Chipatala cha Praises chati chakonza dongosolo lopeleka thandizo lina la zachipatala mwaulele pofuna kuthandiza anthu a m’dera lomwe kuli chipatalachi.
Mkulu wa chipatalachi Dr. Nelson Munthali wanena izi pokondwerera kuti chipatalachi chakwanitsa zaka khumi ndi zisanu (15) chikuthandiza anthu a m’dera la Machinjiri mu m’dzinda wa Blantyre.
“Tinatsegula chipatalachi pa 1 august 2001ndiye tawona kuti pamene tafikapa anthu a kuno ku machinjiri akhala akutipanga support mu zinthu zambiri mpaka chipatalachi chakula ndiye tawona kuti tiwabwerenso anthu a dera lino chifukwa cha ubwino wawo. Pachifukwa chimenechi kuyambira pa 1 august anthu onse ochokera kuno kuno kumachinjiri samalipila ndalama yokawonana ndi a dotolo komanso pa ndalama ya treatment yawo tizichotsako 20 kwacha pa 100 kwacha iliyonse. Komanso anthu amene azichokera kutalibe tiziwabwezera transport,” anatero a Munthali.
Iwo anati apitirizane kuthandiza anthu kudzera mu ntchito za chipatala pozindikira kuti munthu amene amakhala mtauni amayenera akhale wathanzi kuti athe kugwira ntchito yake moyenera.