Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all 1875 articles
Browse latest View live

Papa Francisco Apereka Mwayi woti Anthu Azawone Thupi la Malemu Padre Pio

$
0
0

Likulu lampingo wakatolika lalengeza kuti thupi la malemu Pio oyera yemwe amadziwika bwino ndi dzina loti Padre Pio  adzalitulutsa mmanda kuti anthu adzakhale ndi mwai opereka ulemu kwa iye kuyambira pa 8 mpaka pa 14 February 2016.

Papa Francisco ndi yemwe waganiza zopereka mwai kwa anthu oti adzapereke ulemu wawo kwa Padre Pio ndipo pali chiyembekezo choti thupi lake lidzakhalaponso pamwambo wa phulusa wachaka cha mawa mtchalitchi lalikulu la St Peters Basilica pomwenso mpingo udzakhale ukukondwelera chaka cha chifundo cha Mulungu.

Likululi lati kupezeka kwa thupi la Pio Oyera panthawiyi chidzakhala chinthu chamtengo wapatali kwa atumiki a Mulungu pomwe adzalimbikitsidwe kudzipereka pautumiki wawo monga momwe Padre Pio adachitira.


Mwambo okondwelera kuti Ambuye Emanuel Kanyama ndi Ansembe awiri akwanitsa zaka 25 uchitika Loweruk

$
0
0

Mwambo okondwelera kuti Episkopi wa Dayosizi ya Dedza olemekezeka Ambuye Emmanuel Kanyama ndi ansembe ena awiri akwanitsa zaka 25 ali muunsembe uchitika  Loweruka pa 8 ku parishi ya St Martin De-Poris mudayosiziyo.

Ofalitsa nkhani zadayosiziyo Bambo Peter White awuza Radio Maria Malawi kuti zokonzekera zonse za mwambowu zatha.

Bambo White ayamikira magulu osiyanasiyana kuphatikizapo banki ya NBS yomwe yathandiza Dayosiziyi pokonzekera mwambowu.

“kuno ku Dedza Dayosizi pa 8 August tili ndi chaka  chokondwelera kuti ansembe atatu Bishop Emmanuel Kanyama ndi Bambo Gerald Bwebwa komanso  Bambo Grecian Kalim’mawa akwanitsa  zaka 25 ali mu unsembe ndipo zokonzekera zonse zayenda bwino kwambiri.”Bambo white anatero  

Iwo adapempha akhristu wonse kuti abwere kudzathandiza Dedza Dayosizi kuchikodwelero chimenechi.

                               

Pamwambowu adikoni atatu akuyembekezekanso kudzozedwa unsembe.

Papa Francisco Apempha Maiko Achitepo Kanthu Polimbana ndi Nkhaza.

$
0
0

Mtsogoleri wampingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco wabwerezanso kupempha maiko padziko lonse kuti achitepo kanthu polimbana ndi nkhanza zomwe akhiristu ndi magulu ena azipembedzo zing’onozing’ono  akukumana nazo m’maiko ena.

Kudzera mkalata yomwe Papa Francisco walembera Episikopi othandizira mu Dayosizi ya  Yerusalemu, mtsogoleri wampingo wakatolikayu wati akupitiliza kupemphelera anthu a mdziko la Iraq omwe akukhala  M’dziko la Jordan pothawa ziwembu zomwe magulu a zauchifwamba akumawachitira M’dzikolo.

Iye wati anthuwa akhonza kutchulidwa kuti ndi amalitiri a lero chifukwa cholimba pachikhulupiliro chawo.

Mtsogoleri wampingo wakatolikayu wanena izi pamene mlembi wamkulu wa bungwe la ma Episikopi M’dziko la Italy Arkibishopu Nunzio Galatino ali mdziko la Jordan komwe mwa zina akuyembekezeka kuyendera anthu a dziko la Iraq-lo omwe akukhala m’misasa M’dziko la Jordan-lo.

Dziko la Philippines Likhazikitsa Masiku a Tchuthi Pamene Papa Francisco akukayendera Dzikolo

$
0
0

Pamene mtsogoleri wampingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco akuyembekezeka kukacheza mdziko la Philippines mwezi wa mawa, meya wa mzinda wa Manila mdzikolo walamula kuti anthu mu mzindawo adzakhale pa tchuthi kwa masiku asanu pofuna kuti ntchito zachitetezo zidzayende bwino.

Iye wati ali ndi chiyembekezo choti tchuthichi chitha kukhala cha dziko lonse kuyambira pa 15 mpaka pa 19 January pamene Papa Francisco adzakhale atafika mdzikolo.

Panthawiyi ati sukulu zonse mumzindawo zidzatsekedwa, ndipo anthu ogwira ntchito zosiyanasiyana sadzapita kuntchito, pofunanso kuchepetsa kuthithikana kwa anthu komwe kumachitika panthawi yopita komanso kuweruka kutchito.

Iye wati boma likhonza kukonza zoti masiku omwe Papa adzakhale mdzikolo kudzakhale tchuthi mdziko lonselo kamba koti chidwi cha boma panthawiyi chili powonetsetsa kuti zochitika zonse zampingo zidzayende bwino.

A Quest for a Better and Descent Malawi”

$
0
0

 

                     

“A Quest for a Better and Descent Malawi”

The Catholic Commission for Justice and Peace Media and Advocacy Statement on the Contemporary Socio-Economic and Political Context.

10th August, 2015

 

1.0.            Preamble

We, the Secretaries of the Catholic Commission for Justice and Peace of the Episcopal Conference of Malawi comprising the National Office and Dioceses of Karonga, Mzuzu, Lilongwe, Dedza, Mangochi, Zomba, Blantyre and Chikwawa gathered at the Catholic Secretariat on 27th July, in our normal Commission’s periodic meetings to, among other things on our agenda, reflect upon our nation’s socio-economic and political context. We do as we fulfill our role  of building  a just and peaceful society that  respects the integrity of creation, the dignity of a human beings, the right to life for all, whilst taking into consideration the preferential treatment of the marginalized and the poor.

Malawi is slowly becoming a nation full of anxiety, a nation that is becoming entrenched into poverty, a nation that is slowly forgetting peace, a nation that is growing impatient and is slowly sliding into disrespecting the sanctity of human life and a nation whose citizens are gradually emerging unpatriotic to the national values and needs.

We, the CCJP Secretaries, are inspired, first, by our national duty as Malawian citizens who have the passion and the responsibility for the thriving of our country. Secondly, we are inspired and motivated by our Christian duty and calling to be good stewards of our society and to be light and salt of the world. Our message therefore, is of encouragement, hope, and peace but also of discernment to all duty bearers, citizens and all people of good will.

 

2.0.            Our Affirmations

We affirm that the following basics are highly critical in our country if, as a nation, we must attain the much needed socio-economic and political transformation needed 51 years after attaining independence:

  1. That Malawi can be a better and a happy nation for all.
  2. That in government’s striving processes to make Malawi a better place for all, its own citizens, neighboring friends, development and cooperating partners and the private sector must provide their unwavering  technical, financial, moral and intellectual support for such a noble cause.
  3. That our Government cannot attain any meaningful success on any national initiative if it does not develop a nation vision and clearly defined development agenda that it rallies around all citizens, development and cooperating partners and the private sector.
  4. That healthy, well-fed, well-educated, well-secured and free citizens loyal, obedient, united and patriotic to the ideals of their nation are very important ingredients for an effective steering of the state to the socio-economic development of the individual citizens’ lives, families and the whole nation at large.
  5. That a nation,  that is always at loggerheads, does not agree on anything, does not learn to dialogue when challenges arise,  is a nation doomed to stagnation and is a nation bound to remain in poverty no matter how many good laws or elections it may possess and conduct.

 

3.0.            Our Concerns and Worries

Having affirmed our understanding of the basics for our nation to attain socio-economic and political transformation; we, the CCJP Secretaries, seek also to highlight our painful realization that our society is not yet what we all desire. As guided by the Bishops in their 1st December 2013 Pastoral letter entitled “Strengthening The Vision of Our Destiny” in which they called upon all sectors of Malawi, CSOs, political parties, government leaders, development partners, the private sector and the general citizens to reflect upon and take positive strides to transform the current status of our development 50 years after independence We are worried and concerned that:

3.1.            Shrinking or Total Lack of Financing for Public Service Delivery     

Whilst government is trying to make sure that service delivery is adequately and timely financed, there are continued reports in many Government departments and public health facilities of low funding and supply of necessary resources to effect service delivery. For example, as a result of low or no funding at all, many district hospitals have scaled down their operations, their ambulance services grounded, their medical supplies drastically reduced to few essential drugs, provision of meals to patients reduced to only one meal per day from three. We urge relevant authorities to locate where the main problem is. If it is inefficiencies in different line ministries and departments, capacity building processes must be embarked on soon; if it is negligence from responsible officers, authorities must take drastic measures to sort out this negligence.  This is because the right to health, development and a possibility of a descent life for many Malawians are hugely getting compromised.

3.2.            Misplaced Priorities

Whilst the plight of lessened financial disbursements from many Government ministries are heightening, spending money for less important issues , a specific example being a banquet to celebrate the passing of the national budget is signal of misplaced priorities. Such bad signals in the face of growing poverty and frustrations among people continue to be a sad trend in Malawi.

3.3.            “Cooked” Government Macroeconomic Indicators

The micro-economic indicators on the ground can not in any way prove the hopeful Government macro–economic indicators. There are growing levels of poverty, desperation, hunger and shrinking public service delivery that are untimely and quality compromised.  As such, we suggest that  it is high time our leaders gave the nation the right information so that diversified strategies can be explored to improve the lives of the majority poor Malawians. The right economic indicators would also assist in seeking international collaboration for Government to have the needed capacity to fulfill its roles.

3.4.            National Insecurity

The nation is currently gripped with saddening experiences of sustained insecurity. What is more worrisome, in some instances, is that some police officers, who were supposed to be law enforcers, have joined hands with criminals terrorizing our society in an unprecedented manner. We are further worried that some communities have started taking laws into their own hands as they are torching and killing suspects due to perceived non responsiveness of our security and justice systems. We are also worried that this menace will chase and scare away prospective foreign investors whilst Government has been embarking on a serious drive to attract the much needed investors, a positive initiative for our country. We encourage a multi-sectoral approach that our Malawi Police must lead in seeking better ways of combating crime as it will not be possible for our Police to successfully combat this high level of crime alone.

3.5.            Introduction of New Systems in Public Service Delivery Institutions i.e. Road Traffic and Safety Directorate

Whilst we applaud Government for facilitating the procurement, installation and utilization of the new system at the Road Traffic offices; the bottlenecks that all people seeking road traffic services are facing are worrisome and frustrating.  We believe more could be done to sort out the problem of delays and unnecessary long queues. We think, if the software is the problem, the installers must come in faster; if the workers are not capacitated, capacity building processes should be embarked on soon and if its workers’ sabotage of the system let the authorities deal with such malpractice once and for all.

3.6.            Continued National Food Shortages and Failure to Utilize our God Given Natural Resources

We are worried that governments have come and gone with little or no political will that would seriously allow a committed financing to irrigation agriculture, which in our view, is a solid answer to our perennial food crisis. Whilst our rivers, lakes and dams are full of fresh waters, we seem to be clueless to the importance of such natural resource.  We urge the Government, development and cooperating partners including all people of good will to seriously adopt and finance irrigation farming now! Right to food is a social justice issue!

3.7.            Contemporary Donors’ Position on the Malawi Government Versus the Socio-Economic Rights of Malawian Citizens.

Whilst Government is working at strengthening its financial management and social accountability systems; we are primarily calling upon it to swiftly clean up the systems and strengthen them to stop the corrupt tendencies that have led to the loss of much needed funds for public service delivery and that have, in turn, drawn away development partners. We also encourage the Judiciary not to relent in pursuing the cashgate and other related cases. As failing to do so, is a recipe for further suffering of ordinary citizens and the failure of donor partners in providing direct budget support.

However, whilst we make such calls to government we make a kind request, to Malawi Government’s development and cooperating partners, upon getting satisfied with government reforms and accountability strengthening efforts, to resume timely direct budget support to the Malawi Government, our Government, for it to effectively deliver the much needed public services. We believe with proper social accountability initiatives, such funds will not be subject to abuse any more. We recommend that serious talks have to emerge between the Government and development and cooperating partners for sustainable development of Malawi. We believe our development and cooperating partners are in Malawi for the betterment of the rural and urban poor people of Malawi who have been heavily affected by their decision to stop budgetary support.

3.8.            Continued tensions and conflicts in Local Governance systems and structures.

We were happy that on May 20th 2014, we finally ushered in councilors to effectively make functional our local governance structures in Malawi. Sadly, few months later, we note mounting tensions, suspicions, mistrusts and conflicts among key players in Local government. We believe, if unattended to, the true meaning and relevancy of local government will be watered down and that in turn development and the ordinary citizens are the greatest losers. As such, we encourage Councilors, Members of Parliament, Council secretariat officials and traditional leaders to learn to work together whilst respecting their separate mandates and roles but also by recognizing their complementarities.

3.9.            Malawi after the May 20th  2014 Tripartite Elections

On our journey to the 2014 tripartite elections, calls for transformational leadership across all structures of leadership (Government, Political Parties, CSOs, FBOs, Religious bodies, Traditional authorities) were very strong. However, almost a year after, we note with sadness some encounters that do not reflect this critical aspiration. We sadly note the very same old ways of doing things across political parties. We note the same way of governance styles across the divide. Sadly, we still encounter dwindling spirit of patriotism, lack of commitment to honestly build a better and happy nation. Yet, as we waste this precious time to transform mother Malawi, we are cursing the present and the future generations who will live and continue to wallow in poverty. We urge the Government, Political Parties, faith and traditional leaders, CSO and FBO leaders and all people of good will to build a nation that is honest, that loves peace, that is united, that is hard working and that values life.

       3.10 Politics Versus Development

Malawians have complained more times that the campaign period during elections does not stop even if we have a ruling government in place. Regimes after regime politicians live as if they are in campaigning period. Consequently, time is wasted on politicking than on defining and implementing the nation’s development agenda by government or on providing alternative development agenda by opposition political parties. No wonder poverty is still pervasive in Malawi today. We therefore urge this administration to deal with developmental challenges Malawi is facing. We also urge political parties and people of goodwill to focus on development initiatives and leave retrogressive politics of campaigning when it’s not time for elections.

4.0.            Our Earnest Appeal

We, the CCJP Secretaries, make few critical appeals to the:

4.1.            Government:  To honestly lead Malawi through consensus building and create an enabling economic and political environment for the transformation of mother Malawi.  We further urge Government to thoroughly consult on national policies for the betterment of who those policies will serve.

4.2.            Donor Partners: To resume direct aid to our ailing mother Malawi as not to do so is slowly aiding Malawi into a deathbed. This, only upon getting satisfied with the government reforms and social accountability strengthening processes. There are serious problems currently with accountability and financial management systems, we have already urged government to swiftly improve and we are keenly monitoring the processes. We are hopeful that once beaten twice shy, together we can come up with lasting solutions to avoid a repeat.

4.3.             Political Parties’, CSOs, Media , Faith Communities’ Leaderships and the General Citizenry: To remember thatthis is our country and we have no other. Let us rediscover the vision of our fore fathers and strengthen our destiny to build a better and happy Malawi nation by being loyal, obedient, united, disciplined to the socio-economic transformation agenda of mother Malawi.  We still have time to rework our public ethics and work ethics so that Malawi can be a better place for all. It is therefore time we take positive action for mother Malawi.

 

5.0.            Conclusion

We conclude our message of encouragement, hope and discernment by quoting inspiring words contained in the pastoral letter from our Bishops “Strengthening the Vision of Our Destiny” that whilst we have just gone through our Golden Jubilee celebrations, “we as a country have a golden opportunity to re-examine our nation conscience, recover our original vision, re-define our destiny and forge ahead. Of paramount importance in this strengthening our destiny are the issues of quality leadership, citizen participation, national development agenda and national values”. We thank God for our independence and the strides so far in the democratization and emancipation project for Malawi and we realistically note that there is still a long way to go for this project to reach maturation. As such, the critical and significant roles of many stakeholders that include: state and non-state actors, local and international NGOs, political parties, the private sector, development and cooperating partners and of course the general citizenry cannot be wished away.

May God bless our leaders and bless our mother Malawi as we keep it a land of peace!  

CCJP National Office

CCJP Archdiocese of Lilongwe

CCJP Dedza

CCJP Mzuzu

CCJP Karonga

CCJP Mangochi

CCJP Zomba

CCJP Archdiocese of Blantyre

CCJP Chikwawa.

Anthu omwe Ali ndi Zilema Zosiyanasiyana Ali ndi Mwayi wa Maphunziro a Luso

$
0
0

Unduna owona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa akazi ndi amuna, ana ndi chisamaliro cha anthu olumala wapempha anthu omwe ali ndi abale omwe ali ndi zilema zosiyanasiyana kuti apite kumaofesi a mundunawu kuti akathandizidwe pandondomeko yopereka maphunziro a luso losiyanasiyana kwa anthuwa.

Nduna yowona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa akazi ndi amuna, ana ndi chisamaliro cha anthu olumala   Mayi Patricia Kaliati ndi omwe apereka pempholi polankhula ndi Radio Maria Malawi mumzinda wa Lilongwe.

Mayi Kaliati ati boma layika ndondomeko zosiyanasiyana zomwe likhale likugwiritsa ntchito mpaka mtsogolomu pofuna kuthandiza anthuwa kuti azikhala moyo odzidalira.

Pakadali pano undunawu wati ukupereka mpata oti anthu omwe ali ndi zilema zosiyanasiyana alembere chomwe angathe kuphunzira kuundunawu pasanafike pa 20 mwezi uno, kuti apatsidwe mwayi wamaphunziro pantchito yomwe akufuna.

Bwalo Lamilandu la ICC Siligwira Ntchito Mokondera

$
0
0

Mmodzi mwa akaswiri owona za malamulo komanso mkulu oweruza milandu   mdziko muno wati samagwirizana ndi maganizo a anthu omwe amadzudzula bwalo la milandu la padziko lonse la International Criminal ICC kuti limakondera mayiko a chingerezi pakagwiridwe kake ka ntchito.

Justice Dastain Mwaungulu, yemwenso  ndi mkulu oweruza milandu ku bwalo lalikulu la Appeal mu mzinda wa Blantyre ndiye wanena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi mumzinda wa Blantyre.

Justice Mwaungulu, yemwenso adagwirapo ntchito ku limodzi mwa mabwalo omwe ali pansi pa khothi la ICC mdziko la Tanzania ngati mlangizi wa milandu ya mdziko la Rwanda wati mabwalo oyimilira mayiko osiyanasiyana padziko lonse amagwira ntchito zawo mwaluntha komanso mosakondera koma vuto limakhala ndi atsogoleri a mmayiko, maka a muno mu Africa omwe amakhala ndi ulamuliro wa nkhanza ,zomwe zimachititsa kuti aziganiza molakwika pankhani zokhudza mabwalowa.

Atsogoleri ambiri a mu Africa, amadzudzula bwalo la milandu la ICC kuti limaweruza milandu ya atsogoleri a mmayiko a mu Africa okha kusiya atsogoleri a mmayiko a chingerezi  omwe adapalamulanso milandu ikuluikulu.

Papa Francisco Wakhazikitsa Tsiku la 1 September Kukhala Lopemphelera Chilengedwe

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wakhazikitsa tsiku la pa 1 September chaka chino kuti likhale lopemphelera chisamaliro cha chilengedwe.

Papa Francisco wakhazikitsa tsikuli pa msonkhano womwe anali nawo ndi akuluakulu a mabungwe a Utumiki wa Chilungamo ndi Mtendere ndi Wolimbikitsa Umodzi pakati pa akhristu mu mzinda wa Rome.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya mpingo wakatolika ku likulu la mpingowu ku Vatican, Papa wakhazikitsa tsikuli pofuna kulimbana mokwanira ndi mavuto omwe anthu akukumana nawo kamba kakuwonongeka kwa chilengedwe komwe kukudzetsa mavuto akusintha kwa nyengo.

Papa wati akhristu patsikuli akuyeneranso  kutenga gawo lalikulu pothokoza Mulungu pa chisamaliro komanso chitetezo chapadera chomwe amalandira mwa Mulungu kaamba koti nawonso ndi mbali imodzi ya chilengedwe.


Anthu 22 Asowa Mdziko la China

$
0
0

Anthu oposa makumi awiri akusowa nthaka itagumuka mdera la kumpoto chakumvuma mdziko la  China.

Malipoti a BBC ati nyumba zankhaninkhani zomwe anthu ogwira ntchito pa kampani ina ya migodi mderalo amakhala zamila mmatope omwe adza kamba ka ngoziyi yomwe yachitika lachitatu mmawa.

Pakadali pano anthu khumi ndi anayi ndi omwe apulumutsidwa pangoziyi ndipo ntchito yofufuza anthu ena omwe akhudzidwa ati ikuvutirapo kamba ka mvula ya mphamvu yomwe yakhala ikugwa mderalo.

Anthu makumi anayi ndi omwe akudziwika kuti anali m’nyumba zawo panthawi ya ngoziyi.

Anthu oposa makumi awiri akusowa nthaka itagumuka mdera la kumpoto chakumvuma mdziko la  China.

Malipoti a BBC ati nyumba zankhaninkhani zomwe anthu ogwira ntchito pa kampani ina ya migodi mderalo amakhala zamila mmatope omwe adza kamba ka ngoziyi yomwe yachitika lachitatu mmawa.

Pakadali pano anthu khumi ndi anayi ndi omwe apulumutsidwa pangoziyi ndipo ntchito yofufuza anthu ena omwe akhudzidwa ati ikuvutirapo kamba ka mvula ya mphamvu yomwe yakhala ikugwa mderalo.

Anthu makumi anayi ndi omwe akudziwika kuti anali m’nyumba zawo panthawi ya ngoziyi.

Anthu oposa makumi awiri akusowa nthaka itagumuka mdera la kumpoto chakumvuma mdziko la  China.

Malipoti a BBC ati nyumba zankhaninkhani zomwe anthu ogwira ntchito pa kampani ina ya migodi mderalo amakhala zamila mmatope omwe adza kamba ka ngoziyi yomwe yachitika lachitatu mmawa.

Pakadali pano anthu khumi ndi anayi ndi omwe apulumutsidwa pangoziyi ndipo ntchito yofufuza anthu ena omwe akhudzidwa ati ikuvutirapo kamba ka mvula ya mphamvu yomwe yakhala ikugwa mderalo.

Anthu makumi anayi ndi omwe akudziwika kuti anali m’nyumba zawo panthawi ya ngoziyi.

Mabungwe Atenge Nawo Mbali pa Nkhani ya Magetsi

$
0
0

Kupereka mwayi ku mabungwe osiyanasiyana omwe  siaboma kutenga nawo gawo pa ntchito zokhudza magetsi mdziko muno ati kungathandize kuti  mitengo yamagetsiwa ikhale yotsikirapo.

Wofalitsa nkhani ku unduna wa zamigodi mphamvu zamagetsi zachilengedwe ndi nyama zakuthengo a Josephy Kalowekamondi womwe anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi pomwe imafuna kumva zambiri pa nkhani yofuna kugawa pawiri bungwe logulitsa magetsi mdziko muno la   ESCOM kuti idzitha kukwaniritsa zofuna za anthu.

A Kalowekamoati anthu akuyenera kumvetsetsa kuti silikufuna kugulitsa bungwe la ESCOM koma kuti akufuna kuligawa kukhala nthambi ziwiri zomwe ndi yopanga magetsi  komanso yogulitsa magetsi pofuna kukweza kagwiridwe ka ntchito  ka bungweli.

Mfumu Zwelithini Ikuyembekezeka Kufika Mdziko la Zimbabwe

$
0
0

Mfumu yayikulu ya Angoni mdziko la South Africa Goodwill Zwelithini ikuyembekezeka kufika mdziko la Zimbabwe masiku akudzawa.

Magulu osiyanasiyana omenyelera ufulu wa anthu mdziko la Zimbabwe ati mfumu Zwelithini ndi yolandiridwa mdzikolo ngakhale yakhala ikudzudzulidwa kuti ndi yomwe idachititsa kuti mzika za dziko la South Africa ziyambe kuchitira nkhanza anthu a mmayiko ena omwe akukhala mdzikolo pazifukwa zosiyanasiyana kumayambiliro a chaka chino.

Padakali pano bungwe lowona za maufulu a wanthu mdzikolo la South African Human Rights Commission likupitiliza kufufuza mfumuyi  kamba ka zomwe idalankhula m’mwezi wa March chaka chino pa msonkhano omwe idachititsa mumzinda wa KwaZulu-Natal pomwe idanena kuti anthu a mmayiko ena omwe akukhala mdzikolo abwelere mmayiko awo.

Anthu asanu ndi awiri adaphedwa pa ziwawa zomwe zidabuka potsatira zomwe mfumuyo idanena.

Mfumuyi ifika mdzikolo kumapeto a mwezi uno itayitanidwa ku ukwati wa mkulu wina wazamalonda wa mdziko la Zimbabwe yemwe amagwilira ntchito zake mdziko la South Africa-lo.

Bambo Kamalo a mu Dayosizi ya Zomba Amwalira

$
0
0

Bambo Denis Kamalo omwe amatumikira  mu dayosizi ya Zomba yampingo wakatolika amwalira.

Malinga ndi mkulu wamuofesi yofalitsa nkhani za dayosiziyi Bambo Steven Likhutcha,Bambo Kamalo a mwalira lachinayi nthawi ya 10 koloko usiku kuchipatala cha Pirimiti mu mzinda wa Zomba,atadwala matenda akuthamanga kwa magazi ndi shuga.

Malinga ndi Bambo Likhutcha,malemu Bambo Kamalo adapezeka ndi matendawa m’mwezi wa April chaka chatha atadwalanso matenda owumitsa ziwalo.

Iwo anabadwa mchaka cha 1941 ndipo akhala akutumikira Mulungu ngati wansembe kwazaka makumi anai ndi mphambu zinai 44.

Mzimu wa Bambo Denis Kamalo uwuse ndi mtendere osatha.

Bungwe la UN Liwulura Mayiko Omwe Akuzunza Anthu

$
0
0

Bungwe la mgwirizano wa mayiko la United Nations UN lati liwulula  mayiko omwe akulephera kupereka zilango kwa asilikali awo omwe akukhudzidwa ndi mchitidwe ozunza anthu osalakwa mmayiko omwe bungweli lidatumiza asilikaliwa kuti akhazikitse bata.

Mlembi wamkulu wa bungweli a Ban Ki-moon ndi yemwe wanena izi lachinayi pamsonkhano omwe anali nawo ndi akuluakulu a munthambi yowona zachitetezo kubungweli ya Security Council.

A Moon anena izi pambuyo pochotsa paudindo mkulu wa asilikakali a bungweli mdziko la Central African Republic, chifukwa cha kuchuluka kwa malipoti okhudza mchitidwewu pakati pa asilikali a bungweli omwe akugwilira ntchito yawo mdzikolo.

Mayiko osiyanasiyana omwe ndi mamembala a bungwe la United Nations amatumiza asilikali awo kubungweli kuti akhazikitse bata mmayiko momwe muli nkhondo koma malipoti akusonyeza kuti ena mwa asilikaliwa amachitira anthu nkhanza zosiyanasiyana kuphatikizapo kugwililira.

Iwo ati mu lipoti lawo lapachaka lomwe akuyembekezeka kutulutsa awulula komanso kuchititsa manyazi mayiko omwe akulephera udindo wawo pankhaniyi.

Malinga ndi malamulo a bungwe la United Nations dziko limene litumiza asilikali ake kubungweli kuti akathandize kukhazikitsa bata ndipo amayenera kukhala ndi udindo ofufuza ndi kupereka zilango kwa asilikali awo omwe akukhudzidwa ndi milandu ya mtunduwu.

Bambo Kamalo Ayikidwa Mmanda

$
0
0

Mwambo oyika mmanda thupi la malemu Bambo Dennis Kamalo omwe amatumikira mudayosizi ya Zomba ngati wansembe mumpingo wakatolika wachitika lolemba ku Zomba Cathedral mu dayosiziyo.

Bambo Kamalo amwalira lachinayi pa 13 August 2015 kuchipatala cha Mission cha Pirimiti mu dayosiziyo atadwala kwa nthawi yayitali.

Iwo amwalira ndi matenda akuthamanga kwa magazi komanso Shuga atapezekanso ndi matenda owumitsa ziwalo mchaka cha 2014.

Mwambo wamaliro unayamba nthawi ya 10 koloko mmawa, ndipo mapemphero osiyanasiyana opemphelera mzimu wawo akhala akupitilira kuchokera pomwe adamwalira mpaka lamulungu.

Iwo anabadwa pa 14 September mchaka cha 1941 ndipo akhala akutumikira mpingowu ngati wansembe kwa zaka 44.

Malemu Bambo Kamalo  amkachokera m’mudzi wa Kamaru ku Parishi ya Mlombozi m’boma la Zomba.

Anthu 40 Afa ndi Bwato

$
0
0

Anthu pafupifupi makumi anayi afa bwato lomwe anakwera litamira chifukwa chonyamula  mopitilira muyeso mkatikati mwa nyanja ya Mediterranean mdziko la Libya.

Malipoti a wailesi ya BBC ati anthu oposa mazana atatu ndi omwe apulumutsidwa pa ngoziyo.

Akuluakulu a Mmayiko a kuulaya ati chiwerengero cha anthu omwe alowa mmayikowa pothawa mavuto osiyanasiyana mmayiko awo kuphatikizapo a muno mu Africa chafika poyipa kwambiri.

Malipoti a bungwe la United Nations akusonyeza kuti anthu oposa zikwi ziwiri ndi omwe afa pangozi za mtunduwu kuyambira mmwezi wa January chaka chino kufikira pano.

Malipoti ena akusonyezanso kuti anthu ogwira ntchito za chitetezo pa nyanja ya Mediterranean apulumutsanso anthu oposa mazana awiri mdera la kumvuma kwa nyanjayi mdziko la Greece.


ASisteri a Chipani cha Presentation Alimbikitsidwa mu Utumiki

$
0
0

M’bindikiro wa masiku asanu ndi atatu wa asisiteri a chipani cha Presentation for the Blessed Mary mu dayosizi ya Dedza watha lamulungu mudayosiziyo.

M’bindikirowu omwe unachitika ndi mutu oti Mayi Maria Chitsanzo Cha Atumiki A Mulungu unachitika potsatira pempho la mtsogoleri wampingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco loti chaka chino chikhale chaka cha utumiki.

Polankhula ndi Radio Maria Malawi potsekera m’bindikorowu omwe anatsogolera ndi Bambo Joseph Kimu omwenso ndi mkulu owona za mapulogalamu ku Radio Radio Maria Malawi m’modzi mwa asisiteri omwe anali nawo pa m’bindikirowu Sister Martha Mwaluka ati m’bindikirowu apindula nawo kwambiri pamene alimbikitsika muutumiki wawo.

Iwo ati aphunzira kufunika kokhala odzichepetsa pautumiki wawo,monga mayi Maria ngati mtumiki oyambilira adawonetsa pofuna kutumikira Mulungu.

Ma episkopi Mdziko la America Adzudzula Apolisi

$
0
0

Maepisikopi a mdziko la America adzudzula apolisi ku mchitidwe omawopseza anthu oganiziridwa milandu omwe akuti wakula  kwambiri  mdzikolo.

Ma episikopiwa adzudzula apolisiwo zitamveka kuti iwo akumagwiritsa ntchito njira zosavomerezeka zomwe ndikuphatikizapo kuwopseza, akafuna kupeza umboni pankhani zomwe anthu akuganiziridwa.

Iwo ati uku nkulakwa kwakukulu kamba koti anthuwo, amakhala ndi ufulu wachibadwidwe olandira chilungamo.

Iwo ati mpingo wakatolika, sumagwirizana ndi mchitidwe otere,ndipo ati palibe mfundo zomwe apolisi anganene kuti adzichita nkhanza zotere kwa anthu oganiziridwa milandu.

Makolo M’boma la Nsanje Apitiriza Kutsatira Myambo ina Yoyipa.

$
0
0

Makolo ena ku nsanje  akupitirizabe kuchita miyambo ina yoipa monga kukwatiwitsa ana akadali achichepere  komanso kuwagwiritsa ntchito zokhwima zomwe ati zikumakolezera ana ambiri kusiya sukulu. Mkulu  wa bungwe la CONCERN WORLDWIDE  Mayi Daisy Nyambi ndiwo anena izi ku Nsanje pomwe bungweli likuchita kampeni  yomemeza ana aku pulaimale, makolo komanso adindo za kufunika kwa sukulu.

Iwo ati ana akhoza kudzakhala ndi tsogolo lowala ngati makolo komanso adindo awalimbikitsa pamaphunziro komanso kuwateteza ku miyambo yoipa yosiyanasiyana. Mayi Nyambi achenjezanso anthu m`bomalo kuti kuphwanya maufulu a ana ndi mlandu ndipo anapempha anthu omwe achitiridwa  nkhaza kuti adzikanena ku polisi ndi cholinga choti anthu opalamulawo adziyimbidwa mlandu. Bunngwe la CONCERN WORLDWIDE likuyembekezeka kufikira masukulu 17 m`bomalo.

Hostel ya Atsikana Imangidwa pa Secondary ya Liwonde M’boma la Machinga.

$
0
0

Kumangidwa kwa hostel ya atsikana pa sukulu ya Secondary ya Liwonde m’boma la Machinga kuthandiza kuti atsikana ambiri ayambe kuchita bwino pa maphunziro awo.

Mphunzitsi wa mkulu pa sukuluyi a Welson Magowa ndi amene wanena izi pofotokozera mtolankhani wathu. A Magowa ati atsikana pa sukuluyi akhala akukomana ndi  mavuto osiyanasiyana kamba koti akhala akuchokera m’madera  akutali ndi sukuluyi, koma zomwe bungwe la WORLD UNIVERSITY SERVICES lachita pothandiza ndi chitukuko cha nyumba yogona atsikana pa sukuliyi zithandiza kwambiri pa ntchito zokweza maphunziro  a atsikana m’bomalo.

“Atsikana ambiri amachokera mmadela akutali, ndipo chifukwa chopanda zipangizo zowathandiza pa mayendendwe ngati njinga, zapangitsa atsikana ambiri kutenga pathupi, chifukwa chokhulupirira anthu ena omwe amaoneka ngati akuwathandiza mapeto ake nkuwapatsa mimba.”anatero a Magowa.

Sukulu ya secondary ya Liwonde m’boma la Machinga ndi imodzi mwa sukulu zaboma imene imachita bwino pa zotsatira za mayeso a Boma.

Pulezidenti Kiir Wakana Kusayinira Mgwirizano Wodzetsa Mtendere

$
0
0

Mtsogoleri wa dziko la South Sudan Salva Kiir wakana kusayinira mgwirizano odzetsa mtendere pakati pa iye ndi magulu owukira boma mdzikolo.

Pulezidenti Kiir wakana kusayinira panganoli posachedwapa mumzinda wa Addis Ababa mdziko la Ethiopia komwe anakumana ndi mtsogoleri wakumbali yowukira Rik Marshal.

Boma la South Sudan layika mfundo zoyenera kutsatidwa pa mgwirizanowu koma pulezidenti Kiir wati adzasayinira pangonoli pakatha sabata ziwiri zikudzazi.

Amkhala pakati pa zokambirana zapakati pa akuluakulu awiriwa awopseza kuti mayiko ayamba kusala dzikolo ngati atsogoleri awiriwa samvana chimodzi pomafika lolemba likudzali.

Padakali pano dziko la America lapempha pulezidenti Kiir kuti asayinire pangonoli pomwe mtsogoleri wakumbali yowukirayo wasayinira kale.

Anthu zikwizikwi aphedwa ndipo ena oposa 2 miliyoni athawa mnyumba zawo pankhondo ya pakati pa mbali ziwirizi yomwe idayamba mchaka cha 2013.

Viewing all 1875 articles
Browse latest View live


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>