Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all 1875 articles
Browse latest View live

Ambuye Sitima ati Makwaya Azipeka Nyimbo za Tanthauzo

$
0
0

Episkopi wa Dayosizi ya Mangochi ya mpingo wakatolika Ambuye Montfort Sitima wapempha makwaya mdziko muno kuti aziwonetsetsa nthawi zonse kuti pamene akupeka nyimbo zizikhala za tanthauzo.

Ambuye Sitima amalankhula izi lamulungu ngati mlendo wolemekezeka pomwe kwaya ya St Patricks yochokera ku parish ya St Augustine Cathedral mu dayosiziyi imakhazitsa chimbale cha nyimbo zowonera.

Iwo ati makwaya akamapeka nyimbo zawo aziwonetsetsa kuti  zikugwirizana ndi chiphunzitso cha mpingo wakatolika.

Pamenepa Ambuye Sitima ayamikira kwayayi pa luso lomwe ili nalo lofalitsa uthenga wabwino kudzera mmayimbidwe.


Dziko la Sierra Leone Likondwelera Kutha kwa Matenda a Ebola

$
0
0

Anthu m’dziko la Sierra Leone akupitiliza kuchita chisangalalo chokondwelera kutha kwa matenda a Ebola m’dzikomo.

 

Bungwe la za umoyo pa dziko lonse la World Health Organization ndi lomwe lalengeza izi, potsatira kafukufuku yemwe lachita m’dzikomo.

 

Bungweli lati masiku 42 omwe linakhadzikitsa ofuna kufufuza ngati alipo munthu wina wodwala matenda atha zomwe zikupereka chitsimikizo chakuti matendawa atha m’dzikomo. 

 

Matenda a Ebola anayamba m’dzikomo  ndi mayiko ena oyandikana ndi dzikoli monga a Guinea, Liberia kuyambira mchaka cha 2013.

 

Malingana ndi malipoti anthu oposera 11 sausande ndi amene akuwaganizira kuti anafa atagwidwa ndi matendawa m’mayikowa.

 

Padakali pano ntchito yothana ndi matendawa ati ili mkati m’dziko la Guinea lomwe lachita malire ndi dzikolo.

Nsika wa Kasungu Ukufunika Ndalama Zokwana 10 miliyoni Kwacha

$
0
0

Nsika wa Kasungu omwe unapsa mwezi wa October ati ukufunika ndalama zoposa 10 Million Kwacha kuti ukozedwenso. 

Wachiwiri kwa Meya wa Manicipality ya Kasungu  a Ephate Joshua ndi yemwe wanena izi pomwe kampani yopanga cement ya  Shayona imapereka matumba a cement okwana 1 hundred 20 ku khonsoloyi ndi cholinga chothandizira ntchito yokonzanso  msikawu.

A Joshua ati motoyu unaononga zinthu zambiri kuphatikizapo maofesi ena  a khonsoloyi ndipo pafunika ndalama zokwana 10  million kwacha kuti zinthu zibwerelenso m`chimake.

Iwo ati padakali pano khonsoloyi ikulephera kutolera misokho mumsikawu zomwenso zikubwenzeretsa ntchito zake m`mbuyo.

M`mawu ake m`modzi mwa akuluakulu a kampani ya Shayona a Austin Mvula  anati apereka thandizoli kamba koti anamva za ngoziyi.

Pulezidenti Kagame Adzudzula Dziko la Burundi

$
0
0

Mtsogoleri wa dziko la Rwanda  Paul Kagame  wadzudzula ziwawa zomwe zikuchitika m`dziko la  Burundi zomwe zikuphetsa anthu ankhanikhani.

Pulezidenti Kagame wati  anthu m`dzikolo akungophedwa mwachisawawa tsiku  lililonse komanso matupi a anthu akufa akungopezeka mmisewu ya mdzikolo.

Izi zadza potsatira chenjezo la pulezidenti wa dziko la Burundi a Pierre Nkurunziza omwe anati athana ndi wina aliyense yemwe amatsutsa mfundo zoyendetsera dzikolo.

Zipolowe m`dziko la Burundi zinayamba m`mwezi wa April chaka chino pomwe Pulezidenti wa dzikolo analengeza kuti ayimanso kachitatu pa mpandowu zomwe ndi zosemphana ndi malamulo oyendetsera dzikolo.

Atolankhani Azilemba Nkhani za Matenda Osapatsirana

$
0
0

Atolankhani mdziko muno awapempha kuti azilemba nkhani zokwanira zokhudza matenda osapatsirana omwe ndi kuphatizapo a shuga pofuna kuchepetsa imfa zomwe zimachitika kudzera mmatendawa

Mkulu wa bungwe la atolankhani  olimbana ndi matenda a Edzi a Christopher Bauti,ndi omwe apereka pempholi m’boma la Salima, pa maphunziro a tsiku limodzi a atolankhani a momwe angamalembere nkhanizi pofuna kuzindikiritsa anthu za matendawa.

A Bauti ati pali matenda ambiri osapatsirana monga khansa, shuga ndi ena omwe akutenga miyoyo ya anthu ambiri, ndipo ati mpofunika kuti anthu azizindikiritsidwa mokwanira maka momwe angathe kuwapewera.

“Tinawona kuti ndi cha nzeru kuti tiwayitane atolankhani kuti atithandize kufalitsa uthenga wa matenda a shuga ndi ena kuti anthu azikhala akudziwa,”anatero a Bauti.

Iwo ati maphunzirowo athandiza atolankhaniwa kuti akhale ndi chinthunzinthuzi cha mmene matenda osapatsirana amayambira komanso mmene anthu odwala matendawa angasamalidwile.

 

Ulendo wa Papa Wokacheza Mdziko la CAR Upereka Chiyembekezo kwa akhristu a Mdzikolo Ulendo wa Papa

$
0
0

Akhristu a mpingo wa katolika a m’dziko la Central African Republic omwe akhala akuphana tsiku ndi tsiku kamba ka nkhondo ati akuyembekezera kuti ulendo wa mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wokacheza mdzikolo m’mwezi uno  uthandiza kuchepetsa mavuto omwe dzikolo likukumana nao.

 

Malinga ndi malipoti a News 24 ulendo wa Papa wokacheza mdzikolo upereka chiyembekezo  kwa anthu a mdzikolo.

 

Anthu a mdziko la Central African Republic akhala akuphana kamba ka kusamvana kwa boma la dzikolo ndi magulu owukira. 

 

Pa ulendowu Papa akuyembekezeka kukayendera malo omwe anthu akukumana ndi mavuto kamba ka nkhondoyi amakhala komanso mzikiti womwe umatchedwa kuti ndi woopsa mu mzinda wa Bangui ndipo pamapeto pake akachita mwambo wa nsembe ya misa pa bwalo lalikulu la masewero mdzikolo.

 

Papa akacheza mdzikoli pa 28 ndi pa 29 mwezi uno.

Bungwe la Community of St Egidio Layamba Kuphunzitsa Anthu Kufunika Kolembesa Ana Obadwa Kumene

$
0
0

Bungwe la mpingo wa Akatolika la Community of St Egidio m’dziko muno layamba ntchito yophunzitsa anthu kufunika kwa kalembera wa ana omwe angobadwa kumene.

Polankhula pa mwambo otsegulira maphunziro a ntchitoyi omwe ukuchitikira mu mzinda wa Blantyre mkulu oyendetsa ntchito mu nthambi ya boma yoona za
kalembera ya National Registration Bureau a Francis Chinsinga ati ali ndi chikhulupiriro choti ntchitoyi iyenda bwino kamba ka m’gwirizano omwe ulipo pakati pa boma ndi bungweli m’dziko muno.

 A Chinsinga ati ntchitoyi yomwe yayamba m’boma la Balaka ikuyembekezera kufalikira m’madera ena m’dziko muno.

Apolisi Ati Anthu Azigwiritsa Ntchito Malamulo MoyeneraApolisi Ati Anthu Azigwiritsa Ntchito Malam

$
0
0

Apolisi apempha anthu m’dziko muno kuti azitengera kupolisi anthu onse omwe akuwaganizira kuti apalamula milandu osati kuwalanga okha.

Wachiwiri kwa mneneri wa apolisi ku Limbe mu mzinda wa Blantyre Sergent Pedzesai Zembenako ndi amene wanena izi potsatira  kuphedwa kwa anthu omwe amawaganizira kuti anakaba pa malo ena ogulitsira mowa ku Chigumula mu mzindawu.  

“Ndi zoona kuti anthu aphedwa chifukwa chomenyedwa ndi anthu a mmudzi. Chomwe chinachitika ndi chakuti anthuwo anapita kukaba ku Chigumula pa malo ena  ogulitsira mowa atakwanisa kuba anayamba kuthawa, mwa mwayi anagwidwa ndi anthu pambuyo pake anayamba kuwamenya,” anatero Sergent Zembeneko     

Sergent Zembeneko ati awiri mwa akubawo amwalilira pomwepo ndipo  mmodzi anavulala kwambili ndipo wamwalilira mu njira popita ku chipatala. 

Iwo ati akuyesetsa kuti athetse mchitidwewu  ndipo kudzera munthambi ya chitetezo  cha mmudzi tipitiliza kuwaphunzitsa mmene angachitire akagwira munthu akuba.

Pamenepa Sergent Zembeneko apempha atolankhani mdziko  muno kuti agwirane  ndi apolisi pophunzitsa anthu kuyipa kwa mchitidwe umenewu kamba koti umasokoneza umboni.


nthu ena Anakawombera Mdera la Kumpoto kwa Mzinda wa Paris

$
0
0

Pomwe apolisi mu mzinda wa Paris mdziko la France akupilizabe kuchita kafukufuku wa anthu omwe anachita chiwembu chomwe chinapha anthu pafupifupi 1 hundred 30 mdzikolo, anthu ena omwe sakudziwika ati anakawombera dera la ku mpoto kwa mzindawu.

Malipoti ati dera lomwe anthuwa anakawombera ndi limodzi mwa madera omwe zigawenga za Islamic State linawononga kwambiri pa chiwembu chomwe chinachita mdzikolo posachedwapa.

Malinga ndi malipoti a nyuzi 24   apolisi omwe amagwira ntchito pa nthawiyo avulala.

Padakali pano ndege za asilikali akhondo a mdziko la Russia ndi France zikufunafuna zigawengazi mmadera omwe akuwaganizira mdziko la Syria.

Matenda a Ebola Akuyembekezeka Kutha Mdziko la GuineaMatenda a Ebola Akuyembekezeka Kutha Mdziko la

$
0
0

Munthu wotsiriza yemwe amadwala matenda a Ebola m`dziko la Guinea wachira ndipo amutulutsa mchipatala. 

Malinga ndi wofalitsa nkhani ku nthambi yomwe imayang`anira ntchito zothana ndi matendawa m`dzikolo  wodwalayo yemwe ndi mwana wa masiku khumi asanu ndi atatu ndipo anabadwa kwa mayi yemwe anali ndi matenda a Ebola, atamupima zotsatira zinawonetsa kuti wachira.

Malipoti ati pakatha masabata asanu ndi limodzi opanda munthu odwala matendawa, dzikolo likhala m`gulu la mayiko omwe nthendayi yatha.

Matenda a Ebola anayambira m`dziko la Guineandipo anafalikira m`mayiko a Sierra Leone  ndi Liberia ndipo anapha anthu oposa 11 sauzande  kuyambira m`mwezi wa March  2014.

Dziko la Canada Lichepetsa Chiwerengero Chosunga Anthu Othawa Kwawo

$
0
0

Dziko la Canada lati lisunga anthu othawa kwao okwana 10 sauzande ochokera mdziko la Syria chikamatha chaka chino.

Malipoti a wailesi ya BBC ati dzikoli poyamba linalonjeza kuti lisunga anthu othawa kwao okwana 25 sauzande chikamatha chaka chino.

Malinga ndi malipoti boma la dzikolo lipereka malo okhala kwa amayi, ana komanso mabanja okha.

Padakali pano boma la dzikolo lalonjeza chisamaliro chabwino pa nkhani ya umoyo komanso kuti ndege za asilikali a dzikolo ndi zomwe zikhale zikunyamula anthu kuchokera mdziko la Syria kupita mdzikolo

Anthu Odwala Matenda a Edzi Asasalidwe

$
0
0

Bungwe  la National AIDS Commission NAC lati anthu omwe anapezeka ndi kachilombo koyambitsa  matenda a Edzi sayenera kusalidwa .

 

Mmodzi mwa akuluakulu ku bungweli  a Ahmidu Tung'ande ndi omwe anena izi mu mzinda wa Zomba pomwe amakumana ndi mabungwe a boma komanso omwe si a boma pomwe amawafotokozera momwe bungweli likugwilira ntchito zake.

A Tung'ande ati ndi cholinga cha bungweli kuti pomafika mchaka cha 2020 nthenda ya Edzi idzakhale itatha mdziko muno.

Iwo alangiza azipembezo zina mdziko muno kuti asiye mchitidwe woletsa akhristu awo omwe anapezeka ndi kachilombo ka HIV kuti asiye kumwa makhwala otalikitsa moyo a ARV kamba koti  munthu aliyense amene anapezeka ndi kachilomboka ali ndi ufulu womwa makhwalawa. 

 

A Tung'ande anatinso pali ana ena omwe anabadwa ndi kachilomboka ndipo apempha makolo amene ali ndi anawa kuti aziwonetsetsa kuti nthawi zonse akuwapatsa makhwala.

 

Mmau ake mkulu wa zaumoyo mu mzindawu a Gomezgani Nyasulu anati pakuyenera kukhala  mgwirizano wabwino pakati pa mabungwe omwe amagwira ntchito zokhudza matendawa m’bomalo.

 

Pomaliza a Nyasulu anayamikira bungwe la  NAC kamba ka ntchito yabwino yomwe likugwira yofuna kuthetsa matendawa mdziko muno.

Bungwe la MBTS Lipempha Anthu kuti Agwirane Nalo ManjaBungwe la MBTS Lipempha Anthu kuti Agwirane Na

$
0
0

Bungwe lotolera magazi la Malawi Blood Transfussion Service MBTS lamemeza anthu  kuti agwirane nalo manja powonetsetsa kuti zipatala za m'dziko muno zili ndi magazi okwanira komanso a ukhondo.

 

Mkulu wa bungweli mayi Natasha Nsamala ndi omwe apereka pempholi mu mzinda wa Blantyre pomwe bungweli limafotokozera atolankhani momwe ntchito ya chaka chino yozindikiritsa anthu pa nkhani ya kupereka magazi iyendere.

Mayi Nsamala ati nyengo ya mvula chiwerengero cha anthu osowa kulandira magazi mu zipatala chimachuluka.

Iwo ati nthawi ya zisangalalo ngozi zimachuluka kotero kuti ngati magazi akhala ochepa kapena kusoweratu, miyoyo ya anthu ochuluka imakhala pa chiwopsyezo.

Pamenepa iwo apempha aMalawi omwe ali ndi kuthekera kopereka magazi kuti apereke pa nthawiyi kuti miyoyo yochuluka ipulumutsidwe.

Bungwe la Community of Saint Egidio Likondwelera Zaka 47 Chilikhazikitsire

$
0
0

Bungwe la Community of Saint Egidio lati ndi lokondwa kuti tsopano lakwanitsa zaka 47 kuchokera pomwe bungweli linayamba kugwira ntchito zake zolimbikitsa moyo wa mapemphero ndi kudzipeleka pogwira ntchito zachifundo ndi zina.

Bungweli lomwe linayambira ku Rome  m’chaka cha  in 1968, padakali pano lili ndi mamembala oposera 60,000 ndipo lafalikira mmayiko 73 pa dziko lonse.

Pa mwambo waukulu wokondwelera ntchito za bungweli akuti kunafika ma episcope zana limodzi ochokera mmayiko osiyanasiyana a padziko lonse, omwe mwazina agawana mfundo zikuluzikulu zothandiza pa ntchito za bungweli .

Zina mwa  ntchito zomwe bungweli limagwira ndi kulimbikitsa mtendere wa m’mayiko, moti mbiri imasonyeza kuti bungweli linatengapo gawo lalikulu pothandiza kuthetsa nkhondo ya pa chiweniweni yomwe inachitikapo m’dziko la Mozambique.

Bambo Corna a Mdziko la Italy Amwalira

$
0
0

A ku Likulu la chipani cha Mofolo Woyera ku Rome mdziko la Italy alengeza za imfa ya Bambo Attilio Corna omwe anamwalira  lachiwiri pa 10 February 2015 mu mzinda wa Bergamo mdzikolo.

Bambo Corna amwalira ali ndi zaka 91 zakubadwa atatumikira mu chipani cha Mofolo woyera kwa zaka 71.

Bambo Corna anali wansembe woyamba kukhala mphunzitsi wamkulu ku Seminale ya Saint Paul the Apostles mchaka cha 1985.

Mzimu wa Bambo Atilio Corna uwuse mu mtendere wosatha.


Sister Martha Clemence Manuel Makhasa a Chipani cha SBVM Amwalira

$
0
0

Sister Martha Clemence Manuel Makhasa a Chipani cha Servants of Blessed Virgin Mary (SBVM), amwalira lachisanu.

Malinga ndi akulikulu la chipanichi Sister Martha anabadwa pa 8 September 1932 ndipo malumbiro awo a mpaka kufa anachita pa 8 December 1961. 

Sister Martha Clemence Manuel Makhasa  kudzera m`chipanichi atumikira malo osiyanasiyana monga Nguludi, Namulenga, Limbe, Magomero, Molere, Neno, Matiya, Mulanje, Utale, Nankhunda komanso Mwanza ndipo  Motto yawo ndi ‘kufuna kwanu kuchitidwe.’

Malinga ndi chipani cha SBVM, Sister Martha adzawakumbukira chifukwa cha kudzichepetsa kwawo, kudzipereka pa ntchito komanso kukhala mwa mtendere.

Mwambo woyika m`manda nthupi lawo uchitika pa 16 February 2015 ku mary view ku Nguludi motsogozedwa ndi nsembe ya ukaristia.

Mzimu wa Sister Martha Clemence Manuel Makhasa uuse mu mtendere wosatha.

 

 

KUTHETSA MLILI WA HIV: KUWUNIKA UDINDO WA MPINGO PA NDONDOMEKO YA 90-90-90

$
0
0

            - Osatopa ndikuchita zinthu zabwino- (2 Thess. 3:13)

Uthenga wa HIV ndi EDZI m’chaka cha 2015

From ECM Health Commission

 

1.0 CHIYAMBI

Lero ndi lamulungu loyamba  munyengo ya Adventi. Mpingo wayamba chaka chatsopano, ulendo watsopano muchikhulupiliro.  Pamene mpingo wayamba chaka chatsopanochi, ukhala ukukumbukila tsiku la EDZI, (World AIDS day), pamaodzi ndi dziko lonse la pansi; lomwe limakhalapo pa 1 December chaka chili chonse.

Patsikuli, aboma, mabungwe a mipingo, mabungwe amadela osiyanasiyana ndi anthu mu dziko lonse la pansi amawonetsapo chidwi chawo pa mlili wa HIV komanso kutsindikapo pakufunika kodzipeleka pothana ndi mlili wa matendawa. Ngati akhristu tsikuli limatithandiza kusinkhasinkha za nthenda ya HIV ndi EDZI komanso udindo wathu pa mliliwu.

Chaka chino mutu wathu ndi “kuthetselatu: kuthetselatu kutenga kachilombo ka HIV, kuthetselatu kusankhana ndi kusalana komanso kuthetselatu imfa zodza ndi EDZI” ndicholinga chofuna kukwanilitsa ndondomeko ya 90-90-90 pothana ndi matendawa yomwe inakhazikitsidwa ndi bungwe la United Nations la UNAIDS.

Tsikuli likutipatsanso mwayi woyamikila mipingo pa ntchito yomwe ikugwira pothana ndi mliliwu komanso kuwunikilapo pa ndondomeko ya 90-90-90 yothana ndi matendawa.

 

 

 

1.1 NDONDOMEKO YA 90-90-90

Chaka cha 2014, bungwe la UNAIDS linalengeza ndondomeko yatsopano ya 90-90-90 imene yamanga maziko a nfundo ya “kuthetselatu” ndi cholinga chothetselatu ka chilombo ka HIV pofika m’chaka cha 2030.

Zolinga zawo pofika 2020 ndi izi:

  • Athu 90 mwa handiredi (100) aliwonse omwe ali ndi kachilomboka adzakhala akudziwa momwe magazi  awo ali.
  • Athu 90 mwa 100 aliwonse omwe anawapeza ndi kachilomboka azakhala akulandira mankhwala otalikitsa moyo ama ARV
  • Athu 90 mwa 100 aliwose omwe akumwa mankhwala azakhala ndi chiwerengero cha tizilombo toyambitsa matendawa chotsika kwambiri magazi mwawo.

Kukwaniritsa zolingazi pofika chaka cha 2020 kuzathandiza kuthana ndi mliliwu pofika 2030, zomwe zizathandize kubweretsa moyo ndi chuma chabwino.

2.0 KODI NDI CHANI CHOMWE CHIKUCHITIKA MDZIKO LATHU?

Malawi ndi limodzi mwa mayiko omwe akhudzidwa kwambiri ndi mlili wa HIV. Pafupi-fupi  athu 10 mwa 100 aliwonse azaka zoyambira 12 mpaka 49 zakubadwa ali ndi matendawa. Chiwerengero cha athu omwe ali ndi HIV chikutsika; kuchoka pa 55,000 muchaka cha 2011 kufika pa 34,000 chaka cha 2013. Nzokhumudwitsa kuti theka la athu omwe akutenga nthedayi ndi achinyamata azaka 15 mpaka 24 zakubadwa. Anthu ambiri omwe atenga matendawa ndi omwe ankaonedwa ngati ali pachiopsezo chochepa chotengera matendawa, mwa chitsanzo athu omwe ali pa banja komanso zibwezi zokhazikika.

 

Zinthu zomwe zikupititsa patsogolo kufala kwa chilombocha HIV dziko muno ndi izi:

  • Nchitidwe ogonana, mwachitsanzo kukhala ndi athu ogonana nawo ambiri
  • Kusiyana pakati pa amayi ndi abambo kukuyika amayi ndi atsikana pachiopsezo chochulukirapo potenga matendawa
  • Umphawi omwe ukulimbikitsa kugonana kosithana ndi ndalama.

Mukudzipereka kwake pofuna kuthesa Edzi, dziko la Malawi  lavomera kugwiritsa ntchito  ndondomeko ya 90-90-90. Nfundo zoyendetsera  matenda a HIV mudziko muno zawunikiridwaso  ndi cholinga chofuna  kukumana  ndi ndondomeko ya 90-90-90.

 

 

Pofuna kukwanilitsa ndondomekozo, Malawi akufunika kuchita izi:

                               I.            Kuunika njira zoyezera HIV komanso kuunika uphungu omwe ungaperekedwe kuti athane ndi zikhulupiliro  zolakwika zokhudzana  ndikayezedwe ka HIV, ndikulimbikitsa  anthu kuti akayezetse ndikulandira uphungu oyenera.

 

                            II.            Kuchulukitsa malo olandilirapo chithandizo ndi cholinga chochepetsa kuchulukana kwa anthu pa malo omwe amalandirirapo kale, kuphunzitsa anthu za ndondomeko yatsopano  ya 90-90-90 ndinso kuwalimbikitsa kuti ayambe kumwa mankhwala mwasanga.

 

                         III.            Kulimbikitsa anthu omwe ali ndi matendawa kuti  asamasiyire panjira kumwa mankhwalawa. Kuwalimbikitsa kudzera m’magulu, komanso kaunikidwe ka chiwerengero cha tizilombo toyambitsa matendawa m’magazi mwawo kuti aziwasinthira mankhwala mu nthawi yoyenera.

3. TIKUYENERA KUCHITAPO KANTHU.

Mpingo wa Katolika watengapo mbali pothesa matenda a HIV ndi EDZI mu njira izi:

       I.            Anali oyamba kupangitsa pulogilamu ya Home Based Care mu dziko muno pamene matendawa anangoyamba kumene.

    II.            Kukumbukira tsiku la Edzi la mulungu loyamba mu nyengo ya advent chaka chili chonse.

 III.            Inapanga njira zoyendetsera nkhani  zokhudzana ndi HIV  ndi EDZI mu mpingo. HIV/AIDS Policy

 IV.            Kulimbikitsa kupewa HIV kudzera mukudziletsa kwa achinyamata ndikukhulupilika m’banja.

    V.            Kupereka chithandizo kwa odwala mwachitsazo mankhwala otalikitsa moyo komaso kuthandiza kuchiza matenda omwe angadze kamba ka HIV kudzera muzipatala.

 

Khama la mpingo  likuonekera mu ntchito  zomwe wachita. Komabe pali zambiri zomwe mpingo ungathe kuchita pothana  ndi mliliwu makamaka potsata  ndondomeko ya 90-90-90. Nyengo  ya advent  yayamba ndi mawu anzeru ochokera mwa Khristu akuti “ndinena ndi inu khalani maso (Mariko 13:33,35). Anabwereza katatu ndi cholinga chakuti anthu amvetsetse uthenga ndikutengapo gawo.

 

 

 

 

Kuti mpingo utengepo mbali pothetsa mlili wa Edzi, ufunika  kuchita zinthu izi:

       I.            GWIRIZANO MUPINGO

Mpingo umakhala ndi magawo osiyanasiyana. Tsopano nthawi yafika  yakuti magawo onse ngati a Dayosizi, Madinale, Parishi ndi Miphakati komanso Mabungwe osiyanasiyana achikatorika agwire ntchito limodzi.

    II.            KUFIKILA MAGULU OYENELA KUDZELA MA PULOGALAMU

Kafukufuku waonetsa kuti theka la anthu omwe akutenga  matenda a HIV ndi achinyamata komanso kuti anthu am’mabanja ali pachiopsezo chotenga kachilomboka. Pakufunika  ma pulogalamu kuti afikire magulu a anthuwa. Tsopano  nthawi yakwana kuti mipingo ibweretse ma pulogalamu kuti athe kufikira anthuwa. Mwachitsazo kugwiritsa ntchito makina kuti athe kufikira achinyamata ndi uthenga wa HIV ndi EDZI.

 III.            KUGAWANA NDONDOMEKO ZA 90-90-90 MU MPINGO.

Ntchito ya mpingo wakatolika pa mlili wa HIV m’madera osiyanasiyana dzikoli ikupititsa chitsogolo njira zoyendetsera matenda a HIV ndi Edzi osangothera pakupanga njirazi. Ntchito yathu ikuyezedwa  pakukwanilitsa  zolinga  zathu  komanso pakuvomereza umunthu wa anthu amene ali ndi kachilomboka komanso omwe akhuzidwa ndi matendawa . Ntchito yathu ndiyofikira  anthu ndi chifundo komanso chithandizo kwa azimayi amasiye, ana amasiye, komanso anthu omwe ataya okondedwa awo kamba ka HIV ngati njira imodzi yokumbukira anatisiya kamba ka nthendayi.

Pamene tikufuna kukwanilitsa ndondomeko ya 90-90-90, tiyesetse kutseka mpata pakugonjetsa khalidwe  lolozana chala pa nkhani ya umphwawi, kusankhana ngakhaleso kutenga HIV. Anthu omwe anapezeka ndi kachilombo asamangokhala ndi mwayi wa makhwala okha komanso kukhala ndi moyo wangwiro ndi olomekezedwa, kuchotsa kusalana ndi kusankhana kwa athu amene ali ka chilombo.

Tikuitana magawo onse a mpingo monga ma Commission, Madinare, Maparishi, Miphakati ndi Mabugwe Achikatolika kuti aphatikize ndondomeko 90-90-90 muzochitika zawo.

V.CHIFUNDO NDI CHIKONDI

Monga mpingo, tikuyenera kuzindikira kuti “aliyese ndiwofunika kuthandizidwa”.  Ndi mawu amenewa Papa Francis akuyitana onse achikatolika ndi athu okhulupirira ndiso achifundo kuti atsegule mitima yawo kwa athu osowa kuti awathandize ngati abale awo. Akutiso kwa athu omwe akufuna kudzipeleka  pakupeleka nthawi, chuma, nzeru ndi maluso awo kwa athu ena kuti tikwanilitse zofuna za anthu ovutika.

Choncho tikuyitana ansembe ndi asisteri komanso akhristu  eni ake kuti tigwirane manja pothetsa mliliwu pofika chaka cha 2030. Tonse tigathe!

 

Wolemba

 

Mr. Carsterns Mulume                                               Mrs. Bertha Magomero

DIRECTOR OF SOCIAL DEVELOPMENT                     NATIONAL HEALTH SECRETARY

Papa Francisco Alimbikitsa Achinyamata Kuzamitsa Moyo wa Uzimu

$
0
0

Muuthenga  wachaka cha achinyamata chaka chino, mtsogoleri wampingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco, wapempha akhristu mumpingowu kuti azamitse  moyo wawo wauzimu poyeretsa mitima yawo.

Muuthengawu Papa Francisco, wapempha akhristu makanso achinyamata, kuti akumbukire zolinga zawo za nthawi zonse pomwe amafunitsitsa kukhala moyo osangalala, ndipo walangiza kuti akonze mitima yawo kuti ayanjane ndi Mulungu yemwe angawapatse chimwemwe chomwe amafuna nthawi zonse.

Mwambo okondwelera chaka cha achinyamata, umachitika patsiku lakanjeza chaka chilichonse mumpingowu padziko lonse, ndipo mpingowu, umasonkhanitsa achinyamata mdziko limodzi kuti akondwere limodzi pakatha zaka zinayi.

Mwambo omaliza wa chaka cha achinyamata unachitikira mumzinda wa Rio de Jenairo mdziko la Brazil mchaka cha 2013 ndipo mwambo otsatira,udzachikira mumzinda wa Krakow mdziko la Poland mchaka cha 2016.

Zigawenga za Boko Haram Zilepheretsa Zisankho Mdziko la Nigeria

$
0
0

Mtsogoleri wa gulu la zigawenga za Boko Haram Abubakar Shekau, wanenetsa kuti alepheretsa zisankho za atsogoleri zomwe dzikolo likuyembekezeka kukhala nazo pa 28 March chaka chino.

Iye wanena izi kudzera pakanema wina yemwe gululo latulutsa pambuyo pachiwembu chomwe gulolo lachita mdera lakumpoto chakumvuma kwa dzikolo.

Anthu 38 afa pachiwembucho.

Iye wanenetsa kuti chisankhocho, sichichitika ngakhale iye atamwalira lisanafike tsiku la zisankholo.

Boma la Nigeria lidavomereza kale kuti ntchito yovota, itha kudzakhaladi yovutirapo maka mdera la ku mpoto chamvuma komwe gululo lapha anthuwo  posachedwapa.

Mpingo wa Katolika ku Vatican Uganizira Anthu Osowa

$
0
0

Mpingo wa katolika ku Vatican wakhazikitsa malo ometera awulele a anthu osowa kwawo.

Pa mwambowu womwe unatsekuliridwa ndi mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco kunafika anthu ochuluka osowa kwawo kudzametetsa.

Anthu odzipereka ndi amene azigwira ntchito yometa anthuwa tsiku lolemba lililonse kamba koti pa tsikuli malo onse ometera mdzikolo amakhala otseka.

Izi zadza pambuyo pokhazikitsa malo omwe anthuwa azitha kukasambako omwe azikhala otsekula tsiku lililonse kupatula tsiku lachitatu lomwe mtsogoleri wa mpingo wakatolikayu amakhala akusonkhana ndi akhristu kudzanso alendo osiyanasiyana omwe amafika ku likulu la mpingowu.

Viewing all 1875 articles
Browse latest View live


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>