Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all 1875 articles
Browse latest View live

Boma la Iraq Lalanda Nyumba Momwe Mumakhala Zigawenga za Islamic State

$
0
0

Boma la dziko la Iraq lalanda nyumba yake yomwe mumapezeka zigawenga za chisilamu za Islamic State mu mzinda wa Fallujah mdzikolo.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC akuluakulu a gulu la zigawengazi achoka m’nyumbayo potsatira kumenyana kwa pakati pa asilikali a boma a dzikolo ndi zigawengazi.

Malipoti ati boma la dzikolo linakhazikitsa kumenyana kwa pakati kwa magulu awiriwa pofuna kulanda mzindawo omwe wakhala uli mmanja mwa zigawengazi kwa nthawi yaitali.


Chipatala cha Dedza Chapempha Mafumu Kuti Alimbikitse Uchembere Wabwino

$
0
0

Chipatala cha boma cha Dedza chapempha mafumu kuti apitilize kulimbikitsa amayi oyembekezera kuti azichilira ku chipatala.

Ofalitsa nkhani za chipatalachi, a Alnod Ndalira, wanena izi potsekulira misonkhano yozindikilitsa anthu za uchembere wangwiro pa chipatala cha Chikuse ndi m’mudzi mwa Kadowera m’dera la mfumu yayikulu Kasumbu  m’bomalo.

Ofalitsa nkhani za chipatalayu wati ntchito-yi yomwe imathandiza amayi ndi ndalama pomwe ali oyembekezera ithandiza kuchepetsa imfa za amayi oyembekezera m’bomalo.

“Tili ndi ndondomeko yomwe timati Conditional Cash Transfer imene amayi amalandirako ndalama pamene abwera kuzachilira ku chipatala ngati kuwabwezera transport komanso nthawi imene akukhalira kuchipatala chiofukwa amakhala kuchipatala kwa masiku osachepera awiri kuti adokotala awawone bwinobwino kuti mwana wachira mopanda vuto ndi cholinga chochepetsa imfa za amayi ndi makanda,” anatero a Ndalira.

Iwo ati pakadali pano chipatalachi chikugula zipangizo zoyenelera pofuna kuwonetsetsa kuti amayi azichira mopanda vuto lililonse.

Bungwe la YODEP Likukhazikitsa Mabungwe Othana ndi Nkhanza kwa Ana ndi Amayi

$
0
0

Bungwe la Youth Development and Productivity (YODEP)m’boma la Zomba  lati ntchito yokhazikitsa ma bungwe a abambo omwe akhale akuteteza amayi ndi ana ku nkhanza zosiyanasiyana ikuyenda bwino.

Mmodzi mwa akuluakulu ku bungweli a Joy Mwandama ndi omwe anena izi polankhula  ndi Radio Maria Malawi.

 Iwo ati padakali pano magulu 77 akhazikitsidwa kale kwa mfumu yaikulu  Mbiza ndi Mwambo ndipo ayamba kale maphunziro.

Maphunzirowa ati athandiza abambo kuti awoneke  mwatsopano pokhala patsogolo kuteteza amayi ndi ana ku nkhanza zomwe zikumakolezera matenda a Edzi.

Ntchitoyi akuyigwira ndi thandizo lochokera ku bungwe la UN-AIDS kuchokera mdziko la  South Africa.

Ambuye Msusa Ayamikira Akhristu a Parishi ya Bvumbwe

$
0
0

Akhristu a mpingo wakatolika mu arkidayosizi ya Blantyre awayamikira kamba kochilimika pa zampingo wodzidalira pomwe akugwira ntchito za chitukuko m`maparishi awo.  

Arkiepiskopi wa dayosiziyi, Ambuye Thomas Luke Msusa, anena izi pa mwambo wansembe ya misa  yodzodza  adikoni awiri a mu dayosiziyi kukhala ansembe achipani cha Montfort ku parish ya Bvumbwe komanso pomwe parishiyi imakondwerela  nkhoswe yake yomwe ndi Amalitiri Oyera a ku Uganda.

Ambuye Msusa ayamikira  akhristu a Parishiyi omwe amanga  Goloto lokongola pa iwo wokha osadalira  thandizo lakunja zomwe ati zachitika  kamba kakudzipereka kwawo.

“Ndikuthokoza atsogoleri a parishi ino ya Bvumbwe mogwirizana ndi atsogoleri a arkidayosizi chifukwa chotenga dzina la kudzidalira ndi kuliyika m’manja mwanu.

Iwo anayamikira anayamikira akhristuwa kamba kovomera pempho la a Papa chaka chino pamene tikukondwelera chaka cha chifundo,”anatero ambuye Msusa.

Pomaliza Ambuye Msusa alangiza akhristu kuti athandize ansembe omwe adzozedwa kumenewa powapempherera ndi kuwapatsa zosowa zawo.

 

Ambuye Stima Ayamikira Ophunzira Akale a Sukulu ya St. Paul The Apostle

$
0
0

Anthu omwe anaphunzira pa seminale yaying’ono ya St. Paul the Apostle, mu dayosizi ya Mangochi ya mpingo wakatolika, awayamikira kamba kotengapo gawo popititsa patsogolo chitukuko cha dayosiziyi.

Episkopi wa dayosiziyi, Ambuye Montfort Stima, wanena izi loweruka pa mwambo wokondwerera nkhoswe ya seminaleyi yomwe ndi Paulo Woyera.

Iwo ati ndi udindo wa ophunzira omwe anaphunzira mu sukulu za mu dayosiziyi monga St. Paul kutukula sukulu komanso dayosiziyi.

“Ophunzira amene anaphunzira pa seminale imeneyi ena ndi ansembe komanso ena akugwira ntchito zosiyanasiyana tikuwakumbutsa kuti nthawi imene amachoka pa seminaleyi mpingo unali m’manja mwa azungu zimene zikutanthauza kuti chilichonse amachita ndi azungu. Koma lero tsopano mpingowu uli mmanja mwathu ifeyo eniake achikuda. Choncho tikuwapempha kuti ngakhale akukhala kutali ndi seminaleyi komanso dayosiziyi tikuwapempha kuti ndi luso lawo losiyanasiyana lomwe ali nalo athe kuthandiza mpingowu mu dayosiziyi,” anatero Ambuye Stima.

Iwo anati, “Tikudziwa kuti ena amadandaula nkhani ya ndalama koma kuthandiza sikulira ndalama zokha ayi koma ngakhalenso luso lomwe ali nalo atha kuthandiza dayosiziyi.”

Polankhulapo wapampando wa gulu la anthu omwe anaphunzira pa seminale-yi, a Montfort Howahowa, ayamikira mgwirizano omwe ulipo pakati pa ophunzira akalewa omwe wathandiza kutukula ntchito za bungweli komanso mwa zina   kutukula sukuluyi ngakhalenso dayosiziyi.

“Titamva kuti dayosizi yakonza mwambowu, tonse omwe tinaphunzira pa sukuluyi, tinalumikizana ndi kusonkha pang’onopang’ono mpaka zinakwana zoti tayendetsera mwambo onsewu,” anatero a Howahowa.

Iwo ati ndi okonzeka kuthandiza dayosizi ya Mangochi ngati njira yoyankhirapo pempho lomwe episkopi wa dayosiziyi wapereka pozindikira kuti dayosiziyi ili pa mavuto aakulu komanso ngati njira imodzi yobwezera ulemu womwe dayosiziyi inawapatsa pa nthawi imene anali pa sukuluyi.

 

 

 

Bungwe la FAWO Lati Amayi Amasiye Akhale Odzidalira

$
0
0

Bungwe lomenyela ufulu wa amayi ndi ana amasiye mdziko muno la Foundation for Widows and Orphans (FAWO) lati nthawi yakwana yoti amayi amasiye akhale odziyimira pawokha pa nkhani za chuma.

Polankhula  ndi Radio Maria Malawi mu mzinda wa Blantyre, pokonzekera mwambo wa tsiku loganizira ufulu wa amai amasiye pa dziko lonse lapansi, omwe udzachitike pa 28 June mu mzinda wa Blantyre, mkulu wa bungweli a Kenneth Chipeta wati  ngati amayiwa akhale odziyimilira pawokha pa chuma atha kukhala  ndi kuthekera kothandiza ana omwe asiyilidwa.

“Ana ndi amayi ambiri amadalira bambo amene amakhala akuchita business kapena kugwira ntchito. Ndiye nthawi zambiri bambo akamwalira umakhala ngati mzati wagwa chifukwa ndi amene amakhala akuthandiza banja lake. Udindo wonse tsopano umakhala m’manja mwa mayi wotsala uja monga kulipira sukulu, zovala, chakudya ndi zina zambiri. Ndiye amayi chifukwa amakhala alibe chochita amavutika kwambiri,” anatero a Chipeta.

A Chipeta ati zikhalidwe za dziko lino monga kulowa kufa zikuyika miyoyo ya amaiwa pachiswe. Iwo apempha kuti anthu asamawagwiritse ntchito amayi amasiyewa chifukwa ndi ovutika.

Iwo ayamikira boma ponena kuti likuwonetsa chidwi pa mwambo womwe bungweli likhale nawo posachedwapa komanso makamaka kuti likufuna litagwira ntchito limodzi ndi bungweli pofuna kuthetsa mavuto amene amayi amasiye amakumana nawo.

 

 

 

Papa Wati Chilango cha Kupha ndi Chosayenera

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Fransisko wati chilango chakupha ndi chosayenera kamba koti munthu aliyense ali ndi ufulu wokhala ndi moyo.

Papa amalankhula izi potsatira msonkhano waukulu wa padziko lonse wa chisanu ndi chimodzi omwe uli mkati wofuna kuthetsa chilango chakupha omwe ukuchitikira mdziko la Norway.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican, Papa Fransisko wati ndi ntchimo lalikulu kupereka chilango chakupha kwa munthu ngakhale atakhala kuti wapalamula mlandu  waukulu.

Papa wapempha nthumwi ku msonkhanowu kuti zikambiranenso za chisamaliro chabwino m’ndende zosiyanasiyana za pa dziko lonse.

Nyumba Zosindikiza Ndi Kuwulutsa Nkhani Zizilemba Mwaukadaulo Nkhani Zokhudza Anthu Olumala

$
0
0

Nyumba zotsindikiza ndi kuwulutsa nkhani mdziko muno azilimbikitsa kuti zizifufuza mokwanira komanso kulemba mwaukadaulo nkhani zokhudza anthu olumala.

Wachiwiri kwa mkulu wa nthambi yophunzitsa zamalamulo pasukulu ya ukachenjede ya Chancellor, a Teleza Chome anena izi pambuyo pa pamaphunziro a tsiku limodzi  a atolankhani okhudza maufulu a anthu olumala omwe anachitikira m’boma la Zomba.

Iwo ati atolankhani akuyenera kutengapo gawo popereka uthenga kwa a Malawi pofuna kuonetsetsa kuti maufulu a anthu olumala akulemekezedwa komanso kutetezedwa.

Maphunzirowa anachitika pansi pa mutu oti “Maufulu a anthu olumala: Uthenga ofunika kwa anthu onse” ndipo anachitika ndithandizo landalama lochokera ku bungwe la OSISA.

M’mau ake, mmodzi mwa amene amaphunzitsa atolankhaniwa, Dr Elizabeth Kamchedzera, anati atolankhani akuyenera kusankha bwino mau otchulira anthu amene ali ndi ulumale osiyanasiyana popewa kunyazitsa ndikupereka chithunzi cholakwika cha anthu oterewa.

M’modzi mwa amene amachititsa nawo maphunzirowa yamwenso ndi magistrate ku bwalo la milandu la Zomba, a Rhodrick Michongwe anatsindika kunena kuti nkhondo yolimbana ndikuteteza ufulu wa anthu olumala singayende bwino popanda kugwira ntchito limodzi ndi atolankhani.


PRO-LIFE Yati Kupha ma Alubino ndi Kutsutsana ndi Cholinga cha Mulungu

$
0
0

Bungwe loteteza miyoyo ya anthu la mpingo wa katolika la PRO-LIFE lati kupha anthu a mtundu wa chialubino ndi kutsutsana ndi cholinga cha Mulungu kaamba koti iye analenga munthu aliyense m’chifaniziro chake.

Mkulu woyendetsa ntchito za bungweli, bambo Alpheus Dzikomankhani, anena izi pofotokozera Radio Maria Malawi pomwe imafuna kudziwa dongosolo lomwe bungweli lakhazikitsa pofuna kuteteza miyoyo ya anthu  a mtunduwu.

“Kuphedwa kwa alubino ndi chimodzimodzi ndi kuphedwa kwa munthu wina aliyense chifukwa alubino ndi munthu wolengedwa ndi Mulungu monga alili munthu wina aliyense choncho kuphedwa kwa munthu aliyense ndi tchimo lalikulu pa maso pa Mulungu ndipo ndizosayenera,” anatero bambo Dzikomankhani.

Bambo Dzikomankhani apempha anthu mdziko muno kuti apemphere kolimba kuti agonjetse mchitidwewu.

“Pano tikudziwitsa anthu za kusamala moyo wa munthu kufikira pamene wamwalira. Pamene tikuchita zosayenera monga kupha alubino ndiye kuti moyo wa Mulungu wachoka mwa ife siifenso chifaniziro cha Mulungu ndipo ndiye kuti moyo wathu ndi chimodzimodzi ndi wa nyama,” anatero bambo Dzikomankhani.

Pamenepa Iwo apempha ma bwalo oweruza  milandu kuti apitilize kupereka zilango zokhwima kwa munthu aliyense opezeka ndi olakwa pa mlanduwu.

Mpingo Wakatolika Wati Pasakhale Lamulo Lakupha Munthu Wopha ma Alubino

$
0
0

Mpingo wa katolika mdziko muno wati ukugwirizana ndi ganizo la boma loti pasakhale lamulo lakupha  munthu wopezeka olakwa pa mlandu wosowetsa komanso kupha anthu a mtundu wa chialubino.

Mlembi wa mkulu ku bungwe la ma episkopi  mdziko muno la Episcopal Conference of Malawi (ECM), bambo Henry Saindi anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi.

Bambo Saindi ati mpingo wa katolika umalemekeza ufulu wokhala ndi moyo wa munthu aliyense ndipo suvomereza kuti munthu aphedwe ngakhale atapezeka wolakwa.

“Posachedwapa Papa Fransisko watsindikanso za ufulu ndi ulemelero wa moyo wa munthu kuti palibe amene ali ndi ufulu wochotsa moyo wa munthu wina ngakhale atakhala kuti munthuyo wapha mzake,” anatero bambo Saindi.

Iwo anati, “Mpingo ukugwirizana ndi ganizo la boma loti nkosayenera ndipo nkosaloredwa kuti boma lizipereka lamulo lonyonga kwa anthu amene apezeka ndi mlandu wopha kapena kuzembetsa ma ulubino.”

Bambo Saindi apempha anthu mdziko muno kuti akaneneze ku polisi munthu amene wapezeka akuchita mchitidwewu osati kupha komanso apempha mabwalo a milandu kuti azipereka chigamulo choyenera kwa anthu opalamula mulandu wotere.

YCW Ikutolera Thandizo la Seminale Ya St. Peters

$
0
0

Bungwe la achinyamata mu mpingo wakatolika m’dziko muno la Young Christian Workers (YCW) lati likutolera thandizo pofuna kuthandiza seminale yaikulu ya St. Peters mu dayosizi ya Zomba yomwe padakali pano ikukumana ndi mavuto azachuma.

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa bungweli mdziko muno, a Chrispin Ngunde anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi.

“Anatidziwitsa kuti seminaleyi ili ndi mavuto azachuma ndipo pa budget yawo ya chaka chino kuti amalize semester yomwe ikutha mu july muno ikusoweka 8 million kwacha ndipo tinavomera kuti titengapo gawo,” anatero a Ngunde.

A Ngunde ati ndi udindo wa achinyamata mu mpingo komanso akhristu eni ake kutengapo gawo pothandiza mpingo mu njira zosiyanasiyana pa nthawi yomwe ukukumana ndi mavuto.

“Mkhristu aliyense atha kutengapo gawo pothandiza mpingo kudzera munjira zosiyanasiyana zimene mpingowo watipempha. Sitingachite zonse ayi koma tithe kutengapo gawo lochepa lomwe tingakwanitse. Zimenezi zitha kuthandiza kuti mpingo wathu upite patsogolo ndiponso mpingo uthe kutifikira ife akhristu ndi kutithandiza monga tifunira kutinso tikathe kulandira mphotho yomwe mkhristu aliyense amayifuna yopita kumwamba,” anatero a Ngunde.

CCJP Yadzudzula Aphungu Ena Kamba Kosamapita Kunyumba Ya Malamulo

$
0
0

Bungwe la mpingo wakatolika la chilungamo ndi mtendere la Catholic Commission for Justice and Peace (CCJP) ladzudzula aphungu a ku nyumba ya malamulo kamba ka chisankho chomwe ena mwa iwo akuchita chosapita ku nyumbayi ati zomwe ndi kunyozera ufulu wa anthu woyenera kukhala ndi chitukuko.

Yemwe akuyimilira mkulu wa bungweli ku likulu la mpingo wa katolika mdziko muno la Episcopal Conference of Malawi (ECM), a Martin Chiphwanya walankhula izi kudzera mu uthenga omwe bungweli latulutsa potsatira kusapita kwa aphunguwa ku nyumba ya malamulo.

Iwo ati aphunguwa akuyenera kuzindikira kuti anasankhidwa ndi anthu a m’madera omwe amachokera kuti aziwayimilira ku mavuto omwe akukumana nawo.

Boma Latsimikiza Kuti Zitukuko Zitha Posachedwa M’boma La Machinga

$
0
0

Anthu a m’madera a mafumu a Chiwalo komanso Kapoloma m’boma la Machinga awatsimikizira kuti zitukuko zomwe zikugwiridwa m’madera awo zifika kumapeto posachedwapa.

Nthandizi wa nduna ya za nyumba ndi malo, a Charles Nkozomba, alankhula izi ndi Radio Maria Malawi poyankhapo ena mwa madandaulo omwe anthu a derali anadandaula kaamba ka kuchedwa kutha kwa zitukuko ngati milatho ndi sukulu.

A Nkozomba ati zitukukozi zachedwa kutha kaamba koti ndalama zogwilira ntchitoyi zikuchokera ku thumba la chitukuko cha mdera la phungu lotchedwa Constituency Development Fund (CDF)zomwe zimaperekedwa pang’onopang’ono.

“Zitukuko zomwe tinagwirizana chaka changothachi ndi zoti timanga zipatala za ana (under 5 clinics) komanso timanga ma milatho. Ntchitoyi yatenga nthawi yaitali kamba koti ndalama zomwe timagwiritsa ntchito za CDF zimabwera moduladula. Ndiye ngati tili ndi zitukuko zingapo ndalama zija timaika uku pang’ono kwinanso pang’ono zimene zimachititsa kuti zitukukozi zizichedwa,” anatero a Mkozomba.

Iwo ati ali ndi chikhulupiliro kuti zitukuko zonse zomwe zinalonjezedwa chaka chikuthachi zikhala zitata masabata awiri akudzawa pamene dongosolo la ndalama latsopano a boma liziyamba.

TEVETA Yati Ntchito Zake Zotolera Msonkho Ziyamba Kuyenda Bwino

$
0
0

Bungwe la Technical Interprenual Vocational Education and Training Authority (TIVETA) lati ntchito yake yotolera misonkho iyamba kuyenda bwino kaamba ka mgwirizano omwe bungweli wasayinirana ndi bungwe lotolera misonkho la Malawi Revenue Authority (MRA).

M’modzi mwa akuluakulu a bungweli a Willison Makulumiza Nkhoma alankhula izi lachinayi ndi Radio Maria Malawi mu mzinda wa Lilongwe pomwe mabungwe awiriwa amasayinirana mgwirizanowu.

Iwo ati mgwirizanowu uthandiza kufikira anthu ambiri mdziko muno omwe amayenera kupereka misonkho ku bungwe lawo.

“A MRA akamatolera ndalama aziika ndalama zija mu account yathu ndipo ifeyo ndi amene tili ndi mphamvu yokachotsamo ndalama zija osati MRA,” anatero a Nkhoma.

Poyankhulaponso m’modzi mwa akuluakulu ku bungwe lotolera msonkho mdziko muno la Malawi Revenue Authority (MRA), a Steven Kapoloma anati bungwe lawo pa mgwirizano umenewu ntchito yake ndi yongotolera msonkho m’malo mwa bungwe la TIVETA.

“Pamene tagwirizana kuti ife a MRA tizitolera msonkho m’malo mwa iwo (TIVETA)udindo wathu wagona poonetsetsa kuti wolemba ntchito aliyense abwere ku MRA kudzalembetsa msonkho ndi kuyamba kulipira msonkho wa dziko. Chinanso ndichowadziwitsa kuti aphunzire kumawonkhetsa okha msonkho umenewu wa TIVETA,” anatero a Kapoloma.

Atumiki a Radio Maria Malawi Awapempha Akhale Olimbikira Pofalitsa Uthenga wa Mulungu

$
0
0

Anthu omwe amagwira ntchito modzipereka ku Radio Maria Malawi awalimbikitsa kuti asamabwelere m’mbuyo pomwe akukumana ndi zovuta pa nthawi yomwe akutumikira.

Bambo Edwin Lambulira alankhula izi loweruka  pambuyo pa  m’bindikiro wa anthu omwe amatumikira ku likulu la  wailesiyi ku Mangochi omwe unachitikira ku malo ogona alendo a Namiyasi mu dayosizi ya Mangochi ya mpingo wakatolika.

Iwo ati pa nthawi yomwe akukumana ndi zovuta akuyenera kupemphera kwa Mulungu kuti awatsogolele komanso kuwapatsa chilimbikitso.

“Nthawi zambiri anthu otumikira Mulungu akakumana ndi chinthu choti samachiyembekezera amabwelera m’mbuyo choncho ndinawona kuti ndikwabwino kuti tithandizane popemphera pa tsiku la lero. Ndawapempha kuti zisathere pakulankhula chabe koma azichite ndithu choncho azabala zipatso zochuluka,” anatero bambo Lambulira.

Pamenepa Bambo Lambulira apempha atumikiwa kuti nthawi zonse pamene akufalitsa uthenga wabwino kudzera pa wailesi, iwonso aziwonetsa chitsanzo chabwino kwa ena.

M’modzi mwa achinyamata otumikira ku Radio Maria Malawi yemwe anachita nawo m’bindikirowu a Gabriel Brome anati aphunzilapo kuti pamene akupita kowulutsa mau azikhala atazikonzekera bwino komanso iwowo azikhala chitsanzo chenicheni cha zomwe akuyankhula pa wailesi.

M’bindikirowu unachitika pa mutu wakuti “Kodi nanga inuyo simuchokanso?” Mau ochokera pa Yohane mutu  6 ndime ya 59 kulekezera 69.


Msonkhano wa PMS Watha Lachisanu

$
0
0

M’sonkhano waukulu wa masiku anayi wa atsogoleri oyendetsa ma bungwe a utumiki wa a Papa m’ma dayosizi onse ampingo wakatolika mdziko muno watha lachisanu.

Polankhula pambuyo pa msonkhanowu omwe unachitikira mu dayosizi ya Mzuzu, mkulu wa bungwe loyendetsa mabungwe-wa mdziko muno la Pontifical Mission Societies (PMS),Bambo Vincent Mwakhwawaati ku msonkhanowu akambirana za misonkhano komanso miyambo yomwe ikuyembekezeka kuchitika kutsogoloku monga maphunziro a aphunzitsi a utumiki wa ana komanso chaka cha chibalalitso.

Iwo ati pa msonkhanowu awunikirananso momwe angagwilire ntchito ngati atsogoleri m’madayosizi awo.

Polankhulapo m’modzi mwa atsogoleri omwe anali nawo pa msonkhanowu omwenso angosankhidwa kumene pa udindowu, Bambo Paul Rappozo, ati msonkhanowu wawapindulira kamba koti mfundo zomwe akambirana ziwathandiza kutumikira bwino pa udindowu.

Papa Walimbikitsa Ubale wa Mpingo wa Katolika ndi Orthodox

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Fransisko wapempha kuti mgwirizano omwe ulipo pakati pa mpingowu ndi mpingo wa Orthodox upitilire kuyenda bwino.

Papa amalankhula izi la mulungu mdziko la Armenia pambuyo pa mwambo wa nsembe ya misa yomwe anachitira limodzi ndi mpingo wa Orthodox pa ulendo wake wa masiku atatu wokacheza mdzikolo.

Papa anayamikira mtsogoleri wa mpingo wa Orthodox mdzikolo a Catholicos Karekin kamba ka chikondi chomwe wamuwonetsera pa ulendo wake wokayendera dzikolo.

Malipoti a wailesi ya Vatican ati Papa anali okondwa kamba koti apemphelera limodzi, agawana mphatso komanso mfundo zofuna kupititsa patsogolo mipingoyi.

Mpingo Wa Anglican Wadzodza Ansembe Atatu

$
0
0

Mpingo wa Anglican mu dayosizi ya Upper Shire loweruka wadzoza madikoni atatu kukhala ansembe.

Polankhula pa mwambowu Episkopi wa dayosiziyi Ambuye Brighton Vita Malasa ayamikira ansembe atsopanowa podzipereka kutumikira Mulungu kudzera mu njira ya unsembe.

Iwo ati pozindikira kuti ansembe akusowa, apempha atumiki atsopanowa kuti akalimbikire pa utumiki wao kulikonse komwe atumidwe kukatumikira.

“Lero ndi tsiku lalikulu muno mu dayosizi ya Uppershire lomwe timadzodza ansembe atatu atsopano omwe akatumikire ma parishi osiyanasiyana kugwira ncthito ya Mulungu chifukwa ndi Iye amene waatuma. Tikuthokoza Mulungu kuti anyamata amenewa adzipereka komanso kuti watipatsa ife mphatso ya atumiki amenewa chifukwa masiku ano ansembe akuchepa ndipo akusowa,” anatero Ambuye Malasa.

Poyankhulapo yemwe anali mlendo wolemekezeka patsikuli yemwe ndi nduna ya zofalitsa nkhani ndikuphunzitsa anthu, Mayi Patricia Kaliati MP, ati mpingo wa Anglican umathandizana ndi boma potumikira anthu ake choncho anapempha mpingowu kuti upitirize kuthandiza boma pa ntchito za chitukuko mdziko muno.

“Boma limagwira ntchito ndi mpingo wa Anglican komanso mipingo yonse imene ili mdziko muno choncho tawona chofunikira kuti tichite nawo mwambowu ngati njira imodzi yowathokozera pa zinthu zomwe amatichitira monga kumanga zipatala, sukulu ndi zitukuko zina. Tikuwapempha kuti apitirize ulaliki wawo pa dziko lonse lapansi kuti pakutha pa moyo uno tikalandire kolona,” anatero Mayi Kaliati.

A Kaliati anati, “Ansembe atsopanowa tawapempha kuti apite akalalike monga anachitira ambuye athu Yesu Khristu komanso akamange mabanja ndikupereka ulangizi waukulu kuti akhale mabanja amene Mulungu akakondwere nawo.”

Zigawenga za Boko Haram Zapha Anthu Pafupifupi 150 Sabata Ino

$
0
0

Zigawenga za Boko Haram zapha anthu pafupifupi zana limodzi ndi makumi asanu sabata ino mchigawo cha Borno mdziko la Nigeria.

Anthu omwe awona izi zikuchitika awuza wailesi ya BBC kuti anthu a mfuti analowa mmudzi wina omwe uli pafupi ndi nyanja ya Chad lachitatu ndikupha anthu 97 kuphatikizapo amayi ndi ana.

Anthu ena 48 aphedwa lachiwiri atangomaliza mwambo wamapemphero omwe anali nawo mmidzi ina iwiri mdera lomwelo koma pa chiwembuchi amayi anasiyidwa.

Anthu ena afa paziwembu zosiyanasiyana zomwe zakhala zikuchitika mdzikolo musabata ino kufikitsa chiwerengero cha anthu omwe aphedwa musabata yokhayi pa 150.

Padakali pano malipoti a bungwe lomenyera ufulu wa anthu padziko lonse la Amnesty International akusonyeza kuti anthu 17 sauzande ndi omwe aphedwa ndi zigawengazi kuyambira mchaka cha 2009 pomwe zidayamba mtopola mdzikolo pofuna kukhazikitsa boma laulamuliro wa chisilamu

Mpingo wa Anglican Ukuphunzitsa Anthu za Kuyipa Kozembetsa ndi Kupha ma Alubino

$
0
0

Mpingo wa Anglican mdziko muno wati wayamba ntchito yophunzizitsa ndi kudziwitsa anthu za kuyipa kwa mchitidwe wopha ndi kuzembetsa anthu a mtundu wa chi alubino womwe padakali pano wakula mdziko muno.

Episkopi wa mpingowu wa dayosizi ya Upper Shire, Ambuye Brighton Vita Malasa anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi pomwe imafuna kudziwa zomwe mpingowu ukuchita pofuna kuteteza miyoyo ya anthu amtunduwu.

Ambuye Malasa ati anthu a mtunduwu sakuyenera kusalidwa koma akuyenera kuwonetseredwa chikondi pofuna kusonyeza kuti iwo si osiyana ndi wina aliyense.

 “Tayamba posachedwapa ma awareness, kuwadziwitsa anthu za zakuyipa kwa mchitidwewu. Ndikuwona kuti chimene chikusowa ndi chikondi. Zikanakhala bwino tikanamakondana wina ndi nzake. Ma alubino ndi anthu ngati ife tomwe, analengedwa mchifaniziro chake (Mulungu). Titati tibwerezeretse chikondi dziko lathu liyenda bwino. Ndipemphe  boma, apolisi komanso aliyense wa ife kuti atengepo mbali pothetsa mchitidwe umenewu. Anthu asachite kukhala akapolo mdziko lawo lomwe kumalephera kugwira ntchito zawo,” anatero Bishop Malasa.

Ambuye Malasa apempha mabwalo amilandu kuti azipereka chilango choyenera kwa anthu opezeka ndi mlandu wopha komanso kuzembetsa anthu a mtunduwu, koma ati pasakhale lamulo lonyonga.

“Baibulo limaletsa munthu wina aliyense kupha mzake ndipo mpingo umalalika za chikondi. Ngakhale anthu atalakwa ndi anthube basi ndipo zisafike poti diso kulipa diso chifukwa izi zizatipanga tonse kukhala osawona. Ndiye ngati anthu apezeka olakwa titsatire malamulo chifukwa makhothi ndi amene apatsidwa mphamvu zoweruza. Moyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu choncho Mulungu yemweyo ndi amene ali ndi mphamvu yochotsa moyo wa munthu. Akalakwa alangidwe koma chilango choyenelera ndisanene ine chifukwa m’malamulo a dziko lino chinalembedwa,” anatero Ambuye Malasa.

Viewing all 1875 articles
Browse latest View live


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>