Bungwe la zachitukuko mu mpingo wakatolika la Catholic Development Commission in Malawi (CADECOM)lapempha atolankhani mdziko muno kuti atenge gawo lalikulu pofalitsa mauthenga a ndondomeko zosiyanasiyana zomwe boma likukhazikitsa.
Mkulu woyang’anira za chitukuko ku bungweli a Yusuf Mkungula alankhula izi m’boma la Salima pambuyo pa maphunziro a masiku awiri omwe bungweli linakonzera atolankhani a nyumba zofalitsa mawu mdziko muno.
Iwo ati pali ndondomeko monga kusintha kwa nyengo komanso ngozi zogwa mwadzidzidzi zomwe zinakhazikitsidwa kale zomwe zikusowa ukadaulo wa atolankhani kuti ndondomekozi ziyambe kugwira ntchito yake komanso zikhazikitsidwe.
“Ndondomeko zina zinakhazikitsidwa monga ya kusintha kwa nyengo ndi ya ngozi zogwa mwadzidzidzi koma zina sizinakhazikitsidwe monga ya za ulimi ndi ya ufulu wa chakudya. Tikufuna atolankhani atithandize kupititsa patsogolo ntchito yowanenera anthu akumidzi kuti ndondomekozi zikhazikitsidwe ndipo ziyambe kugwira ntchito. Pakadali pano ntchito imene tikugwira sizikuthandiza kwenikweni chifukwa tikugwira ntchitozi popanda chida chotiunikira pazimene tikuyenera kutsata kuti tipititse miyoyo ya anthu a kumudzi,” anatero a Mkungula.
Poyankhulapo mmodzi mwa anthu omwe anachititsa nawo maphunzirowa a Alfred Kambwiri ati ndondomeko ya ulimi ndi yofunika kwambiri kamba koti dziko la Malawi limadalira kwambiri pa ulimi.
Iwo ati pali chiyembekezo kuti chikamatha chaka chino ndondomekoyi ikhala itakhazikitsidwa choncho apempha atolankhani kuti agwire bwino ntchito yawo kuti a Malawi akhale ndi masomphenya pa nkhani zamalimidwe mu zaka zikubwerazi.
Mmawu ake mmodzi mwa atolankhani amene anachita nawo maphunzirowa a Precious Msosa ayamikira bungwe la Cadecom kamba ka maphunzirowa ndipo ati athandiza atolankhani azilemba nkhani mokomera anthu pofuna kuti ndondomekozi ziziyenda bwino zikakhazikitsidwa.
“Zitithandiza kulemba nkhani zothandiza adindo kuti akhazikitse ndondomekozi ndi cholinga choti zithandize anthu akumidzi kuti ufulu wawo wokhala ndi chakudya ukwaniritsidwe,” anatero Msosa.
Bungwe la CADECOM ligwira ntchitoyi kwa zaka zitatu ndipo ipindulira mabanja 1250 ndipo bungweli likugwira ntchitoyi ndi ndalama zochokera ku Department For International Development (DFID)