adafika mdziko la Greece kuchokera mmayiko osiyanasiyana.


Bungwe la Eye of the Child ndi Lokhudzidwa ndi Imfa ya Mwana wa Zaka Zisanu

$
0
0

Bungwe la Eye of the Child lati ndi lokhudzidwa kwambiri ndi imfa ya mwana wazaka zisanu yemwe waphedwa masiku apitawa mumzinda wa Lilongwe pofuna kugwiritsa ntchito ziwalo zake ngati zizimba zokulitsira bizinezi.

 

Bungweli lati mpofunika kuti boma lichitepo kanthu pothana ndi mchitidwe waupandu omwe anthu ena kuphatikizapo madotolo a mankhwala a zitsamba akuchita mdziko muno.

 

Kudzera mchikalata chomwe bungweli latulutsa lamulungu,mkulu wa bungwe a Maxwell Matewere apempha boma kudzera mmakhonsolo a maboma onse kuti likhazikhazikitse malamulo a padera omwe aziletsa asing’ana kugwira ntchito zawo mdziko muno.

 

Iwo ati mbiri ya kuphedwa kwa ana komanso alubino, ikhudze m’Malawi aliyense  ndipo apempha magulu osiyanasiyana kuti agwirane manja ndi bungweli polimbikitsa boma kudzera kunyumba ya malamulo kuti likhazikitse malamulo kuti liwunikenso malamulo okhudza ufiti pofuna kuteteza magulu osiyanasiyana omwe akuchitiridwa nkhanza zomwe zikukolezeredwa ndi madotolo a mankhwala azitsamba.

Dziko la Egypt Lidzudzula Kazembe wa M’dziko la Britain

$
0
0

Dziko la Egypt linayitanitsa kazembe wa dziko la Britain mdzikolo John Casson, chifukwa chodzudzula bwalo la milandu mdzikolo lomwe lalamula atolankhani atatu a wailesi ya kanema ya Al-Jazeera kuti akakhale kundende kwa zaka zitatu aliyense, litawapeza olakwa pa mulandu ofalitsa nkhani yabodza.

Akuluakulu a boma anayitanitsa kazembeyo iye atanena kuti ndi okhudzidwa kwambiri ndi chigamulo chomwe bwalo la milandulo  lapereka kwa atolankhaniwo.

Boma la Egypt lati zomwe kazembeyo walankhula n’kulowera ntchito za makhothi zomwe ndi zosavomerezeka.

Anthu ambiri omwe athilirapo ndemanga pa nkhaniyi kudzera pamakina a intaneti, ati mpofunika kuti dziko la Britain lichotse ntchito kazembeyo.

Polankhula pambuyo pokumana ndi akuluakulu a bomawo, kazembeyo wati zomwe iye walankhula ndi maganizo a dziko la Britain pa mulandu wa atolankhaniwo kamba koti ena mwa atolankhani omwenso akhala akuyimbidwa mulanduwu ndi a ku Britain.

Asilikali a Dziko la South Sudan Aphwanya Pangano

$
0
0

Asilikali owukira boma mdziko la South Sudan adzudzula asilikali a boma mdzikolo chifukwa chophwanya pangano la mtendere lomwe atsogoleri ambali ziwirizi asayinira masiku apitawa asilikaliwo atakawombera mmalo omwe asilikali owukirawa akumakhala mmbali mwa mtsinje wa White Nile mdzikolo.

 

Ofalitsa nkhani za asilikali owukirawo ati asilikaliwo ayamba kuchita zamtopolazi loweruka usiku,pomwe panganolo limayembekezeka kuyamba kugwira ntchito.

 

Padakali pano boma la dzikolo komanso nthambi yowona zachitetezo silidakambepo kanthu pankhaniyi.

 

Panganoli lasayiniridwa pofuna kuthetsa nkhondo yapachiweniweni yomwe yakhala ikuchitika mdzikolo, dziko la South Sudan litasiya kukhala mbali imodzi ya dziko la Sudan.

Anthu Awiri Afa ndipo Ena 9 Avulala pa Ngozi ya Galimoto M’boma la Zomba

$
0
0

Anthu awiri afa ndipo ena asanu ndi anayi avulala minibus yomwe anakwera itagubuduzika  dalaivala wake atalephera kuwongolera m’boma la Zomba.

 

Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomali a Patricio Supriano watsimikiza za nkhaniyi.

 

Iwo ati minibus-yo yomwe ndi ya mtundu wa Toyota Hiace nambala yake ndi BS 8345 amayendetsa ndi a Willy Kapinga, ndipo yagubuduzika teyala lake litaphulika zomwe zinachititsa kuti alephere kuwongolera moyenera.

 

Anthu awiriwo amwalira pa malo pomwepo ndipo asanu ndi anayiwo akulandira thandizo ku chipatala chachikulu cha Zomba.

Anthu Khumi Afa ndi Moto Mdziko la France

$
0
0

Anthu khumi afa ndi ena anayi avulala kodetsa nkhawa ndi moto omwe unabuka mwadzidzi mu nyumba ina mu mzinda wa  Paris mdziko la France.

Malinga ndi malipoti a wayilesi ya BBC chomwe chinayambitsa motowo padakali pano sichinadziwike.

Pangoziyi anthu ena ati anakwanitsa kudathawa kudzera mmawindo ndipo motowo ati unakhudza nyumba zina khumi ndi zisanu zoyandikana ndi nyumba yomwe motowo unabuka.

Malipoti ati ngozi ya moto wa mtunduwu  nkoyamba kuchitika mdzikolo patapita nthawi yayitali.

 

 

Viewing all 1875 articles
Browse latest View live


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>