Katswiri pankhani ya zisudzo m`dziko muno Michael Usi, wapempha mtsogoleri wadziko lino ProfessorArthurPeter Mutharika asasainile lamulo latsopano lokhudza malo kamba koti a Malawi ambiri kuphatikizapo mafumu sanafunsidwe maganizo.
A Usi anena izi poyakhura ndi Radio Maria Malawi munzinda wa Blantyre.
Iwo ati boma komanso nyumba ya malamulo akuyenera kuzindikiritsa anthu magawo omwe ali mu lamulori .
Nyumba ya malamulo yavomereza lamulo latsopano lokhudza malo posachedwapa lomwe kwambiri likupereka mphamvu zambiri kwa nduna ya zamalo kuti izitha kupanga chiganizo pa malo omwe kale anali m`manja mwa mafumu.