Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all 1875 articles
Browse latest View live

Bungwe la MANEB Litulitsa Zotsatira za Mayeso a MSCE

$
0
0

Bungwe lowona za mayeso mdziko muno la Malawi Examination Board (MANEB latulutsa zotsatira za mayeso a Malawi School Certificate of Education MSCE.

Malinga ndi wofalitsa nkhani ku unduna wa zamaphunziro, sayansi ndi Luso a Manfred Ndovi ophunzira 75 sauzande 2 hundred 96 ndi omwe achita bwino pa mayesowa ndipo mwa ophunzira 1 hundred ndi 36 sauzande 2 hundred 96 omwe analemba mayesowa.

Iwo ati zotsatira za mayeso a chaka chino zikusiyana ndi za chaka chatha kamba koti  chaka chatha ophunzira 54 pa 100 aliwonse ndi omwe anachita bwino  ndipo chaka chino ophunzira  55 pa ophunzira 100 aliwonse ndi omwe akhonza.

‘Tilimbikitse ophunzira onse omwe panopa ali form 4 kuti alimbikire maphunziro awo ndi cholinga choti chaka chamawa kankhonzedwe kadzakhale koposera chaka chino, anatero a Ndovi.’ 

Zotsatira za mayesowa zasonyezanso kuti anyamata ambiri ndi omwe ankhoza kusiyana ndi atsikana    


Ana Aziwonetserana Chikondi Pamene Akumana

$
0
0

Episkopi wa ArchdayosiziyaLilongwe wolemekezeka AmbuyeTarcizio Ziyaye walimbikitsa ana mu mpingowu kuti azikhala okondana nthawi zonse pomwe akumana malo amodzi.

Ambuye Ziyaye anena izi ku parish  ya StFrancis mu Archdayosiziyo pomwe amachita chaka cha utumiki wa ana chimene chachitika Loweruka potsatira chaka chachikulu chimene anawa anachita lamulungu la Epifania.

Iwo ati chikondi pakati pa ana ndi chofunika kwambiri chifukwa chimathandiza kulimbikitsa umodzi wawo maka pomwe akumana malo amodzi.

Kumwambowu kunafika ana a m’ma parish onse opekeza mu Archdayosiziyi.

Boma la Chikwawa Lakhudzidwa Kwambiri ndi Ngozi za Madzi

$
0
0

Nthambi yowona za ngozi zogwa mwadzidzidzi yati boma la Chikwawa ndi lomwe lakhudzidwa kwambiri ndi ngozi ya madzi poyerekeza ndi maboma ena pamene mvula yamphamvu ikugwa mmadera ambiri mdziko muno.

Mkulu wowona ntchito za munthambiyi a James Chiusiwa,ndi yemwe wanena izi Lamulungu pomwe nthambiyi, imapereka thandizo losiyanasiyana kwa anthu omwe nyumba zawo zagwa ndi madzi osefukira mmadera a Makawa komanso Namkumba m’boma la Mangochi.

A Chiusiwa ati mabanja oposa mazana asanu ndi limodzi 600, ndi omwe akhudzidwa ndi ngoziyi pakadali pano m’boma la Chikwawa, ndipo ku Mangochi,mabanja oposa 450 ndi omwe akhudzidwa.

Bungweli lati pamene layamba kupereka thandizo kwa anthu omwe akhudzidwa mmaboma osiyanasiyana, likukonzanso zochita kawuniwuni yemwe athandize kudziwitsa anthu malo oyenera kumangapo nyumba komanso oyenera kugwiritsidwa ntchito zina maka mmaboma omwe amakhudzidwa kwambiri ndi ngozizi,pofuna kupewa ngozi za mtunduwu mtsogolo.

Polankhulapo phungu wa dera lapakati m’boma la Mangochi a Clement Chiwaya, wayamikira boma  chifukwa chopereka thandizo mwachangu kwa anthuwo omwe akuti analibe chilichonse chowathandiza pamoyo wawo pambuyo pangoziyi.

Apolisi Agwira Mzika Zina za Mdziko la DRC

$
0
0

Apolisi ku Chiponde m’boma la Mangochi, agwira mzika 34 za mdziko la Democratic Republic of Congo zomwe zimafuna kulowa mdziko la Mozambique kudzera mdziko muno mosavomerezeka.

Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Inspector Rodrick Maida,watsimikiza zankhaniyi.

Inspector Maida wati anthuwo, apezeka mderalo galimoto lina litawasiya pa malo ena mdera la mfumu yayikulu Jalasi m’bomalo.

Malinga ndi malipoti a apolisi,,mwa anthuwo asanu ndi awiri ndi akazi, ndipo atatu ndi ana.

Pakadali pano,anthuwo akuti awapereka mmanja mwa dipatimenti yowona za anthu olowa ndi otuluka mderalo kuti awathandize kubwerera kwawo ku Congo.

Likulu la Mpingo Wakatolika Lilamula Wansembe kuti Apitilize Utumiki Wake

$
0
0

Likulu la mpingo wa Katolika ku Vatican lalamula likulu la mpingowu ku Iraq, kuti ulole wansembe yemwe anachoka ku parish yake mdzikolo powopa ulamuliro wachisilamu kuti apitilize utumiki wake.

Mpingowu udayimika wansembeyo pa utumiki zitadziwika kuti wachoka chifukwa cha ulamuliro wa dzikolo.

Pakadali pano mpingowu ku Iraq walangiza ansembe onse omwe achoka mmaparish awo momwe amatumikira kuti abwelere.

Mpingowu wati ansembe akuyenera kukhala pafupi ndi akhristu awo ngakhale pa nthawi imene utumuki wawo uli pachiwopsezo chilichonse.

Wansembeyo, Bambo Noel Gorgis anachoka mdziko la Iraq kupita ku America ulamuliro wachisilamu utayamba ku Iraq ndipo akuluakulu a mpingowu ku California anapempha likulu la mpingowu kuti lilole Bambo Gorgis kupitiliza kutumikira mpingo ku America komweko.

 

 

BISHOP WATSOPANO WA DIOCESE YA ZOMBA

$
0
0

Nduna ya apapa mmaiko a Malawi ndi Zambia yalengeza kuti mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco lachinayi pa 15 October 2015 wasankha Bambo George Desmond Tambala kukhala Episkopi watsopano wa Dayosizi ya Zomba. Bambo Tambala anabadwa pa 11 November mchaka cha 1968. Maphunziro awo a Sekondale anakachitira ku Seminale ya Nankhunda kuyambira mchaka cha 1983 mpaka 1987, pambuyo pake anakachita maphunziro awo za nzeru zakuya a Philosophy m’boma la Balaka. Mchaka cha 1990 analowa  mchipani cha Carmelite ndipo anachita malumbiro  awo oyamba pa 31 July mchaka cha 1991. Atamaliza ndi maphunziro awo a unsembe ku sukulu ya ukachenjende ya Tangaza, ku Nairobi mdziko la Kenya, anadzozedwa kukhala wansembe pa 13 April mchaka  cha 1996 ku parish ya Chiphaso mu Archdiocese ya Lilongwe. Iwo anachita maphunziro a ukachenjede ku Teresa-St. John of Avila International Centre ku Spain m’chaka cha 2000 komwe adatenga  Masters Degree m’maphunziro a pamwamba za uzimu. Bambo Tambala anakhakhala wothandizira bambo Mfumu ku parish ya Kapiri mu Archdiocese ya Lilongwe (1996-1998), Woyang’anira ma Postulanti ku International Congregation Institute ICI ku Balaka, mphunzitsi  wa za uzimu ku Balaka komweko, (2000-2002), Woyang’anira ansembe a chipani cha Carmelite ku Malawi (2002-2008), Mkulu wa nyumba ya mapemphero ku Nyungwi ku Archdiocese ya Blantyre, ndipo kuyambira mchaka 2009 mpaka pano akhala akutumikira ku likulu la chipani chawo ku Roma monga woyimirira ansembe mu Africa ndi Madagascar. Iwo amalankhula zilankhulo izi: Chingerezi, Chichewa, Chyao, Chiswahili, Chitaliyana, Chispanish ndi chi faransa. Ambuye Thomas Luke Msusa omwe akhala akuyendetsa ntchito za dayosizi ya Zomba akhala akupitiliza mpaka  episkopi watsopanoyu adzakhazikitsidwe.

Akhristu Ali ndi Udindo Wofalitsa Uthenga Wabwino

$
0
0

Akhristu ati ali ndi udindo wolalika uthenga wabwino kudzera mu sacramenti la ubatizo lomwe analandira.

 

Bambo Tony Mfune ndi omwe amankhula izi  pambuyo pa mwambo wa nsembe ya misa  womwe unachitikira ku parishi ya St Tereza Nkhamenya mudayosizi ya Mzuzu pomwe lamulungu mpingo wakatolika umachita chaka cha chibalalitso cha mpingo.

 

Iwo ati  ubatizo ndi sacramenti lokhalo lomwe limatsogolera akhristu pa kufalitsa uthenga wabwino.

 

“Sacramenti la ubatizo lomwe mkhristu amalandira limapereka uthenga woyamba  kuti ali ndi udindo wofalitsa uthenga wa Mulungu,”anatero Bambo Mfune.

 

Iwo anati “akhristu ali ndi udindo wopemphera akhristu anzawo omwe akukumana ndi mavuto osiyanasiyana.”

 

Pamenepa iwo ati ndalama zomwe apereka akhristu pa tsikuli zithandiza pa ntchito ya kufalitsa uthenga mmadera osiyanasiyana.

 

“Ndalama zomwe akhristuwa apereka zithandiza anzawo kuti alandire mawu aMulungu kamba koti ntchitoyi imafunika ndalama,”anatero Bambo Mfune.

Akhristu ati ali ndi udindo wolalika uthenga wabwino kudzera mu sacramenti la ubatizo lomwe analandira.

 

Bambo Tony Mfune ndi omwe amankhula izi  pambuyo pa mwambo wa nsembe ya misa  womwe unachitikira ku parishi ya St Tereza Nkhamenya mudayosizi ya Mzuzu pomwe lamulungu mpingo wakatolika umachita chaka cha chibalalitso cha mpingo.

 

Iwo ati  ubatizo ndi sacramenti lokhalo lomwe limatsogolera akhristu pa kufalitsa uthenga wabwino.

 

“Sacramenti la ubatizo lomwe mkhristu amalandira limapereka uthenga woyamba  kuti ali ndi udindo wofalitsa uthenga wa Mulungu,”anatero Bambo Mfune.

 

Iwo anati “akhristu ali ndi udindo wopemphera akhristu anzawo omwe akukumana ndi mavuto osiyanasiyana.”

 

Pamenepa iwo ati ndalama zomwe apereka akhristu pa tsikuli zithandiza pa ntchito ya kufalitsa uthenga mmadera osiyanasiyana.

 

“Ndalama zomwe akhristuwa apereka zithandiza anzawo kuti alandire mawu aMulungu kamba koti ntchitoyi imafunika ndalama,”anatero Bambo Mfune.

Katundu ndi Nyumba za Anthu 10 Sauzande Zawonongeka Mdziko la Philippines

$
0
0

Anthu oposa 10 sauzande akusowa pokhala mumzinda wa Luzon kumpoto kwa dziko la   Philippines kamba ka mvula ya mphepo  yomwe  yawononga nyumba  ndi katundu osiyanasiyana .

                                            

Malinga ndi malipoti a wayilesi ya BBC nyumba zambiri zagwa ndipo mitengo yatchinga misewu ikuluikulu mtawunimo.

 

Akastwiri  a sayansi ya mvula ati mphepoyi  ikuyembezeka kutha sabata ikubwelayi zomwe zikupereka chiwopsezo chakuti mumzindawu  mukhala madzi osefukila ambiri .

 

Padakali pano asilikali a dzikolo ali pakalikiliki wopulumutsa anthu ndipo maulendo apandege komanso pa bus aletsedwa.

 

Mu chaka cha 2013 anthu okwana 6,300 adafa kamba ka mvula ya mphepo m`dzikolo.

Anthu oposa 10 sauzande akusowa pokhala mumzinda wa Luzon kumpoto kwa dziko la   Philippines kamba ka mvula ya mphepo  yomwe  yawononga nyumba  ndi katundu osiyanasiyana .

                                            

Malinga ndi malipoti a wayilesi ya BBC nyumba zambiri zagwa ndipo mitengo yatchinga misewu ikuluikulu mtawunimo.

 

Akastwiri  a sayansi ya mvula ati mphepoyi  ikuyembezeka kutha sabata ikubwelayi zomwe zikupereka chiwopsezo chakuti mumzindawu  mukhala madzi osefukila ambiri .

 

Padakali pano asilikali a dzikolo ali pakalikiliki wopulumutsa anthu ndipo maulendo apandege komanso pa bus aletsedwa.

 

Mu chaka cha 2013 anthu okwana 6,300 adafa kamba ka mvula ya mphepo m`dzikolo.


Likulu la Mpingo Wakatolika Lilengeza Dongosolo la Maulendo a Papa ku Africa

$
0
0

Likulu la mpingo wakatolika mumzinda wa Vatican lalengeza ndondomeko ya ulendo wa mtsogoleri wa mpingo wakatolika padziko lonse lapansi  Papa Francisko wodzacheza m`mayiko ena a muno mu Africa.

Papa Francisco akuyembekezeka kukacheza m`maiko a Kenya, Uganda komanso Central African Republic kuyambira pa 25 mpaka pa 30 November chaka chino.

Muulendo wake mwazina Papayu akuyembekezeka kuchititsa miyambo ya ukaristia kukayendera pomwe  Amalitiri aku Uganda anaphedwera ndi zina.

Papa Francisko  akafikanso  m`dziko la Central Africa Republic  ngakhale kuti m`dzikolo mwabuka zipolowe ndipo zipembedzo zikugwirila ntchito limodzi poonetsetsa kuti mdzikolo muli bata ndi mtendere kamba koti Papayu akayenderanso anthu azipembedzo zina kuphatikizapo chisilamu komanso anthu othawa kwawo.

Matenda a Mmimba Akusokoneza Ntchito za Umoyo M’boma la Zomba

$
0
0

Ofesi yowona ntchito za umoyo m’boma la Zomba yati matenda a kolera ndi otsekula mmimba ndi awiri mwa matenda asanu omwe amasokoneza kwambiri ntchito za umoyo m’bomali.

Mkulu wa muofesi yowona kapewedwe ka matenda m’bomali a Innocent Mvula ndi omwe anena izi polankhula ndi mtolankhani wathu wapadera m’bomalo pamene dziko lino sabata yatha inagwirizana ndi mayiko padziko lonse pokumbukira ndondomeko yosamba mmanja moyenera ngati njira imodzi yochepetsera kufala kwa matendawa.

A Mvula ati kupyolera mundondomeko zaumoyo zomwe zidakhazikitsidwa mchaka cha 2011, ofesi yawo yakhala ikudzipereka kwathunthu powonetsetsa kuti pali zipangizo zoyenera kulimbana ndi matendawa.

Iwo ati zina mwa zifukwa zomwe zikukolezera matendawa ndi kupezeka kwa Nyanja ya Chilwa  yomwe imachititsa kuti anthu azipezeka  ndi matendawa ngakhale munyengo yomwe siyamvula. 

Pamenepa Iwo apempha anthu m’bomali kuti aziwonetsetsa kuti akutsatira njira zoyenera zaukhondo kuti azikhala ndi umoyo wabwino nthawi zonse.

Papa Francisco Alangiza Akhristu kuti Akhale Ofalitsa Uthenga

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco,walangiza a khristu a mpingowu mdziko la Philippines kuti adzikhala a kazembe a Yesu Khristu pofalitsa uthenga wa Mulungu ndi chikondi chake.

Mu uthenga wake opita kwa akulu akulu a mpingowu komanso a semino, Papa wati anthu mdziko la Philippines akuyenera kuthetsa zimene zimawalekanitsa, kamba koti izi zimatsutsana kotheratu ndi chiphunzitso cha Yesu Khristu mwini.

Episkopi wa Dayosizi ya Mzuzu Wamwalira

$
0
0

Bungwe la ma Episkopi a mpingo wa katolika mdziko muno  la Episcopal Conference of Malawi (ECM)  likudziwitsa za imfa ya Olemekezeka Ambuye Joseph Mukasa Zuza amene anali Episkopi wa dayosizi ya Mzuzu komanso wapampando wa bungwe la ma Episkopi a katolika m’Malawi (ECM).

Malinga ndi uthenga umene talandira, Ambuye Zuza anachita ngozi ya galimoto ndipo amwalira pamene anali kulandira chithandizo kuchipatala cha St John ku Mzuzu.

Padakali pano dongosolo la mwambo wa maliro silidadziwike.

Mzimu wa Ambuye Joseph Mukasa Zuza uuse mu mtendere wosatha.

Mabungwe omwe si Aboma Achita Ziwonetsero

$
0
0

Ziwonetsero zofuna kukakamiza mabungwe omwe analandira thandizo la ndalama  kuchokera ku bungwe lowona za matenda a Edzi mdziko muno la National Aids Commission  NAC kuti abweze ndalamazi zachitika lachiwiri mmizinda yonse mdziko muno.

Paziwonetserozi mabungwe omenyerera Ufulu wa anthu mdziko muno,apereka chikalata chamadandaulo awo pa nkhaniyi.

Kudzera mchikalatachi,mabungwewa awopseza kuti ngati mabungwe omwe analandira thandizoli kuchokera kubungwe la NAC sabweza ndalamazi pasanathe masiku 100, achita zinthu zomwe chikalatacho sichidanene.

 

 

Anthu 153 Afa ndi Mvula Yamphamvu Mboma la Nsanje

$
0
0

Lipoti lomwe khonsola ya boma la Nsanje latulutsa, lati pafupifupi anthu 153 afa kuyambira pomwe mvula ya mphamvu yayamba mmadera ambiri mdziko muno.

Bwanamkubwa wa bomalo a Harry Phiri,anena izi lachinayi polankhula ndi mtolankhani wathu wapadera m’bomalo.

Iwo ati chiwerengerochi chadziwika nthambi yowona za ngozi zogwa mwadzidzi m’bomalo motsogozedwa ndi othandizira ntchito za nthambiyo a Hamphrey Magalasi, itafufuza midzi yomwe yakhudzidwa ndi ngoziyi,pomwe yapeza kuti anthu a  mmabanja ena akusowa.

Madera a mafumu omwe akhudzidwa kwambiri ndi ngoziyi ndi kwa mfumu yayikulu Mbenje, Mlolo komanso Nyachikadza.

Malinga ndi a Phiri boma lapereka kale ndege ziwiri za mtundu wa helikopita komanso boti imodzi yothandizira kupulumutsa anthu omwe azunguliridwa ndi madzi mmadera a mafumuwo.

Pamenepa iwo ati anthu m’bomalo akusowa chakudya, matenti, madzi, mankhwala ndi zina zambiri.

Ngakhale izi zili chonchi a Phiri ati anthu ena mmadera omwe akhudzidwa,akukana kuwasamutsira mmadera okwera.

Pakadali pano phungu wadera la kumpoto m’boma la Nsanje a Esther Mcheka Chilenje Nkhoma komanso  phungu wadera lapakati a Francis Kasaila ali limodzi ndi anthuwo.

Pali chiwopsezo choti chiwerengero cha anthu omwe afa pangoziyi chitha kukwera.

Papa Francisco Ayendera Dziko la Phillipines

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco, wafika mdziko la Phillipines paulendo wake wa masiku asanu ndi limodzi oyendera mayiko aku Asia. Pakadali pano akhristu a mpingowu ndi ena akupitiliza kufika mu mzinda wa Manila komwe Papa atsogolere zochitika zosiyanasiyana. Polankhula pa mapemphero a mthenga wa m’njelo kwa mai Maria dzulo mdziko la Sri-Lanka,Papa Francisco wapempha anthu mdzikolo kuti ayanjane maka mitundu yomwe yakhala ili pankhondo. Iye wati mtima okhululuka,umayambira pomwe munthu wayamba wavomereza kulakwa kwake pachinthu chilichochonse chomwe chadzetsa kusamvana. Iye walangiza anthuwo kuti atengere moyo okhululuka ngati wa mai Maria,omwe adawonetsa pokhululukira anthu omwe adapha mwana wawo Yesu Khristu pomupachika pa mtanda.


Bambo Masauko Amwalira

$
0
0

Mwambo woyika m`manda thupi la malemu  Bambo Edward Masauko uchitika lolemba ku Limbe Cathedral mu ark dayosizi ya Blantyre.

Malinga ndi chikalata chomwe bungwe la ma episkopi la Episcopal Conference of Malawi ECM latulutsa mwambo wa nsembe ya misa yotsanzikana ndi Bambowa udzayamba nthawi ya 10 koloko m`mawa.

Bambo Masauko amwalira lachisanu ku chipatala cha Mwaiwathu mumzinda wa Blantyre atadwala kwa nthawi yochepa.

Iwo anabadwa pa 1 March 1960 ndipo anadzozedwa unsembe pa 21 July 1985.

Iwo amwalira atatumikira kwa zaka makumi atatu.

Makolo Akhale Patsogolo Kusula Asemino

$
0
0

Dayosizi ya Mangochi ya mpingo wakatolika yati makolo akuyenera kukhala ndi chidwi chosula anyamata omwe ali ku seminale zazikulu zosulira ansembe. Episkopi wa dayosiziyi Ambuye Montfort Sitima ndi omwe alankhula izi m’boma la Mangochi pa msonkhano wa makolo omwe ali ndi anyamata mseminalezi. Ambuye Sitima ati iyi ndi njira imodzi yowalimbikitsa anyamatawa pa chiyitanidwe chawo kamba koti ambiri amalephera kugwiritsa ntchito zomwe aphunzira ku sukulu akapita kukaphunzira moyo wa mmaparishi. “Ansembe ena amalephera kukwaniritsa zimene aphunzira ku seminale chifukwa cha zovuta zimene akukumana akapita kukatumikira mmaparishi osiyanasiyana,”anatero Ambuye Sitima. Ambuye Sitima anati pamene akumana ndi makolo a anyamatawa ali ndi chikhulupiliro kuti ayamba kuyendera limodzi pofuna kuthandiza ansembe a mawawa. Polankhulapo mkulu woona za chiyitanidwe mu dayosiziyi Bambo Christopher Sichinga ati pakuyenera kukhala mgwirizano wabwino pakati pa iwo ndi makolo a anyamatawa ndi cholinga choti anyamatawa athandizike moyenera. “Tikufuna kuti makolo atengepo gawo pa chisankho chomwe ana awo anasankha kuti anyamatawa azitha kumvetsa bwino cholinga cha utumiki womwe anasankha,” anatero Bambo Sichinga. Dayosizi ya Mangochi ili ndi asemino 18 omwe akuphunzira ku seminale zazikulu za Kachebere ku Mchinji ndi St Peters ku Zomba.

Anthu Oposa 42 Afa ndipo Ena Zana Limodzi Avulala Mdziko la Nigeria

$
0
0

Anthu oposa 42 ati afa ndipo ena oposa zana limodzi avulala anthu ena ataphulitsa mabomba awiri m`malo osiyanasiyana  m`dziko la Nigeria.

Bomba loyamba ati linaphurika pa mzikiti wina omwe angowutsekura kumene, anthu akuchita mapemphero a m`mawa m`dera la Yola ndipo lina linaphulika munzinda wa Maiduguri.

Padakali pano yemwe wachita chiwembuchi sakudziwika  koma gulu la zauchifwamba la Boko Haram lakhala likuchita ziwembu zamtunduwu   m`deralo.

Gulu la Boko Haram lakhala likuchita zamtopola zosiyasiyana ndi kwa akhristu komanso asilamu omwe amatsutsana ndi zikhulupiliro za gululo.

Anthu zikwizwikwi akhala akuphedwa ndipo ambiri anathawa m`nyumba zawo  kamba ka zamtopola zomwe gululi lakhala likuchita pofuna kukhazikitsa boma la ulamuliro wa chisilamu.

Chiwerengero cha Anthu Odwala Matenda Opatsirana Pogonana ndi Chokwera M’boma la Mangochi

$
0
0

Boma la Mangochi ati ndi limodzi mwa maboma omwe ali ndi chiwerengero chokwera cha anthu odwala matenda opatsirana kudzera pogonana.

 

Dokotala wamkulu pa chipatala cha Banja la M’tsogolo m’bomalo a Lucius Kozomba ndi omwe anena izi pa maphunziro a ogwira ntchito za umoyo m’bomalo.

 

A Kozomba ati chiwerengerochi ndi chokwera kamba koti azachipatala akukhala ndi chidwi pothandiza anthuwa , m’malo moti aziperekanso uphungu oyenera kwa odwalawo.

 

Iwo  atinso odwala ambiri amakana kubwera kudzalandira thandizo la  mankhwala ndi okondeka awo kamba kamanyazi ndi mantha, zomwe ati ndi zina mwa zomwe zikukolezera kufala kwa matenda odza kamba kogonana m’bomalo.

Boma la Mangochi ati ndi limodzi mwa maboma omwe ali ndi chiwerengero chokwera cha anthu odwala matenda opatsirana kudzera pogonana.

 

Dokotala wamkulu pa chipatala cha Banja la M’tsogolo m’bomalo a Lucius Kozomba ndi omwe anena izi pa maphunziro a ogwira ntchito za umoyo m’bomalo.

 

A Kozomba ati chiwerengerochi ndi chokwera kamba koti azachipatala akukhala ndi chidwi pothandiza anthuwa , m’malo moti aziperekanso uphungu oyenera kwa odwalawo.

 

Iwo  atinso odwala ambiri amakana kubwera kudzalandira thandizo la  mankhwala ndi okondeka awo kamba kamanyazi ndi mantha, zomwe ati ndi zina mwa zomwe zikukolezera kufala kwa matenda odza kamba kogonana m’bomalo.

Papa Francisco Asonkhanitsa Anthu Oposa 6 Miliyoni mu Mzinda wa Manila

$
0
0

Malipoti ochokera mdziko la Phillipines ati anthu oposa 6 miliyoni ndi omwe adali nawo pa mwambo wa nsembe ya ukalistia yomwe mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco anatsogolera mu mzinda wa Manila Lamulungu lapitali.

Wofalitsa nkhani ku likulu la mpingowu ku Vatican Bambo Federico Lombardi ati aka ndi koyamba kuti anthu ochuluka chotere asonkhane pa mwambo wa nsembe ya ukalistia  yotsogoleredwa ndi Papa mu mbiri ya mpingowu.

Mu ulaliki wake Papa Francisco anabwerezanso kutsindika zakufunika kwa banja ku dziko komanso mpingo.

Malinga ndi malipoti uthengawu wakhudza kwambiri anthu m`dzikolo, pamene boma langokhazikitsa kumene malamulo okhudza kulera omwe akulukaulu a mipingo sakugwirizana nawo.

Papa Franciscowati ndi zomvetsa chisoni powona kuti masiku ano, mabanja sakutetezedwa ku zoyipa zosiyanasiyana, zomwe zina mwa izo zikulimbikitsidwa mmapulogalamu a boma kuphatikizapo okhudza kulera.

 

Viewing all 1875 articles
Browse latest View live


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>