Mtsogoleri wakale wa dziko la France a Nicholus Sarkozy wadzudzula boma la dzikolo kamba kolephera kupereka chitetezo chokwanira mdzikolo.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC mtsogoleri wakaleyu walankhula izi potsatira ziwembu zosiyanasiyana zomwe zakhala zikuchitika mdzikolo pomwenso sabata yatha anthu makumi asanu ndi atatu aphedwa galimoto la mtundu wa lore yomwe anakwera litachitidwa chiwembu.
Malipoti ati a Sarkozy apempha boma la dzikolo kuti lithamangitse anthu onse obwera mdzikolo omwe akukolezera za uchifwamba.