Bungwe lomenyera ufulu wa anthu a chi alubino m’dziko muno laAssociation of People with Albinism(APAM) lati ngakhale boma likutsindika kuti lithana ndi mchitidwe wosembetsa ndi kupha anthu a achialubino bungweli silikuona kusintha kwina kulikonse pa chitetedzo cha anthu-wa m’dziko muno.
Yemwe akutsogolera bungweli aOvaston Kondowe anena izi pothilira ndemanga pa zimene nduna ya za m’dziko ndi apolisi, a Jappie Muhango yanena itakayendera mayi Lucia Kayinga a mtundu wa chi alubino omwe agonekedwa pa chipatala cha Mzuzu anthu ena atawadula manja.
A Kondowe ati boma likuyenera kudzipereka kotheratu pa chitetezo cha anthu-wa m’dziko muno, kupanda kutero ndiye kuti anthu a mtundu wa chi alubino m’dziko muno apitiriza kukhala pa chiopsezo chachikulu kwambiri.
“Sitikukhutitsidwa chifukwa tinapempha kuti kumene kulibe chitetezo apolisi aziyendako. Mabungwe osiyanasiyana tikanakonda kuti apolisi akhwimitse chitetezo; azipanga patrol, ma road block komanso azipezeka malo akumidzi komwe kuli anthuwa. Apolisi ndi ambiri. Boma limakwanitsa kutumiza apolisi mmasukulu onse mdziko muno pa nthawi ya mayeso choncho izinso nzotheka,” anatero a Kondowe.
Iwo apempha boma kuti lipereke zida zokwanira kwa achitetezowa ndipo ati izi zitachitika kwa chaka chimodzi atha kudzanena kuti boma layesetsa.