Anthu omwe anamangidwa kaamba kowaganizira kuti ali mgulu la Boko Haram ati akufa kundende kaamba ka matenda osiyanasiyana monga onyetchera.
Malinga ndi lipoti lomwe bungwe la Amnersty International latulutsa lasonyeza kuti m`dende za m`dzikolo muli anthuwa okwana zana limodzi ndipo anthu asanu ndi atatu ndiwo akumafa pa mwenzi m`dzikolo.
Malinga ndi wailesi ya BBC, mndende za zadzikolo muli mavuto ankhaninkhani ngakhale dzikolo likukana zomwe lipoti la bungweri lomenyera ufuluri latulutsa.
Gulu la Boko Haram lakhala likuchita zamtopola zosiyanasiyana pogwiritsa ntchito mabomba a tinkenawo m`dzikolo ndipo anthu oposa mazana asanu ndiwo anafa afa kaamba ka dziwembudzi.
Dziko la Cameroon linachita malire ndi dziko la Nigeria komwe la Boko Haram likufuna kukhazikitsa ulamuliro wachisilamu.