Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Ambuye Warduni Ati ndi Okhudzidwa ndi Mavuto Omwe Anthu Othawa Kwao Akukumana Nawo

$
0
0

Episkopi wa mpingo wakatolika mdziko la Iraq, Ambuye Shlemon Warduni wati ndi okhudzidwa ndi mavuto omwe anthu othawa kwao akukumana nawo m’malo omwe akukhala.

Malinga ndi malipoti a Catholic Culture, Episkopiyu wati mavuto omwe anthuwa akukumana nawo monga kusowa kwa chakudya, akusowa thandizo kuchokera kwa anthu akufuna kwabwino. Malipoti ati atsogoleri a maiko ngakhalenso mabungwe akhala akulankhulapo za nkhaniyi koma chomvetsa chisoni ndi chakuti sakuchitapo kanthu.

Ambuye Warduni ati apitiriza kuwayikiza mmapemphero anthuwa pozindikira kuti pa nthawi yomwe anali mdziko la kwao anali ndi nyumba ngakhalenso ntchito koma padakali pano alibe chilichonse.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>