Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all 1875 articles
Browse latest View live

Canon Opuma wa Mpingo wa Anglican Atisiya

$
0
0

A ku likulu la chipani cha Anglican mu dayosizi ya Upper Shire mdziko muno akulengeza za imfa ya Canon Absalom Kasiya opuma omwe amwalira lero pa ngozi ya galimoto ku Liwonde.

Maliro akulilira ku nyumba kwao ku Liwonde ndipo padakali pano thupi la malemu Canon Kasiya akulisunga ku nyumba yachisoni ya College of Medicine mu mzinda wa Blantyre. Dongosolo lonse la malirowa ati alilengezabe.

Mzimu wa  Canon Absalom Kasiya opuma uuse mu mtendere wosatha.


Sister Moyo Amwalira

$
0
0

A ku likulu la chipani cha Rosarian Sisters mu dayosizi ya Mzuzu alengeza za imfa ya Sister Maria Rita Moyo.

Sister Moyo anabadwa mu chaka cha 1948 ndipo anachita malumbiro awo oyamba mu chipanichi pa 28 August mu chaka cha 1969.

Pa nthawi ya moyo wao Sister Moyo anagwirapo ntchito ngati mphunzitsi wa ku pulayimale komanso amakonda kuyimba nyimbo za ambuye yesu okhala mu sacrament la Ukaristia.

Thupi la malemu Sister Moyo aliyika lachiwiri pa 28 June 2016.

Mzimu wa  Sister Maria Rita Moyo uuse mu mtendere wosatha.

Alamulidwa Kupereka 5 Sauzande Kamba Kopezeka Akugulitsa Malonda Malo Osayenera

$
0
0

Bwalo la milandu la Midima ku Limbe mu mzinda wa Blantyre lalamula anthu khumi ndi awiri 12 kuti apereke chindaputsa cha ndalama zokwana 5 sauzande aliyense kaamba kopezeka akuchita malonda pa malo oletsedwa mtawuni ya Limbe mu mzinda wa Blantyre.

Wapolisi wotengera milandu ku polisi ya Limbe Sergent Steve Mpira anauza bwaloli kuti anthuwa anawagwira m’misewu ya tawuni ya Limbe lachiwiri.

Sergent Mpira ati apolisi mogwirizana ndi anthu ena ogwira ntchito ku khonsolo ya mzindawu anali pa ntchito  yofuna kuchepesa mchitidwe ogulitsa malonda m’malo olakwika.

Pamenepa Sergent Mpira anapempha oweruza milandu ku bwaloli kuti apereke chilango chokhwima kwa anthuwa potengera kuti milandu ya mtunduwu ikuchuluka mu mzinda wa Blantyre.

Popereka chigamulo, oweruza milandu ku bwaloli, a Benedictus Chitsakamire anati anthu omwe amagulitsa malonda m’malo olakwika amakolezera milandu ing’ono ing’ono monga yopisa anthu m’matumba  kamba koti mbava zimatengerapo mwayi kamba ka mpungwe-pungwe omwe a malondawa amadzetsa m’misewu.

Pamenepa a Chitsakamire anati anthuwa sapereka msonkho zomwe zimabwezera m’mbuyo chitukuko cha mmakhonsolo.

Katundu yemwe anawapeza anthuwa akugulitsa ndi monga zipatso za apozi, masefa a ufa, zakumwa zoziziritsa kukhosi ndi zina zambiri.

 

Papa Ayikiza M’mapemphero Anthui Okhuzidwa ndi Chiwembu Mdziko la Turkey

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Fransisko anapempha mphindi yokhala chete pofuna kuyikiza mmapemphero anthu onse omwe akhudzidwa ndi chiwembu chomwe chachitika  pa bwalo lina la ndege mu mzinda  wa Istanbul mdziko la Turkey.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican Papa anachita izi lero ndi alendo omwe amakayendera likulu la mpingowu omwe amasonkhana nawo lachitatu lililonse.

Papa anati awayikiza mmapemphero anthu onse omwe akhudzidwa pa chiwembuchi ngakhalenso mabanja awo.

Malipoti ati padakali pano chiwerengero cha anthu omwe afa powomberedwa ngakhalenso ndi mabomba omwe anaphulitsidwa pa chiwembuchi ndi chokwana 41 ndipo ena   239 avulala ndipo ati gulu la zauchifwamba la Islamic State ndi lomwe lachita chiwembuchi.

Radio Maria Malawi Yapempha Anthu Akwaniritse Malonjezo awo a Mariatona

$
0
0

Abwenzi a Radio Maria Malawi komanso anthu akufuna kwabwino awapempha kuti akwaniritse lonjezo lawo lothandiza wailesiyi pamene Mariatona wa chaka chino akupita kumapeto.

Wapampando wa Mariatona ya chaka chino a Emmanuel Kaliati anena izi pomwe Mtolankhani wathu amafuna kudziwa za momwe wailesiyi yakonzera dongosolo la mwambo wotsekera mariatonayi omwe uchitikire ku phiri la Michiru ku Chilomoni mu Ark-dayosizi ya Blantyre.

“Pa 2 July tili ku Michiru kukatsekera ulendo womwe tinauyamba pa 7 May ku Balaka. Mwambo ukayamba 6 koloko m’mawa ndi kukwera phiri popemphera kolona. Tikatsekera sikuti zonse zathera pompa ayi. Inu amene muli nako mwina mumadikira mwezi kuti uthe mutha kutumiza kangachepeko ndipo tikukumemezani nonse amene munapanga pledge kuti chonde kwaniritsani malonjezo anu kuti zonse ziyende bwino,” anatero a Kaliati.

Pa Mariatona wa chaka chino, Radio Maria Malawi ikufuna 10 million kwacha kuti imange goloto la Amai Maria, kugula chipangizo cha magetsi cha UPS komanso kubweza ngongole ku bungwe loyang’anira nyumba zoulutsa mawu mdziko muno la MACRA.

Dziko la Turkey Lakhazikitsa Lachinayi Ngati Tsiku Lapadera

$
0
0

Dziko la Turkey lakhazikitsa tsiku la lachinayi pa 30 June, 2016 kukhala lapadera mdzikolo pofuna kukhudza maliro a anthu 42 omwe afa pa chiwembu chomwe chachitikira  pa bwalo la ndege mu mzinda wa Istanbul mdzikolo.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, zigawenga zomwe zachita chiwembuchi zitafika pamalowa zinayamba kuwombera anthuwa ndipo apolisi atalowelera ati zigawengazi zinaphulitsa mabomba omwe zinavala.

Malipoti ati anthu 239 ndi omwe avulala pa chiwembuchi ndipo mwa anthuwa 41 ati avulala modetsa nkhawa.

Padakali pano ati palibe gulu la zauchifwamba lomwe labwera poyera kuti ndi lomwe lachita chiwembuchi koma malipoti osatsimikizika akusonyeza kuti zigawenga za Islamic State zikukhudzidwa ndi chiwembuchi.

Mphunzitsi Amangidwa Kamba Kogwilirira Mwana wa Sukulu

$
0
0

Apolisi m’boma la Ntchisi amanga mphunzitsi wa pa sukulu ina ya pulayimale kamba kogwirira ophunzira wina pa sukulupo wa zaka 16 zakubadwa.

Mneneri wa apolisi m’bomalo Sergent  Gladson M’bumpha watsimikizira Radio Maria Malawi za nkhaniyi ndipo wati Mphunzitsiyo, Justice Zambira wa zaka 24 zakubadwa anagwililira mtsikanayu kanayi pa sukulu ya pulayimale ya Kayoyo.

Sergent M’bumpha wati mphunzitsiyo wakhala akuyitana mtsikanayu kunyumba kwake kuti azikamugwilira ntchito za pakhomo ndipo akamaliza ati ndi pomwe amamugwililira. Mtsikanayu ati anakauza makolo ake za nkhaniyi omwe anakanena ku polisi ndipo malipoti a ku chipatala chaching’ono cha Nthondo atsimikiza za mchitidwewu.

Mphunzitsiyu atafunsidwa ndi apolisi ati anavomera za nkhaniyi ndipo kuti iye amachita izi kamba koti mtsikanayo anamuuza kuti ali ndi zaka zoposera 18.

A Justice Zambira akuyembekezeka kukawonekera ku bwalo la milandu komwe akayankhe  mlandu wogwiririra ndipo iwo amachokera mmudzi mwa Wimbe kwa mfumu yaikulu Wimbe mb’oma la Kasungu.

Zokonzekera Kutsekera Radio Maria Malawi Mariatona Zili Mchimake

$
0
0

Pali chiyembekezo chakuti mwambo wotsekera Radio Maria Mariatona ku phiri la Michiru ku Arkdayosizi ya Blantyre ya mpingo wakatolika loweruka ukhala wopambamba kamba koti zonse zokonzera tsikuli ati zili mchimake.

Mlembi wa bungwe la abwenzi a Radio Maria Malawi ku arkidayosizi ya Blantyre ndi Chikwawa a Elia Jenela alankhula izi ndi Radio Maria Malawi yomwe imafuna kudziwa za dongosolo lomwe lakonzedwa pa tsikuli.

A Jenala  apempha abwezi ndi akhristu akufuna kwabwino kuti azafike ku mwambowu kamba koti kukakhala zochitika zosiyanasiyana kuphatikizapo nsembe ya ukalistiya yothokoza Mulungu.

“Tikupempha abwenzi komanso akhristu onse akufuna kwabwino azafike pa tsikuli ku Chilomoni. Tili ndi chikhulupiliro kuti zonse zizayenda bwino. Ngati pali ma balance onsewo azatha tsikuli ndipo 10 million imeneyi tizaikwanitsa.

Patsikuli accountant adzatiuza ndalama zonse zomwe zatoleredwa kuyambira tsiku limene tinatsegulira Mariatona mpaka pamene tikutsekera. Makwaya amene akakometse mwambowu ndi St. Bernadette ya ku Bangwe parish komanso St. Cecilia ya ku Chilomoni parishi. Mlendo wathu wolemekezeka ndi a Mark Katsonga Phiri,”anatero a Jenala.

Malinga ndi a Jenala, mwambowu ukayamba ndi kukwera phiri njira ya kolona ndipo kenako nsembe ya ukaristia yomwe adzatsogolere ndi bambo Mwinganyama mothandizana ndi a Director a Radio Maria Malawi bambo Joseph Kimu. Mkatikati mwa misayi mukakhala kudalitsa zinthu zosiyanasiyana zomwe anthu akabweretse monga madzi, mchere, kandulo, mafuta ndi zina ndipo pamapeto pa nsembe ya misayi pakakhala perekaniperekani.


Msonkhano Waukulu Wachiri Wa ECM Watha

$
0
0

Msonkhano waukulu wachiwiri wa pachaka wa ma episkopi a mpingo wakatolika mdziko muno watha lero ku likulu la mpingowu mu mzinda wa Lilongwe.

Polankhula ndi Radio Maria Malawi pambuyo pa msonkhanowu mlembi wamkulu wa bungwe la maepiskopi mdziko muno la Episcopal Conference of Malawi (ECM), bambo Henry Saindi, ati pa mfundo zomwe maepiskopiwa akambirana alimbikitsa moyo wa banja la chikhristu mowunikiridwa ndi kalata ya apapa yotchedwa “Amoris Lactitia” yomwe inatulutsidwa pambuyo pa misonkhano iwiri ya maepiskopi ya sinodi ya mabanja.

Bambo Saindi ati maepiskopiwa apempha mabungwe akufuna kwabwino kuti athandize dziko lino ndi chakudya kaamba koti madera ambiri mdziko muno akukumana ndi vuto la njala.

 Mwa zina ku msonkhanowu maepiskopiwa alandira malipoti kuchokera ku mabungwe akuluakulu a mpingowu. Msonkhanowu omwe unali wa masiku anayi  unasonkhanitsa ma Episkopi onse a mdziko muno kuphatikizapo nthumwi ya apapa mmaiko a Malawi ndi Zambia Arch-bishop Julio Murat.

Woyimira Anthu pa Milandu Wapezeka Atafa Mdziko la Kenya

$
0
0

Loya wina yemwe amayimilira  munthu wina pamlandu woti apolisi m`dziko la Kenyaakumachitira nkhanza  anthu m`dzikolo wapezeka  atafa munzinda wa Nairobi m`dzikolo.

Loyayu, Willie Kimani wa zaka 32, pamodzi ndi dalaivala yemwe  amamuyendetsa pathawiyo anasowa sabata yapitayo atangotuluka mu  bwalo la milandu. Thupi la mkuluyu ati alipeza litakulungidwa  m`phepete mwa mtsinje wina omwe uli pamtunda  wa makilomita 70 kumwera chakum`mawa kwa  mzinda wa Nairobi.

Bungwe la Malamulo m`dzikolo lati kuphedwa kwa loyayu ndi chinthu chomvetsa chisoni kwambiri pantchito yoteteza malamulo a dzikolo.

Apolisi mdziko la Kenya akhala akudzudzulidwa kuti amachitira nkhanza mzika zadzikolo komanso kugwirizana ndi mbava  polimbikitsa umbanda ndi umbava.

Pakadali pano mkulu wa apolisi mdzikolo walamula kuti apolisi atatu amene akuganiziridwa kuti ndi amene achita izi amangidwe.

Ma Episkopi Mdziko la South Africa Adzudzula Ziwawa Mdzikolo

$
0
0

Maepiskopi a mpingo wakatolika mdziko la South Africa adzudzula  mchitidwe wa ziwawa omwe ukuchitika mdzikolo potsatira chisankho cha makhansala chomwe chikuyembekezeka kuchitika mwezi wa mawa.

Malinga ndi uthenga omwe bungwe la maepiskopi latulutsa omwe wasainidwa ndi wapampando wa chilungamo ndi mtendere mu bungweli, Ambuye Abel Gabuza wapempha mamembala onse a zipani za ndale kuti akakhale nawo pa mwambo wa mapemphero opemphelera mtendere omwe uchitike lachitatu sabata la mawa.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican, Ambuye Gabuza ati mtendere mdziko la South Africa sukuyenera kutengedwa ngati chinthu chapafupi ndipo mzika ngakhalenso zipani za ndale za mdzikolo zikuyenera kukhala ndi udindo  wodzetsa mtendere makamaka pa nthawi ya chisankho.

Ambuye Gabuza adzudzulanso zipani za ndale zomwe zimagwiritsa ntchito achinyamata kuchita ziwawa ndipo apempha achinyamatawa kuti asalole kugwiritsidwa ntchito ndi zipanizi.

Pomaliza kalatayi yapempha mzika zoyenelera za dzikoli kuti zikaponye nawo voti pa chisankhochi ndi kukasankha atsogoleri oti awayimilire moyenera.

Chitukuko Chingapite Patsogolo Ngati Adindo ndi Mzika Akulumikizana

$
0
0

Kulumikizana pa nkhani za chitukuko cha m’madera pakati pa adindo komanso mzika ati ndi njira yokhayo yomwe ingapititse patsogolo chitukuko cha dziko lino.

Wachiwiri kwa mfumu ya mzinda wa Blantyre, a Wild Ndipo alankhula izi mu mzindawu ngati mlendo wolemekezeka pa msonkhano owunika momwe chitukuko cha maboma aang’ono chikuyendera pomwe mabungwe ndi anthu okhudzidwa pachitukuko amachita kawuniwuni pa momwe ntchito zachitukuko zikuyendera.

Iwo ati kusalumikizana pa nkhani zachitukuko cha m’madera sikoyenera, ichi ndi chifukwa chake nthumwi ku msonkhanowu zapeza kuti anthu ambiri akulephera kusamala chitukuko chomwe amalandira kamba ka vutoli.

Msonkhanowu omwe unakonzedwa ndi mabungwe a State of the Union, Eye for Development, Malawi Economic Justice Network {MEJN} komanso Citizen Alliance unasonkhanitsa makhansala, ma bwanamkubwa a mmaboma ena, akuluakulu a ku unduna wa maboma ang’onoang’ono komanso mabungwe.

Katsonga Wapempha Akhristu Azithandiza Radio Maria Malawi

$
0
0

Akhristu a mpingo wakatolika m`dziko muno awapempha adzitenga  gawo lalikulu pothandiza Radio Maria Malawi.

Yemwe anali mlendo wolemekezeka pa mwambo wotsekera ntchito yotolera thandizo la wailesiyi lotchedwa Mariatona, Wolemekezeka a Mark Katsonga Phiri anena izi ku Michiru Shrine mu arkidayosizi ya Blantyre.

Iwo ati Radio Maria Malawi pomwe ikugwira ntchito yofalitsa uthenga wa Mulungu, ikukumananso ndi mavuto a nkhaninkhani zomwe ati zikufunika kuti akhristu onse a mpingowu azichita msonkhansonkha ngati umenewu.

Pa mwambowu, Radio Maria Malawi yapereka certificate kwa m’modzi mwa abwenzi a wailesiyi mayi Veronica Sembereka kaamba kotolera ndalama zambiri pa mariatona wa chaka chinoyu.

Ndipo m’mawu ake Director wa Radio Maria Malawi bambo JosephKimu ati zomwe akhristu achita chaka chino ndi chitsimikizo choti anthu ambiri amayikonda wailesiyi.

Yemwe anali wolemekezeka pa mwambowu a Mark Katsonga Phiri apereka ndalama yokwana 1 million Kwacha ndipo chaka chino Radio Maria Malawi yakwanitsa kupeza mulingo wa ndalama zomwe inayerekeza kuti ipeze wa 10 million kwacha.

Amuna Awiri Amangidwa Kamba Kobera Mayeso a MSCE

$
0
0

Amuna awiri ali m’manja mwa apolisi atapezeka akubera mayeso a fomu 4 m’boma la Balaka.

M’modzi mwa amunawa a Joseph Makiyi omwe amagwira ntchito ku Prison Fellowship anatenga tchuthi kuntchito kwawo kuti akukalemba mayeso a MSCE ku Balaka Islamic Institute ndipo m’malo mwake anapempha mzawo a Charles Kumwenda omwe amagwira ntchito  ngati wa zaumoyo pa chipatala cha Kapire m’bomalo kuti akawalembere mayesowo.

Masana a tsiku la pa 30 June pamene ophunzira amalemba mayeso a Human Geography ndi pamene mkuluyi anagwidwa ndi m’modzi mwa ogwira ntchito ku MANEB yemwe anafika kudzayang’nira m’mene mayeso amayendera pa malopa.

Pakadali pano amuna awiriwa avomera mlanduwu ndipo akuyembekezeka kukawonekera ku bwalo la milandu ndikukayankha mulandu wobera mayeso.

Amunawa amachokera m’mudzi mwa Lupanga mfumu yaikulu Nsamala m’boma la Balaka.

Alamulidwa Kukakhala ku Ndende Zaka 10 Kamba Kopereka Mimba kwa Mtsikana Wachichepere

$
0
0

Mwamuna wina wa zaka 18 zakubadwa amulamula kuti akakhale kundende ndikukagwira ntchito ya kalavula gaga kwa zaka khumi (10) kamba kopereka mimba kwa msungwana wa zaka 15 m’boma la Mwanza.

Mneneri wa apolisi m’bomali, a Edwin Kaunda, auza atolankhani a MANA kuti bwalo lamilanduli lachinayi linapeza a Allan Wizzard wolakwa pa mlandu wopereka mimba kwa mwana wang’ono m’mudzi mwa Chikolosa m’bomalo.

Malinga ndi a Kaunda, a Wizzard omwe amakana mlandu wogwilirira msungwanayu anachita chibwenzi ndi msungwanayu pa 5 May chaka chino ndipo ati tsiku lina msungwanayu anasowa pakhomo pa makolo ake zimene zinachititsa kuti makolowo akadandaule kwa a mfumu omwe analamula anthu kuti ayambe kumusaka ndipo anakampeza kunyumba kwa a Wizzard omwe amati msungwanayo ndi mkazi wawo.

A Kaunda ati msungwanayu anamutengera pa chipatala cha boma cha Mwanza komwe anatsimikiza kuti ali ndi mimba ya mwezi umodzi.

A Wizzard amachokera m’mudzi mwa Minjale mfumu yaikulu govati m’boma lomwelo la Mwanza.


Papa Wapepesa Anthu Amene Akhuzidwa Ndi Chiwembu Mdziko la Bangladesh

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Fransisko wapereka uthenga wa chipepeso kwa anthu omwe akhudzidwa ndi chiwembu chomwe chaphetsa anthu makumi awiri mu mzinda wa Dhaka mdziko la Bangladesh.

Malinga ndi kalata yochokera ku likulu la mpingowu yomwe yasayinidwa ndi mlembi wake Cardinal Pietro Parolin, Papa ndi wokhudzidwa ndi chiwembuchi ndipo wati mchitidwe wa mtunduwu ndi tchimo kwa Mulungu ngakhalenso pa umunthu.

Malipoti a wailesi ya Vatican ati Papa walonjeza kuti awayikiza m’mapemphero achibale onse a anthu omwe aphedwa komanso anthu omwe avulala pa chiwembuchi.

Padakali pano boma la dziko la Bangladesh lakhazikitsa masiku awiri okhudza maliro a anthuwa ndipo malipoti a wailesi ya BBC ati gulu lomwe lachita chiwembuchi si la zigawenga za Islamic Statekoma ndi gulu lina la za uchifwamba lomwe analithamangitsa mdzikolo zaka khumi zapitazo.

Mutharika Wati Atukula Mzinda wa Zomba

$
0
0

President wa dziko lino Professor Arthur Peter Mutharika wati boma lake likhazikitsa zitukuko zosiyanasiyana mu mzinda wa Zomba ndi cholinga choti mzindawu udzifanafana ndi mizinda ina ya mdziko muno.Mutharika amayankhula izi lachisanu atayendera misewu yatsopano yomwe  ikumangidwa mu mzindawu.

Iye wati mzinda wa Zomba uli ndi mbiri ya dziko lino motero ukuyenera kukhala ndi zinthu za makono.

“Ndikufunitsitsa kuti mzindawu upite patsogolo ndi program imeneyi ya misewu ndi maprogram ena. Tilinso ndi mapulani oti timange bwalo la masero a mpira wa miyendo la tsopano(stadium)paja pamene pali community ground. Tilinso ndi plan yoti timange Shopping Mall pafupi ndi Mulunguzi Centre,”anatero a Mutharika.

Iye wati boma lake likuchitanso ndondomeko yokonza magetsi onse mu misewu yonse ya mu mzindawu.

Mutharika anapezelaponso mwayi pa msonkhanowu kutsutsa zomwe zimamveka kuti pulezidentiyu pa msonkhano wake wachitukuko mboma la mulanje anati anthu azidya mbewa komanso zitete pa nthawi ino anthu mdziko muno akuvutika ndi mliri wa njala.

“Sabata yatha ndili ku Mulanje ndinanena kuti anthu ambiri amadalira chimanga chokha zomwe sizabwino. Chomcho ndinati anthu azidyanso mbatata, chinangwa komanso zicheche ena amati zilazi pachingerezi timati yams, sinnanene kuti zitete,” anatero Mutharika.

Boma la Mutharika latsimikizira anthu kuti likufuna kuthana ndi misewu yonse ya fumbi yomwe ili mmizinda yonse ya mdziko muno ndi kuyikamo phula.

Papa Francisco wati Ntchito za Migodi Zikomere Anthu Okhala Moyandikana ndi Malowa

$
0
0

Mtsogoleri wampingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco,wapempha mayiko kuti adziwonetsetsa kuti ntchito za migodi zomwe zikuchitika mmayiko awo zikuchitika mokomera anthu  onse maka oyandikana ndi malo omwe migodiyo ikuchitikira.

Papa Francisco,wapereka pempholi muuthenga wake omwe atumizira nthumwi zomwe zili kumsonkhano okhudza chitukuko cha migodi ndi zotsatira zake,omwe ukuchitikira ku likulu la mpingowu ku Vatican.

Cholinga cha msonkhanowo omwe wakonzedwa ndi nthambi yowona za chilungamo ndi mtendere kulikulu lampingowu ndi chofuna kuwunika madandaulo omwe anthu okhala mmadera oyandikana ndi migodi amakumana nawo nthawi zonse.

Mmawu ake mkulu owona zamabungwe a mumpingowu kulikululo Kadino Peter Turkson, wati nthawi zambiri ntchito zamigodi zimabweretsa mavuto monga kuwonongeka kwa chilengedwe ndipo ndi pofunika kuti mayiko aziganizira mbali zonse akafuna kuyambitsa ntchitozi.

Atsogoleri a Zipani Zotsutsa Sapikisana Nawo pa Chisankho cha Pulezidenti Mdziko la Burundi

$
0
0

Pamene chisankho cha pulezidenti mdziko la Burundi chikuyembekezeka kuchitika lachiwiri, mtsogoleri wa dzikolo Pierre Nkurunziza ati akuyembekezeka kupambana pa chisankhochi zomwe zichititse kuti akhale pa ulamuliro wa dziko logawikana.

Malinga ndi malipoti a NEWS24 zipani zotsutsa ndi magulu omwe si aboma akana kutenga nawo mbali pachisankhocho ndipo ati zomwe achita a Nkurunziza ndi zotsutsana ndi malamulo komanso kuphwanya mgwirizano wa mtendere womwe unakhazikitsidwa mdzikolo mu chaka cha 2006 pambuyo pa nkhondo ya pachiweniweni yomwe inachitika mdzikolo.

Chisankhocho chomwe otsutsa akana kupikisana nawo ati kamba koti ndi chobera, Pulezidenti Nkuruzinza alibe wopikisana naye.

Mmodzi mwa akuluakulu otsutsa mdzikolo wati boma la dzikolo ladzipatula kuti lichite chisankhocho litakanika kumvana pa zokambirana zodzetsa mtendere zomwe amachititsa mtsogoleri wa dziko la Uganda a Yoweri Museveni.

Ambuye Musikuwa Apempha Asisiteri Akhale Odzipereka pa Utumiki

$
0
0

Episkopi wa dayosizi ya Chikwawa ya mpingo wakatolika Ambuye Peter Musikuwa wapempha asisteri kuti azikhala odzipereka pa utumiki wao.

Ambuye Musikuwa alankhula izi pa mwambo wa malumbiro a ku nthawi zonse a asisteri a chipani cha Divine Providence omwe unachitikira ku parishi ya Fatima mu dayosiziyi.

Iwo ati atumikiwa akuyenera kuzindikira kuti satana atha kubwera pakati pawo ndi kuwalepheretsa utumiki wao.

“Satana amabwera mwanjira zosiyanasiyana natiyesa pa malumbiro athu aja koma ngati tilimbika mchikhulupiliro, tikazindikiranso kuti chiyitanidwe ndi chikondi cha Mulungu tizalimbika mu utumiki wathu komanso chiitanidwe,” anatero Ambuye Musikuwa.

Ambuye Musikuwa anati, “Tikuyeneranso kudziwa kuti Mulungu anatiyitana kuti tikhale zida zake zoti azigwiritse ntchito yopulumutsira anthu. Munthu woyitanidwa ndi chida cha Mulungu. Choncho tikuyenera kukhala okonzeka nthawi zonse kuti Mulungu atigwiritse ntchito. Tikuyenera kukhala ndi mtima ngati wa Simoni woti chifukwa cha mawu anu tisunthira kozamako.”

Viewing all 1875 articles
Browse latest View live


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>