Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all 1875 articles
Browse latest View live

Akhristu 49 akuno ku Malawi ankhala nawo pa Mwambo wa Misa Wokumbukila Amariliti ku Ugunda

$
0
0

Akhristu 49 a mpingo wakatolika akuno ku Malawi, lachitatu anakhala nawo pamwambo wamapemphero okumbukira a maritiri 22 ku Namugongo Shrine mdziko la Uganda.

Mmodzi mwa amaritiriwa Charles Lwanga Oyera adaphedwa pa 3 June 1886 pomutentha, mfumu Mwanga ya mdzikolo yomwe inkadana ndi Chikhristu italamula kuti iye ndi anzake omwe adasiya moyo wachikunja ndikulowa Chikhristu aphedwe powatentha.

Malinga ndi mbiri yampingo Charles Oyera adakanitsitsa kusiya Chikhirisitu atakakamizidwa kutero ndipo panthawi yophedwa iye adathandizira kusonkhanitsa zipangizo zomwe anthu omwe adamutentha adagwiritsa ntchito pofuna kutsimikiza chikhulupiliro chake mwa Mulungu.

Paulendo wakumalo oyerawa akhristuwa akutsogoleredwa ndi bambo Bernard Tiyesi omwe amatumikira mu Arkdayosizi ya Blantyre.

 

 

 

 


Chiwelengelo cha Akhristu Achikatolika Chikukula

$
0
0

Lipoti lomwe nthambi yowona zakafukufuku pa sukulu ina ya ukachenjede mdziko la America yatulutsa lati chiwerengero cha akhristu a mpingo wakatolika padziko lonse chikukwera kwambiri maka mmaiko a mu Africa.

Lipotilo lati chiwerengerochi chakwera ndi 400 miliyoni padziko lonse kuyambira mchaka cha 1980.

Ilo lati ngakhale izi zili choncho chiwerengero cha akhristu amene akutsatira masakaramenti mumpingowu chikutsika.

Ndipo chifukwa cha kukwera kwa chiwerengero cha akhristuwa chiwerengero cha maparishi komanso ansembe chikuchepa.

Lipotili lati mpofunika kuti maanja alimbikitse ana kuvomera mautumiki osiyanasiyana mumpingowu ndicholinga choti akhristu adzithandizidwa mokwanira pankhani za masakaramenti.

Cadecom Inkhazikitsa Tchito Yonthandiza Anthu Mboma la Chikhwawa.

$
0
0

Dayosizi ya mpingo wakatolika ya Chikhwawa yati iwonetsetsa kuti ntchito za Bungwe lowona zachitukuko mumpingowu la CADECOM zikupindulira anthu onse mu Dayosiziyo.

Episikopi wa Dayosiziyi  wolemekezeka Ambuye Peter Musikuwa anena izi pamwambo wokhazikitsa ntchito yothandiza anthu kutukuka pa chuma, umoyo  ndinso kudzikonzekeretsa pa ngozi zogwa mwadzidzi.

“kunkhazikitsa kwa pulogaramu imeneyi anthu ambiri osowa chinthandizo alandila chinthandizo mokwanila ,pakutelo tikutukula miyoyo yawo komanso kutukula dziko lanthu.” Anatelo  Ambuye Musikuwa.

Iwo anapitiliza ponena kuti mpigo unankhazikisidwa ndi cholinga  chakuti munthu yense anthe kutukuka muuzimu ndi muthupi.

Ndipo Paramaunti Tchifi Lundu ya m’bomali inanthokoza bungwe la Cadecom ponkhazikitsa pulogaramuyi.

“Mu pulojekitiyi muli zinthu zingapo monga za Ulimi,jenda, Mabanki komanso za Umoyo, koma kwakukulu ndikunthetsa njala ,ndiye ife tailandila ndi manja awiri.” Anatelo A Lundu.

 Ndipo tchitoyi akuyitcha Ubale yomwe  idzitsogoleredwa ndi  bungwe la CADECOM mu Dayosiziyi.     

Apolisi M’dziko la New Guinea Akuwaganizira Kuti Apha Ophunzira Anayi Omwe Amachita Chionetsero

$
0
0

Apolisi m’dziko la New Guinea akuwaganizira kuti apha ophunzira anayi   a pa sukulu ina ya ukachenjede omwe amachita chionetsero chosonyeza kusakondwa ndi zochita za nduna yaikulu ya dzikolo.

Malingana ndi malipoti a wailesi ya BBC chionetserocho chinayambira ku sukulu yawo ndipo chinakathera ku nyumba yamalamulo ya dzikolo.

Ophunzira-wa ati akufuna kuti ndunayi itule pansi udindo wake kuti ikayankhe milandu ya ziphuphu ndi katangale.

Malipoti ati ndunayi ikukana kutula pansi udindo wake ndipo yati sikudziwapo kanthu pa nkhanizi.

Anthu Makumi Atatu Afa Zigawenga za Islamic State Zitaphulitsa Bomba La Timke Nawo

$
0
0

Anthu makumi atatu afa, ndipo ena 80 avulala  gulu la zigawenga la Islamic State litaphulitsa  mabomba awiri atinkenawo  munzinda wa Baghdad  m`dziko la Iraq

Malinga ndi malipoti awailesi ya BBC, bomba loyamba linaphulika m`dera la Shiandipo linapha anthu 19 pomwe bomba lina linaphulika  pamalo ena pomwe asilikali amachitira chipikisheni  a Taji kumpoto kwa mzinda wa Baghdad  ndikupha  anthu  11 kuphatikizapo asilikali.

Gulu la zigawengazi ati likupitiriza kuchita zamtopola  munzindawu pomwe asilikali adzikoli akulimbikitsa  ntchito  yolanda   maziko azigawengazi otchedwa  Falluja  omwe ali pamtunda wa makulomita 60 kumwera kwa mzinda wa Baghdad.

ECM Yasankha Bambo Likutcha Kukhala Mlangizi wa Apolisi

$
0
0

Bungwe la ma episkopi mdziko muno la Episcopal Conference Of Malawi [ECM] lasakha Bambo Steven Likhucha kukhala  mlangizi wa apolisi  mumpingowu m’dziko muno.

Bungweli  lanena izi kudzera muchikalata chomwe latulutsa ndipo chasainidwa ndi mlembi wa bungweli Bambo Henry Saindi.

Bambo Likhutchaalowa m`malo mwa Bambo David Bello, omwe anapuma zaka zawo zokhalira paudindowu zitatha.

Kalatayi yatinso Bambo Likhutcha omwe ndi wamsembe otumikira  ku dayosizi ya Zomba ayamba kugwira ntchito paudindowu pa 30 June chaka chino.

Kanyongolo Wapempha Boma Libwezeretse Maubale Ndi Maiko Ena

$
0
0

Katswiri wa malamulo yemwenso ndi mphunzitsi wa malamulo pa sukulu ya ukachenjende ya Chancellor, Professor Edge Kanyongolo wapempha boma  kuti libwezeretse ubale womwe unasokonekera pakati pa boma la Malawi ndi mayiko komanso mabungwe omwe amathandiza  dziko lino pa chuma.

Professor Kanyongolo wanena izi lachinayi poyankhula  ndi Radio Maria Malawi .

Iwo ati ndondomeko yachuma yachaka chino ipweteketsa anthu osauka chifukwa adzidulidwa nsonkho akagula katundu  wina aliyense.

A Kanyongolo ati dziko la Malawi silinafike podzidalira palokha pachuma chifukwa lilibe zinthu zoziyenereza monga migodi ndi makampani akulu akulu. Iwo ati dziko la Malawi limadalira fodya yekha pa chuma yemwenso sakuyenda bwino pa msika.

Kaswiri wa malamulo-yi wati boma liyenera kuvomereza kuti zinthu mdziko muno sidzilibwino pa chuma. Iwo ati zipatala za mdziko muno muli mavuto ambiri  monga kusowa mankhwala komanso kuchepa kwa ogwira ntchito ndipo wati izi zikusonyeza kuti boma lili pa mpanipani wosonyeza kuti lilibe chuma choyendetsera dziko.

Pa nkhani ya njala yomwe ili m’dziko muno Professor Kanyongolo wapempha boma kuti ligule chimanga chambiri kuti chizakwanire anthu onse omwe alibe chokudya. Iwo ati boma lisadzalowetse ndale podzagawa chimangachi koma chidzafikire aliyense.

Polisi ya Kanengo Iyenda Ulendo Wandawala Pofuna Kuzindikiritsa Anthu za Kuipa Kwa Mchitidwe Wopha M

$
0
0

Ngati njira imodzi yotenga  nawo gawo pa ntchito yothana ndi m`chitidwe wopha anthu a mtundu wa chi alubino, apolisi a Kanengomu m’zinda wa Lilongwe akonza  ulendo wa ndawala womwe cholinga chake ndikuzindikiritsa anthu za kuipa kwa m`chitidwe  wopha anthu-wa mdziko muno. 

M’neneri wa apolisi pa polisi ya Kanengo, mai Salome Chibwana, wati apolisi mogwirizana ndi anthu onse ozungulira Kanengo kuphatikiza omwe ndi ma alubino, a mipingo yosiyanasiyana asing’anga komanso azipani zonse za ndale ndiwo atenge mbali pa ulendowu.

Mutu wa ndawala-yi ndi woti “Apolisi sakugwilizana ndi mchitidwe wozembetsa Komanso Kuphedwa Kwa Anthu A Chi Alubino” Ulendowu ukayambira Pa Salima Turn Off kuzungulira Area 25 ku Lilongwe ndi kukamaliza ku polisi ya Kanengo , komwe kukakhale msonkhano womaliza wozindikilitsa anthu za kuyipa kwa mchitidwe-wu m’dziko muno.


Alshabaab Yapha Asilikali Makumi Anayi a AU ku Somalia

$
0
0

Gulu la zigawenga la  Al-Shabaab  lati lapha   asilikali okwana  makumi anayi  pachiwembu  chomwe linachita  kumalo a asilikali  a African Union   m`chigawo chapakati pa dziko la Somalia.

Bungwe la AUlatsimikiza za chiwembuchi ndipo  anthu omwe azungulira malowa ati anamva kulira kwa mfuti pa malowa. Asilikali abungwe la African Union akuthandiza asilikali adziko la Somalia kulimbana ndi guluri lomwe likulamulira madera osiyanasiyana m`dzikolo.

Dziko la Ethiopia ndi limodzi mwa maiko asanu omwe anatumiza asilikali ake m’dziko la Somaliakukathandiza pa ntchito yothana ndi zigawengadzi.

Mgwirizano wa Apolisi ndi Amalonda Ungapititse Patsogolo Chitetezo cha Dziko Lino

$
0
0

Chitetezo cha dziko lino ati chingalimbikitsidwe ngati pali ubale wabwino pakati pa apolisi ndi anthu amalonda.

Wachiwiri kwa mkulu wa apolisi ya Bvumbwe , SupretendantMoses Katanda walankhula izi ndi  Radio Maria  kwa Bvumbwe m’boma la Thyolo pambuyo pa mkumano wa apolisi ndi eni malo azisangalalo pa msika wa Bvumbwe.

Supretendant  Katanda wati ntchito yolimbikitsa chitetezo ndi ya wina aliyense kotero pakufunika umodzi pogwira ntchitoyi.

“Tikupempha onse amalonda kuti tigwirane manja. Akawona anthu okaikitsa kumalo awo a malonda azitidziwitsa chifukwa nthawi zambiri anthu okuba kapena ochita zauchifwambawa amapezeka mmalo awo omwera mowa akudikilira kuti akachite zaupandu,” anatero Supretendent Katanda.

A Katanda apemphanso eni malo azisangalalo wa kuti azikhala ndi ziphaso zochitira malonda awo.

Abungwe la Amayi Akatolika Akonzekere Bwino Msonkhano wa Padziko Lonse

$
0
0

Amayi ampingo wakatolika mdziko muno awapempha akuti adzipeleke pa ntchito yokonzekera msonkhano wawo wapaziko lonse umene udzachike mwezi wa September m’dziko muno.

Msonkhanowu ndi wa amayi pa dziko lonse ndipo wakonzedwandibungwe loyimira amayiwa laWorld Union of Catholic Women Organisationndipo chaka chino awukonza kuti uchitikire mdziko muno.

Pofotokozera Radio Maria Malawi m’modzi mwa atsogoleri akale a bungweli mu arkidayosizi ya Blantyre,mayiEmily Kapeta,ati amayi mdziko muno akuyenara kutenga msonkhanowu ngati madalitso akululu kamba koti uyika pa mapu mbiri ya mpingowu mdziko muno.

“Msonkhano taukonzekera bwino ndipo tikuwulandira ndi manja awiri. Tikupempha amayi apitirizebe kupereka ma K200 kuti tikwanitse kukonzekera bwino msonkhano umenewu kuti uzayende bwino,” anatero mayi Chipeta.

Iwo ati kupatula ndalama zomwe amayiwa akupereka kuti izathandizire pa msonkhanowu, bungweli lakonza ulendo wandawala ndi cholinga chofuna kuwonjezera ndalamazi.

Aka kakhala koyamba kuti msonkhanowu uchitikire mdziko muno. 

MOAM Ipempha Boma Liwunikenso Misonkho

$
0
0

Bungwe la eni minibus m`dziko muno la Minbus Owners Association of Malawi(MOAM) lapempha boma kuti liwunikenso  misonkho pofuna kuti ikhale yokomera anthu  ochita malonda ang’onoang’ono omwe ambiri ndimzika za  m`dziko lino.  Mlembi wa mkulu wa bungweli a Coxley Kamange wanena izi poyakhula ndi Radio Maria Malawi.

Iwo ati kuwunikanso misonkhoyi kuthandiza anthu ochita  malonda an`gonoan`gono  kuti asamathawe misonkho.

“Mukati muwonetsetse anthu ambiri amasiya ma biziness awo kuthawa misonkho yomwe ndi yokwera kwambiri mdziko muno.. Titakumana ndi anduna tinawapempha kuti atatsitsako misonkhoyi kuti izi zisamachitike koma mpaka pano sizikusintha. Boma likanatsitsako msonkho kuti mwina ukhale pa 10% zikanachita bwino, ifeyo ndi a Malawi ndipo dzikoli ndi lathu,” anatero a Kamange.

A Kamange anadandaula kuti a Malawi omwe ndi eni dziko akuvutika kupereka misonkho yambiri zomwe zikumachititsa kuti asamapeze phindu lochuluka pa bizinezi zawo pamene anthu ena obwera monga amwenye ndi maburundi akumachita chinyengo ndikusamalipira misonkho pamapeto pake akumapeza phindu lochuluka kuposa mzika za dziko lino.

Mkulu wa Bungwe la Community of Saint Egidio Mdziko Muno Wamwalira

$
0
0

Bungwe la Community of Saint Egidio lati lili mkati mokonza dongosolo la mwambo woyika m'manda yemwe anali mkulu wa bungweli m'dziko muno a Ellard Alumando.

Malemu-yi Ellard Alumando anamwalira masiku apitawa kuchipatala china m'dziko la South Africa ali mkati molandira thandizo , atakhuzidwa pa ngozi ya galimoto.

Pofotokozera Radio Maria Malawi m'modzi mwa amsembe otumikira bungweli m'dziko muno bambo Ernest Kafunsa ati pali chokonzero choti mwambo woyika m'manda thupi la malemu-yi udzachitika pa 21mwezi uno.

"Mwambo wa maliro udzachitika pa 21 June chifukwa pali alendo ochokera ku likulu lathu ku Italy omwe adzakhale nawo pa mwambowu. Amenenso adzatsogolere mwambowu ndi Bishop wa ku likulu lathu ku Vatican," anatero bambo Kafunsa.

A Kafunsa anati, "ngakhale kumudzi kwawo ndi ku Mangochi, a Allumando tiwayika ku Blantyre chifukwa ndi munthu amene wakhala akuthandiza anthu osauka ndi okalamba kwa nthawi yaitali . Iwowanso anali m'modzi mwa atsogoleri a gulu la Dream lomwe ntchito yake ndi kuthandiza anthu odwala matenda a Edzi ndi kuwapatsa mankhwala."

A Allumando anachita ngozi yagalimoto pa 28 December 2015 ndipo anapita ku chipatala china mdziko la South Africa komwe akhalako kufikira nthawi ino imene amwalira.

Achinyamata Azigwiritsa Bwino Ntchito Luso la Makono Pofalitsa Uthenga wa Mulungu

$
0
0

Achinyamata a bungwe la Young Christian Workers (YCW) mumpingo wa katolika  awalangiza kuti azigwiritsa  bwino ntchito maluso atsopano omwe akubwera mdziko muno  monga ma computer komanso internet pantchito yofalitsa mawu a Mulungukomanso kupezapo zinthu zokhuza maphunziro.

Bambo mfumu a parish ya Kadikira, Bambo Godferry Ntchera  anena izi  pa m`bindikiro watsiku limodzi  wa  achinyamata a YCW a dinale ya Limbe omwe unachitikira ku NantipwiriPastrol  Centre.

“Tikuwunikikira za utumiki wa achinyamata ngati mboni za Yesu Khristu m’masiku amakono ano. Cholinga ndi chakuti achinyamata ngakhale akumana ndi mavuto osiyanasiyana asafooke kapena kubwelera mmbuyo koma akhale ndi mtima opitiriza kutumikira. Iwowanso awathandize anzawo omwe sachita zachikhristu kuti atembenuke mtima ayambenso nawo kukhala mboni za Yesu Khristu chifukwa achinyamatawa ndi mchere komanso kuwala kowalira ena amene ali mu mdima,” anatero bamboo Ntchera.

Iwo ati achinyamata akusokonekera  kamba koti akumaonera zinthu zolaula ndi makhalidwe olakwika zomwe pamapeto pake zikumasokoneza  moyo wawo wanthupi ndi wauzimu.

M`mawu ake wapampando wa bungwe la YCWmudinaleyi LenardMataka wati kudzera mu m`bindikirowu achinyamata alimbikitsidwa zomwe ziwathandize kuthana ndi mavuto omwe amakumana nawo tsiku ndi tsiku komanso kukhala nyale za ena.

Ma Episkopi Apempha Mzika Kuti Zipempherere Dziko la Nigeria Pofuna Kuthetsa Katangale mdzikolo

$
0
0

Bungwe la ma episkopi mdziko la Nigeria la Catholic Bishops’ Conference of Nigeria lapempha  mzika za dzikolo kuti zipitilize kupemphelera dzikolo pofuna kuthana ndi mchitidwe wa katangale komanso ziwembu zomwe zikuchitika mdzikolo.

Bungweli lati ngakhale boma la dzikolo layesetsa kuchita chotheka kuti lithane ndi mavutowa, likuyeneranso kuti liwunikire mavuto omwe akuchitsa kuti anthu mdzikolo azikhala mwa mantha mmoyo wao wa tsiku ndi tsiku.

Malipoti a wailesi ya Vatican ati bungweli lapemphanso mzika za dzikolo kuti zikhale ndi udindo polemekeza malamulo a dziko akafuna kuthetsa mavuto omwe akumana nawo.

Bungweli lati ngakhale ndi udindo wa boma wopanga malamulo, anthu akuyenera kuzindikira kuti boma silingakwanitse kuyendetsa moyo wa munthu aliyense.


Boma Lati Lipereka Chilango Chokhwima kwa Opezeka ndi Mlandu Wopha ma Alubino

$
0
0

M’tsogoleri wa dziko lino Professor Arthur Peter Mutharika wati boma lake lionetsetsa kuti aliyense wopezeka ndi mulandu wakupha kapena kuchitira nkhanza anthu a mtundu wa chi Alubino m’dziko muno akulandira chilango chokhwima.

President Mutharika wanena izi lolemba m’boma la Kasungu pa mwambo wa tsiku loganizira anthu a chi Alubino.

Iye wati ndi wokhudzidwa kwambiri ndi kukula kwa mchitidwewu m’dziko muno.

“Ndikuthokoza nonse amene mwakhala mukutenga nawo mbali popereka malipoti a anthu oganizilidwa komanso omwe akhala akukhudzidwa ndi mchitidwe umenewu. Mupitirize kumadziwitsa apolisi koma chonde musatengere lamulo mmanja mwanu,” anatero Mutharika.

President Mutharika wapemphanso makolo omwe ali ndi ana a mtundu wa chi alubino kuti awasamalire ndi kuwateteza.

Nduna yoona kuti sipakukhala kusiyana pakati pa amuna ndi akazi pakagwilidwe ka ntchito, ana, olumala ndi chisamaliro cha wanthu, Dr. Jean Kalirani anayamikira m’tsogoleri wa dziko linoyu kamba kodzichepetsa ndi kukhala nawo pa mwambo woganizira tsikuli.

Polankhulanso pa mwambowu nthumwi ya bungwe la mgwirizano wa maiko onse la United Nations, mayi Sepa, ati dziko la Malawi likuyenera kuchita zomwe lingakwanitse pa ntchito zosamalira anthu a achi Alubino m’dziko muno, ndipo kuti thandizo la chipatala kwa anthuwa likuyenera kumapezeka mzipatala zonse maka zikuluzikulu za m’dziko muno mwa ulere.

Mwambowu patsikuli wachitika pa mutu woti “Tithetse nkhanza kwa anthu a chi alubino.”

Eye Of The Child Ikhazikitsa Bukhu Lozindikiritsa Mavuto Omwe Ana Amakumana Nawo

$
0
0

Bungwe la Eye ofthe Child m’dziko muno lalemba bukhu lomwe lili ndi mfundo zothandiza kuzindikira mavuto omwe ana amakumana nawo monga kugwililidwa mosavuta.

 

Polankhula ndi Radio Maria Malawi, mkulu wa bungweli m’dziko muno, a Maxwell  Matewere, ati bungweli laganiza zotulutsa bukhuli  ndi cholinga choti lithandize anthu mdziko muno kudziwa njira zoyenera kutsata kuti azitha kupereka chitetezo ndi chisamaliro chokwanira kwa ana kuti asamapezeke akukhudzidwa ndi mavuto ogwiliridwa amene akukolezera imfa zosiyanasiyana pakati pawo.

 

Iwo ati bukhuli alikhazikitsa lolemba pa 20 June mu m’zinda wa Lilongwe, mogwilizana ndi bungwe la FAWEMA  ndipo mledo wolemekezeka ku mwambowu ndi mkazi wa mtsogoleri wa dziko lino mayi Getrude Mutharika.

Dziko la Malawi Lichita Mwambo wa Tsiku Loganizira Mchitidwe Wogwiritsa Ana Ntchito

$
0
0

Dziko la Malawi lachisanu lichita mwambo wa tsiku loganizira m’chitidwe woyipa wogwilitsa ntchito ana (World Day Against Child Labour).

Dziko la Malawi lidzachita mwambowu pogwilizana ndi mayiko pa dziko lonse. M’tsogoleri wa dziko lino Professor Peter Muthalika ndi amene adzatsogolere mwambo woganizira tsikuli omwe wakonzedwa kuti udzachitikire mu mzinda wa Lilongwe.

Mutu wa chaka chino woganizira tsikuli, ukulimbikitsa anthu m’dziko muno kuti  adzipeleke pa ntchito zolimbana ndi m’chitidwe-wu, omwe ukuchitika m’mayiko pa dziko lonse.

Malingana ndi kalata yomwe a ku unduna wa za  ntchito,  achinyamata ndi zina, m’chitidwewu wafika pa 29% ukuchitika m’dziko muno, omwe ndi ma percent okwera kwambiri kusiyanasiyana momwe zinthu zikukhalira m’mayiko ena.

Bungwe lowona za antchito, la International Labour Organisationndi lomwe linakhadzikitsa tsikuli pofuna kulimbikitsa mayiko pa ntchito zolimbana ndi m’chitidwewu komanso kuwonetsetsa kuti ana akulandira chisamaliro ndi chitetezo chokwanira. 

Mfumu Kachule Ikulimbikitsa Maphunziro Kwa Ana Mdera Lake

$
0
0

Mfumu Kachule ya m’dera la mfumu yayikulu Kachere m’boma laDedza yati ipitiliza kudzipeleka pa chisamaliro ndi chitetezo cha ana a m’dera lake ndi cholinga choti azikhala ndi kukula ndi makhalidwe abwino.

Mfumu-yi yanena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi pamene inafika ndi kudela-li.

Mfumuyi yati zina mwa zomwe ikuchita polimbikitsa makhalidwe a tsogolo labwino kwa anawa ndi monga kuwalimbikitsa za ubwino wa maphunziro, komanso kulumikizana ndi makolo kuti asamalore anawa kupezeka m’malo omwera mowa.

“Ndimalimbikitsa kuti ana asukulu mdera langa asamapezeke mmalo omwera mowa komanso kuti azikhala olimbikira sukulu. Makolo ndimawauza kuti tithandizane pancthitoyi chifukwa mphunzitsi wamkulu ndi kholo,” anatero Mfumu Kachule.

Bungwe la Episcopal Conference of Malawi Liri ndi Mlembi Watsopano.

$
0
0

Mlembi watsopano wabungwe la maepiskopi mdziko muno la Episcopal conference of Malawi Bambo Henry Saindi ati apitiliza kudzipereka potumikira Mulungu pogwiritsa ntchito mphatso zomwe ali nazo pofunanso kuthandiza anthu ena kupyolera muudindo womwe asankhidwa.

Bambo Saindi anena izi lero polankhula ndi Radio Maria Malawi yomwe imafuna kumva momwe iwo awulandilira udindowu.

Iwo ati nthawi zina anthu amaganiza kuti kukhala paudindo waukulu ndi chiphinjo pa moyo wa munthu ,koma iwo ati nkhani ya udindo amaiwonera mbali ziwiri mbali yoyamba ndichinthu cholemela pamene mbali ina tintha kuwona udindo ngati mwayi umene munthu walandila ndicholinga choti atenge nawo mbali  awonese mphatso imene ali nayo ponthandidza anthu ena ponthandidza mpingo komanso mbali zina.  

“Ine poyamba ndikufuna kuthokoza Mulungu amene kupyolela Mbungwe la Episcopal Conference of Malawi wandiona kuti ndine woyenela kunkhala pa udindo umenewu”.

Iwo anapitilidza kunena kuti ngati tichita bwino ndi Mulungu amene amatinthandidza kuti tikwanilise, ndipo ndimulungu yemweyo wandiyetsa kuti ndine woyenela.

 Kalata yotsimikiza Bambo Henry Saindi kunkhala Mlembe wa bungweri yatuluka lachinayi.

Viewing all 1875 articles
Browse latest View live


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>