Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all 1875 articles
Browse latest View live

Papa Francisco Akacheza Mdziko la America M’mwezi wa September

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wa Katolika pa dziko lonse Papa Francisco watsimikiza za ulendo wake wokacheza mdziko la America m’mwezi wa September chaka chino.

Polankhula kwa atolankhani omwe anali nawo paulendo wobwelera ku Rome, atatha kuyendera mayiko aku Asia kwa masiku asanu ndi limodzi, Papa Francisco anawuza atolankhaniwo kuti paulendo waku America, sadzayima mdziko la Mexico monga anthu ena akufalitsira,kamba koti adzakhala ndi zochita zambiri mdziko la America.

Paulendowu, mtsogoleri wa mpingo wa Katolikayu adzayendera maofesi a bungwe la mgwirizano wa mayiko  a United Nations ku likulu lake ku New York komanso Washington.

Papa Francisco anatsimikiza kale kuti paulendo womwewu, adzakhala nawonso pa msonkhano wa mabanja womwe udzachitikire mu mzinda wa Philadelphia mdziko lomwelo la America.

Pakadali pano likulu la mpingowu silidatsimikize ntchito zina zomwe Papa Francisco adzagwire akadzafika mdzikolo.


Papa Wapereka Uthenga wa Chipepeso Mmayiko a Afghanistan ndi Pakistan

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapereka uthenga wachipepeso kwa anthu omwe akhudzidwa ndi ngozi ya chivomerezi  mmayiko a Afghanistan ndi Pakistan.

Mu uthenga womwe Papa watumiza kudzera kwa nthumwi yake mdziko la Pakistan wati iye ndi wokhudzidwa ndi imfa, kuvulala komanso kusowa kwa anthu zomwe zadza kamba ka ngoziyi.

Malipoti a wailesi ya Vatican ati iye ali nawo limodzi anthu omwe akhudzidwa pa ngoziyi kudzera mmapemphero. Ngozi ya chivomereziyi inachitika lolemba ndipo inapha anthu pafupifupi 400.

Umbuli pa Matenda a Cancer Ukuphetsa Anthu

$
0
0

Kusadziwa komanso ulesi opita kuchipatala kukayezetsa nthenda ya Cancer ndi zina mwanjira zomwe zikupititsa patsogolo chiwerengero cha anthu odwala matendawa  m'dziko muno. 

 

M'modzi mwa madotolo akuluakulu a zachipatala Dr Getrude Sambakunsi ndi omwe anena izi mu mzinda wa Blantyre pofotokozera mtolankhani wathu yemwe amafuna kudziwa zina mwa njira zomwe zikuchititsa kuti nthenda ya Cancer izitenga miyoyo ya anthu yochuluka masiku ano.

Dr Sambakunsi ati ndi zomvetsa chisoni kuti kufikira pano anthu ochuluka sadziwa zambiri zokhudza matendawa komanso alibe chidwi chofuna kudziwa momwe thupi lawo likugwilira ntchito.

Pamenepa Dr Samvakunsi ati nthendayi imavuta kwambiri ikazindikiridwa mochedwa.

Iwo apempha a Malawi kuti ngati njira imodzi yothanira ndi nthendayi, anthu akuyenera kumaonana ndi madotolo pafupipafupi makamaka ngati awona zizindikiro zina zodabwitsa pathupi lawo.

Chiwerengero cha Achinyamata Omwa ma ARV Chakwera M’boma la Mangochi

$
0
0

Chiwerengero cha achinyamata omwe amalandira mankhwala otalikitsa moyo a ARV ati chikukwera m’boma la Mangochi.

Mkulu oyang’anira anthu omwe amamwa mankhwalawa pa chipatala chachikulu cha Mangochi a Mike Nyirenda  ndi omwe anena izi pa msonkhano womwe bungwe la Malawi Interfaith linakonzera akuluakulu a mipingo yosiyanasiyana m’boma la Mangochi ndi cholinga choti adziwe momwe ntchito yogawira mankhwala otalikitsa moyo kwa achinyamata ikuyendera m’bomali.

Iwo ati chiwerengero cha achinyamata olandira makhwalawa pa chipatalachi chikupitilira kukwera chikhazikitsireni zipatala za Teen Clinic zomwe zimatsekulidwa kamodzi pa mwezi ndi cholinga chofuna kupereka mpata kwa achinyamatawa kuti azifotokoza mavuto omwe akukumana nawo pa nthawi yomwe akumwa mankhwalawa.

Pamenepa iwo ati  achinyamatawa akumakumananso ndi mavuto osiyanasiyana monga kusowa uphungu pa makhwala otalikitsa moyowa  komanso kusalidwa ndi anthu omwe amawayang’anira ndipo apempha atsogoleri a mipingowa kuti akhale patsogolo pothetsa mchitidwe wosalana.

A Nyirenda anatinso ndi okhudzidwa kamba kakuchepa kwa chiwerengero cha abambo omwe amakayezetsa magazi ndipo anayamikira amayi a m’bomali kaamba koti nthawi zonse amakhala patsogolo kukayezetsa magazi kuti adziwe momwe mthupi mwao mulili.

Bungwe la AU Lakhazikitsa Kafukufuku wa Maufulu Ophwanyidwa Mdziko la Burundi

$
0
0

Bungwe la United Nations lati likugwirizana ndi mfundo  yomwe bungwe la African Union lakhazikitsa, lochita kafukufuku wa maufulu a anthu omwe akhala akuphwanyidwa mdziko la Burundi.

Bungweli ati ndi lokhudzidwa ndi kupitlira kwa zamtopola zomwe zakhala zikuchitika mdzikolo kuyambira pomwe mtsogoleri wa dzikolo Pierre Nkurunziza analengeza kuti apikisana nawo kachitatu pa chisankho cha Pulezidenti chomwe chinachitika mdzikolo.

Malipoti a nyuzi 24 ati bungweli lalonjeza kuti lichitapo kanthu pa zipolowe zomwe zikuchitika mdzikolo.

Bungweli lalonjezanso kuti liletsa mayendedwe a anthu komanso kutseka zitupa za anthu onse omwe akuthandizira pa zamtopolazi.

Anthu pafupifupi 200 anaphedwa ndipo ena 200 sauzande anathawa mdzikolo kamba ka mchitidwewu.

Achiwembu Mdziko la Niger Apha Anthu ndi Kutentha Matchalitchi ndi Nyumba za Ansembe ndi Asisiteri

$
0
0

Malipoti ochokera mdziko la Niger ati anthu khumi aphedwa, ndipo maparishi ochuluka komanso nyumba za ansembe ndi asisiteri, zatenthedwa mdziko la Niger pa chiwembu chomwe anthu omwe sakudziwika achita kumathero a sabata yatha.

Malipotiwo ati mu mzinda wa Niamey womwe ndi likulu la dzikolo, mwambo wa nsembe ya ukaristia anawulepheretsa, maparishi asanu ndi imodzi atatenthedwa pa ziwembuzo.

Pakadali pano, akhristu 285 mu mzindawo, athawira ku malo a asilikali.

Malipoti a boma ati matchalitchi makumi anayi ndi asanu, ndi omwe atenthedwa pa ziwembuzo.

Mdziko la Niger,muli anthu 17.1 miliyoni omwe 80 pa 100 aliwonse, ndi asilamu, ndipo akhristu alipo ochepa kwambiri.

Anthu akuganizira kuti ziwembuzo, zachitika pokwiya ndi chithunzi chonyoza mneneri Muhamad wa chipembedzo chachisilamu, chomwe nyuzipepala ina mdziko la France, inatsindikiza masiku apitawa,zomwe zidachititsa chiwembu china mdzikolo.

Anthu 17, anaphedwa pa chiwembucho.

 

Bank ya Standard Imanga Midada Yophunziliramo M’boma la Chiradzulu

$
0
0

Boma ati likuyenera kumanga makalasi okwana 38 sauzande kuti likwaniritse kupereka maphunziro apamwamba m`dziko muno.

Mlembi wamkulu wa mu unduna wa zamaphunziro sayansi ndi luso Mayi Lonely Magareta ndi omwe anena izi pamwambo womwe bank ya standard imapereka midadada iwiri ya makalasi ya ndalama zokwana 33 million kwacha  pa pulayimale ya Mkuyu kwa mfumu yaikulu Onga m`boma la Chiradzulu.

Iwo ati ndi zokhumudwitsa kuti padakali pano ophunzira ena akadaphunzilirabe pansi pamitengo kamba kosowa zipinda zophunziliramo ndipo ati vutoli likudza kamba ka kuchuluka kwa ana.

Mayi Magareta apemphanso makampani ena kuti atengere chitsanzo chomwe bankiyi yachita.

Mkulu wa Bank ya Standard DR Rex Harawa ati bankiyi yamanga zipinda zophunziliramozi ngati njira imodzi yobwenzera kwa anthu lina mwa phindu lomwe amapeza.

Papa Francisco Alimbikitsa Ansembe Kuthandiza Akhristu pa Mavuto

$
0
0

M’tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse PapaFrancisco walimbikitsa ansembe mu mpingowu kuti azikhala okhudzidwa ndi kuthandiza pa mavuto omwe akhristu akukumana nawo.

Papa wati ansembe akuyenera kuwonetsa zitsanzo zabwino kamba koti mulungu anawapatula kuti akhale abusa oweta nkhosa zake  osati akapitawo , kapena kuti akulu a oweluza milandu, choncho zochita zawo zikuyenera kusonyezadi mtima wa chikondi pakati pa omwe amawatumikira.

Papa Francisco anapeleka uthengawu lachisanu, pomwe amachititsa nsembe ya ukaristia pa tchalichi lina ku likulu la mpingowu ku Vatican.

Iye anadzudzula ansembe omwe samawonetsa chidwi chotenga nawo mbali pa ntchito zosiyanasiyana zochitika mu mpingowu.

Pambombowu panachitikanso chaka chokondwelera kuti Cardinal Javier Lozano Barragan wakwanitsa zaka 60 akutumikira Mulungu ngati wansembe mu mpingo wakatolika .


Dziko la Germany Litseka Zipata Zake ndi Dziko la Australia

$
0
0

Dziko la Germany lati litseka zina mwa zipata zake ndi dziko la Australia pofuna kuchepetsa anthu othawa kwawo omwe akulowa m`dzikolo kudzera mdziko la Australia lo.

Akuluakulu a dziko la Germany ati akudandaula kamba kosowa mgwirizano pakati pa mayiko awiriwa zomwe zikuchititsa kuti dziko la Germany lilephere kuthandiza mokwanira anthu omwe akulowa m`dzikolo.

Pakadali pano anthu othawa kwawo akulowanso m`dziko la Germany kudzera m`dziko la Greece ngakhale kuti kuli nyengo yozizira.

Malinga ndi malipoti awailesi ya BBC anthu  makumi awiri  omwe ambiri ndi ana afa boti lomwe anakwera litamira m`dziko la Greece pomwe amafuna kuwoloka paulendo wawo wa m`maiko akuulaya.

Dziko la Germany lati litseka zina mwa zipata zake ndi dziko la Australia pofuna kuchepetsa anthu othawa kwawo omwe akulowa m`dzikolo kudzera mdziko la Australia lo.

Akuluakulu a dziko la Germany ati akudandaula kamba kosowa mgwirizano pakati pa mayiko awiriwa zomwe zikuchititsa kuti dziko la Germany lilephere kuthandiza mokwanira anthu omwe akulowa m`dzikolo.

Pakadali pano anthu othawa kwawo akulowanso m`dziko la Germany kudzera m`dziko la Greece ngakhale kuti kuli nyengo yozizira.

Malinga ndi malipoti awailesi ya BBC anthu  makumi awiri  omwe ambiri ndi ana afa boti lomwe anakwera litamira m`dziko la Greece pomwe amafuna kuwoloka paulendo wawo wa m`maiko akuulaya.v

Mnyamata wa Zaka 27 Amupeza Wolakwa pa Mlandu Wogwilira

$
0
0

Bwalo loyamba la milandu m’boma la Ntchisi lagamula sing’anga wina wa zaka 27 zakubadwa kuti akakhale  ku ndende kwa zaka khumi ndi kukagwira ntchito ya kalavula gaga kamba kopezeka olakwa pa mulandu wogwilira mayi wa zaka 35 zakubadwa.

 

Wapolisi wofalitsa nkhani m’bomalo Sergent Gladson M’bumpha watsimikiza za nkhaniyi.

Iwo ati Sing’angayo yemwe amadziwika ndi dzina loti Willard Jabesi Njovu anapalamula mlanduwu pa 16 mmwezi wa September, pomwe mayiyo  Emlida Mwale anapita kwa sing’angayo kukafuna thandizo la mankhwala kamba  kosowa mphatso ya mwana m’banja mwawo.

“Mayiyu atapita kwa singangayo anamuwuza kuti avule zovala kuphatikizapo chovala cha mkati, ndipo anamuza kuti agone ndi cholinga choti amuwunike, pambuyo pake ndi pomwe anamugwililira,”anatero Sergent M’bumpha.

Iwo anapitiliza ponena  kuti singangayo anauza mayiyu kuti asakanene kwa anthu kamba alodzedwa koma mayiyu atabwelera kumudzi anakauza mwamuna wake yemwe anakanena nkhaniyi ku polisi.

 A Willard Jabesi Njovu amachokera m’mudzi mwa Mingu kwa mfumu yaikulu Choolo m’boma la Ntchisi.

Ambuye Ziyaye Alimbikitsa Pakati pa Akhristu

$
0
0

Ark Episkopi wa Arch Dayosizi ya Lilongwe Ambuye  Tarsizius Ziyaye apempha akhristu a m’parishi ya St Kizito mu Ark dayosiziyo kuti alimbikitse m’gwirizano wabwino pakati pawo.

Ambuye Ziyaye anena izi lamulungu pa mwambo wokhazikitsa bukhu la ndondomeko  za chitukuko m’parishiyi.

Iwo ati mapulani a zachitukuko omwe parishiyo yakonza ndi osavuta kuwakwaniritsa pokhapokha atamanga mgwirizano pakati pawo

Bambo wina M’boma la Ntchisi Wafa ndi Chiphaliwali

$
0
0

 

Bambo wina wa zaka 40 zakubadwa wamwalira atawombedwa ndi mphenzi m’boma la Ntchisi.

Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Sergent Gladson M’bumpha watsimikiza za nkhaniyi.

Iye wati chiphaliwalichi chinadza kamba ka mvula ya mphamvu yomwe inagwa m’delalo masana a lachiwiri m’bomalo.

Malingana ndi a M’bumpha chiphaliwalicho chitamuwomba mkuluyi ati anthu anamutengera ku chipatala komwe malipoti anasonyeza kuti anali atamwalira kale.

Malemuyu Richard Banda anali wochokera m’mudzi wa Buleya kwa mfumu yaikulu Nkhombedza m’boma la Salima.

Papa Wapepesa Dziko la Romania Kamba ka Ngozi ya Moto

$
0
0

Mtsogoleri wa Mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapepesa Pulezident wa dziko la Romania potsatira ngozi ya moto yomwe yapha anthu makumi atatu ndi awiri, ndikuvulaza ena 130 mu m’dzinda wa Bucharest m’dzikolo.

 

Papa  wati ndi wokhuzidwa chifukwa mwa anthu omwe amwalira komanso kuvulala ndi anyamata ndipo  wati alimbikitsa mapemphero ku m’maanja omwe akhudzidwa ndi ngoziyi.

 

Malipoti a wailesi ya Vatican ati   motowo unayamba kamba ka mphamvu ya magetsi yomwe bandi yomwe imasangalatsa anthu patsikulo imagwiritsa ntchito.

Anthu 11 Avulala pa Ngozi ya Galimoto

$
0
0

 

Anthu khumi ndi m’modzi avulala pa ngozi ya galimoto m’boma la Ntchisi.

Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomali Sergent Gladson Mb’umpha wati pa anthu omwe avulalawo, anayi avulala kodetsa nkhawa ndipo akulandira thandizo pa chipatala chachikulu cha m’bomalo, pomwe mayi m’modzi amutumiza ku chipatala cha Kamuzu Central mu mzinda wa Lilongwe.

Galimotolo ati lachita ngoziyi kamba koti dalaivala yemwe amayendetsa galimotolo analephera kuwongolera kamba ka vuto la ma buleki.

Dalaivalayo ndi Benson Ching’ombe, pomwe galimoto lomwe amayenetsalo ndi la mtundu wa Toyota Hilux , nambala yake ndi NS 479 ndipo linanyamula anthu khumi ndi asanu omwe amapita ku maliro .

Alimi Apewe Kugula Mbeu Wamba

$
0
0

Kampani yogulitsa  mbeu mdziko muno ya Mosanto Malawi yachenjeza alimi   kuti apewe kugula mbeu kwa mavendor.

Mkulu wa zamalonda ku kampaniyi a Denis Kachikho ndi omwe anena izi potsatira kumangidwa kwa a Mavuto Chilipa omwe apolisi   anawapeza akugulitsa mbeu yowonongeka    ya chimanga pa nsika wa Bvumbwe m’boma la Thyolo.

A Kachikho ati ma venda nthawi zina amapezeka ndi katundu wosayenera choncho ndi kofunika kuti alimi asamagule mbeu zawo.

Iwo apemphanso boma kuti liwunikenso malamulo ogulitsira mbeu ndi cholinga choti aliyense wopezeka akugulitsa mbeu yowonongeka azipatsidwa chilango chokhwima.

Pamenepa Iwo ati  mchitidwe wotere umabwezera m’mbuyo chitukuko ndinso njala m’dziko muno.


Dziko la Nigeria Lalephera Kuteteza Mzika Zake

$
0
0

Bungwe lowona za ufulu wa anthu padziko lonse la Amnesty International,lati dziko la Nigeria lalephera kuteteza mzika zake zomwe zikukhala mdera la Baga,pamene gulu la zigawenga la Boko Haram lawopseza kuti lichita zamtopola mderalo.

Malipoti ena ati akusonyeza kuti anthu pafupifupi zikwi ziwiri aphedwa mderalo mmwezi wa December okha chaka chatha,koma boma la Nigeria likungotchula chiwelengero cha anthu 150 okha kuti ndi omwe aphedwa mmweziwo paziwembu zomwe zigawengazo zakhala zikuchita mderalo.

Padakali pano, mmodzi mwa akuluakulu a asilikali mdzikolo yemwe sadafune kutchulidwa dzina,ati wawuza bungweli kuti ngakhale boma silikuchitapo kanthu,gululo lawopseza zochita chiwembu mdera la Baga.

Pothilirapo ndemanga mneneri wa asilikali a boma mdzikolo wauza mtolankhani wa BBC kuti asilikali ali okonzeka mderalo pomwenso akumayendera matauni ake pafupipafupi

Mabungwe Achitepo Kanthu kwa Anthu Okhudzidwa ndi Kusefukira kwa Madzi

$
0
0

Bungwe lowona ma ufulu a anthu mchipembedzo cha Chisilamu la Muslim Forum for Democracy lalangiza mabungwe omenyera ufulu wa anthu mdziko muno,kuti athandize anthu omwe akhudzidwa ndi mvula ya mphamvu yomwe  yakhala ikugwa mdziko muno.

Wapampando wa bungweli Sheikh  Jafar Kawinga ndi yemwe wapereka langizoli ,pomwe bungweli mogwirizana ndi bungwe la Al-barakah Charity Trust, limapereka   katundu wosiyanasiyana kwa anthu omwe akhudzidwa ndi mvula yamphamvu mdera la   group Mkupu mfumu yayikulu Kadewere mboma la Chiradzuru..

Sheikh Kawinga wati mabungwe omenyera ufulu wa anthu , padakali pano angokhala chete pomwe anthu omwe amati amawayimilira, akuvutika ndi vuto la kusefukira kwa madzi. Pamenepa iwo ati nthawi yakwana yoti mabungwewa awonetse mbali yawo pothandiza anthuwa pomwe ali pamavuto osiyanasiyana kamba ka mvulayi.

Dziko la Malawi Lipundula pa Ntchito Yofalitsa Uthenga Wabwino

$
0
0

Dziko la Malawi ati likuyembekezeka kupindula pa ntchito yofalitsa uthenga wabwino komanso yotukula dziko lino potsatira msonkhano waukulu wanyumba zofalitsa nkhani za Radio Maria womwe wachitikira m`dziko laItaly.

Mkulu oona za pulogalamu ku Radio Maria Malawi  Bambo Joseph Kimundi omwe anena izi potsatira msonkhano omwe cholinga chake chinali kuwunika momwe wailesizi zagwilira ntchito mzaka zitatu zapitazo komanso kukambirana momwe agwirile ntchito  mzaka zitatu zikubwerazi.

Mwazina nthumwi kusonkhanowu zagwirizana kutsekula nyumba zina zofalitsa mawu m`mzigawo za Africa komanso Asia.

Bambo Kimu ati anthu m`dziko muno ayembekezere mapulogalamu abwino kamba koti ku msonkhanowu aphunziranso momwe wailesi zina zikuchitira pa ntchito yofalitsa uthenga wabwino.

Dziko la Malawi ati likuyembekezeka kupindula pa ntchito yofalitsa uthenga wabwino komanso yotukula dziko lino potsatira msonkhano waukulu wanyumba zofalitsa nkhani za Radio Maria womwe wachitikira m`dziko laItaly.

Mkulu oona za pulogalamu ku Radio Maria Malawi  Bambo Joseph Kimundi omwe anena izi potsatira msonkhano omwe cholinga chake chinali kuwunika momwe wailesizi zagwilira ntchito mzaka zitatu zapitazo komanso kukambirana momwe agwirile ntchito  mzaka zitatu zikubwerazi.

Mwazina nthumwi kusonkhanowu zagwirizana kutsekula nyumba zina zofalitsa mawu m`mzigawo za Africa komanso Asia.

Bambo Kimu ati anthu m`dziko muno ayembekezere mapulogalamu abwino kamba koti ku msonkhanowu aphunziranso momwe wailesi zina zikuchitira pa ntchito yofalitsa uthenga wabwino.

Bwalo Lalikulu la Milandu Mdziko la Kenya Lakana Kuwonjezera Malipiro Aphunzitsi Mdzikolo

$
0
0

Bwalo lalikulu lamilandu mdziko la Kenya lakana kuwonjezera malipiro a aphunzitsi a mdzikolo ndi ma peresenti 60 monga momwe bwalo la milandu lowona za kagwiridwe komanso kalembedwe ka ntchito linagamulira.

 

Bwaloli lati bwalo la milandu lowona za kagwiridwe komanso kalembedwe ka ntchito  linalibe mphamvu zopereka chigamulo pa mlanduwu.

 

Malipoti a wailesi ya BBC ati koyambilira kwa chaka chino aphunzitsi mdzikolo ananyanyala ntchito kwa sabata zisanu kaamba koti boma limakana kuwakwezera malipiro.

 

Malinga ndi malipoti boma la dzikolo ati likhala lokondwa ndi chigamulochi kaamba koti silikanakwanitsa kuwonjezera aphunzitsiwa malipolo awo kaamba ka vuto la zachuma mdzikolo.

 

Padakali pano aphunzitsiwa ati akamang’ala ku bwalo lalikulu la supreme kuti  litembenuze chigamulochi.

JOINT MEDIA AND ADVOCACY STATEMENT

$
0
0

1.0. PREAMBLE

The Catholic Commission for Justice and Peace (CCJP) which is a social justice and advocacy arm; and the Research and Social Commission which is the communication arm of the Episcopal Conference of Malawi, an umbrella body of the Catholic Bishops in Malawi, have noted with concern the current updates provided by the Malawi Government on the status of Access to Information Bill (ATI). So far, the updates provided by the Leader of Government Business,  Honorable Francis Kasaira and Minister of Information, Honorable Jappie Mhango, whilst they have more details; lack precision, timeliness and are far from bringing about the much needed enabling legal framework of access to information highly needed by Malawian citizenry, CSOs and the media. We, therefore, kindly request government and especially cabinet to expedite ‘’the VERY advanced stages’’ of the ATI Bill so that this bill is soon enacted into law. In any case, we are convinced as per the DPP February, 2014 Manifesto commitment made on chapter 30, page 57 and paragraph 4 that the DPP led government is already committed to seeing this bill legislated and in operation.

2.0. OUR APPRECIATION

We, the Catholic Commission for Justice and Peace and the Research and Social Communication Commission of the Episcopal Conference of Malawi, in this discourse for the enactment of the Access to Information Bill appreciate the following:

                   I.            That government and other relevant stakeholders that value this relevant bill have already shown high levels of commitment and effort to bring this bill into existence

                II.            That most political parties showed commitment to this bill by highlighting it as a priority in their 2014 manifestos

             III.            That presently Access to Information Bill continues to dominate national discourse further highlights the importance Malawians accord this bill.

3.0. OUR CONCERNS

We, the Catholic Commission for Justice and Peace and the Research and Social Communication Commission of the Episcopal Conference of Malawi, while we appreciate the clarification made by Government of Malawi through a media statement released on Friday, 6th November, 2015 by the Minister of Information, would like to raise the following concerns:

       I.            The ATI Bill has been outstanding spanning four political regimes from Dr. Bakili Muluzi’s Administration (1994-2004) and later Dr. Bingu wa Mutharika’s administration (2004-2012), Dr. Joyce Banda’s administration (2012-2014) and the current Professor Arthur Peter Mutharika’s administration. The length of time that the bill has taken before enactment is raising suspicions as to the lack of sustained political will to expedite the process by all regimes.

    II.            We note that while Government indicates that the bill is at an advanced stage, it, however, does not provide an indicative time frame that the bill has to go through before being presented in Parliament. Considering the serious delayed and sluggish history of the bill, the recent update from Government is wanting as it is devoid of specific time frames.

 III.            As noted above in this statement, the DPP manifesto outlined the ATI Bill as a priority. On the contrary though, it is disheartening that 5 parliamentary sessions have gone by without tabling the bill; instead what the nation gets are mere assurances that the bill will be tabled. We are therefore worried that this might be a continuation of the established trend whereby administrations come and go without enacting the ATI when they promised so during their campaigns.

4.0. OUR APPEAL

We, the Catholic Commission for Justice and Peace and the Research and Social Communication Commission of the Episcopal Conference of Malawi, would like to make the following appeal to the following key stakeholders:

       I.            The President and Cabinet: To ensure that the process gets political backing and support at all levels and that cabinet prioritizes the bill in their most immediate meetings.

    II.            The Ministry of Justice and Ministry of Information: We are imploring them to expedite the process that will lead to the passing of the bill in Parliament.

 III.            CSOs, the Media and General Public: To be vigilant, proactive and intrusive and to exercise active citizenship to ensure that our leaders live by the promise to pass the bill.

5.0. CONCLUSION

We, the Catholic Commission for Justice and Peace and the Research and Social Communication Commission of the Episcopal Conference of Malawi, aware of the varying opinions, frustrations, fears among different interested stakeholders call upon Malawi Government to act with speed and honesty to ensure that the ATI bill is tabled before Parliament. Noting the relevance and the critical significance of the ATI, We, the Catholic Commission for Justice and Peace and the Research and Social Communication Commission of the Episcopal Conference of Malawi are releasing this advocacy media statement to contribute to the already existing efforts from other interested stakeholders for an expedited enactment of the ATI Bill. Since Malawi government joined the open government initiative, it is only prudent and logical that this ATI is in place to domesticate this global initiative. The legal enabling environment therefore is very key.

 

Signed by:

Carsterns Mulume, Director for Social Development Directorate

Chris Chisoni, National Secretary for Catholic Commission for Justice and Peace

Fr. Andrew Kaufa, National Secretary for Research and Social Communication Commission

Viewing all 1875 articles
Browse latest View live


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>